Dowload PDF (direct link)

Listen/Download MP3

Qur’an yolemekezeka ikutifotokozera kuti Mneneri Ibrahim adalamulidwa ndi Allah kuti alengeze ndi kuwawuza anthu za Hajj, omwe mu lamulo la Mulungu adzavomera kuyitana kwa Mwini lamulo ndipo adzakonza maulendo kuchokera madera osiyanasiyana kupita ku Makkah pogwiritsa ntchito njira za kayendedwe zosiyanasiyana. Ndipo kumeneko azikapanga miyambo ya Hajj, kupemphera mapemphero, kudyetsa osauka, ndi kupeleka chopeleka. Qur’an yolemekezeka ikufotokoza motere:

“Ndipo kumbukirani pomwe tidamnkhazikitsa Ibrahim ndi kumulondolera pamalo pa nyumba yopatulikayo tidamuwuza kuti:” Usandiphatikize ndi chilichonse: Ndipo Iyeretse nyumba yanga chifukwa cha amene akuyizungulira ndikumakhala pompo (pochita mapemphero awo),  ndi omwe amawerama pogwetsa nkhope zawo pansi. Ndipo (Tidamuwuza): Lengeza kwa anthu za Hajj! Akudzera ena oyenda ndi mapazi, ndipo ena ali pamwamba pa pachiweto chowonda chifukwa cha masautso a paulendo; adza kuchokera kunjira zamtalimtali. Kuti adzawone zabwino zawo, ndikuti aculukitse kutchula dzina la Mulungu m’masiku odziwika (ubwino wake), kupyolera mzimene wawapatsa monga ziweto za miyendo inayi. Ndipo idyani ina mwa nyamayo ndi kumdyetsa wovutika, osauka. Kenako adziyeretse kuzitakataka zawo, ndipo akwaniritse malonjezo awo ndikuzungulira nyumba yakale.” (22:26-29).

Chipembedzo cha Allah chomwe chinabvumbulutsidwa kudzera mwa Ibrahim chinafalikira nthawi imeneyo  mumzinda wa Makkah ndi madera onse ozungulira. Anthu omwe anatsatira chipembedzo cholungamachi anali kugwadira Mulungu m’modzi yekha ndipo sanamuphatikize iye ndi china chilichonse. Iwo anali kupanga ndi kukwaniritsa malamulo onse a Hajj motsogoleredwa ndi chibvumbulutso chomwe chinabvumbulutsidwa kwa Mneneri Ibrahim mtendere ukhale pa iye. Koma chifukwa cha kudutsa nthawi yayitali komanso chifukwa cha kusintha kwa mibado ndi miyambo, malamulo a chipembedzo chomwe chinabvumbulutsidwa kwa Ibrahim anasakanikirana ndi miyambo yachabechabe ya anthu opembedza mafano. Ndipo izi zinapitilirabe kufikira panthawi yomwe Mtumiki wathu Muhammad madalitso ndi mtendere zikhale kwa iye anabadwa, fuko lirilonse la ma Arab linali ndi mafano omwe anali kusemedwa kuchokera ku matabwa, miyala ndi zinthu zina. Ndipo zokudzana ndi kumugwadira Mulungu, Mwini chilamulo komanso mphamvu zonse inali mfundo yopanda pake ndipo anthu sanalabade za kufunika kwa kumugwadira Mulungu m’modzi.

Machitidwe a mwambo wa Hajj anali kupitilira ngakhale kuti unali utasinthidwa posakanikirana ndi miyambo ya anthu ogwadira mafano. Izi zinali choncho chifukwa cha kufunika kwa miyamboyi makamaka pa malonda. Nyumba ya Ka’bah inasandulika chimake chopembedzerapo mafano ndipo inazunguliridwa ndi mafano osiyanasiyana malingana ndi mitundu ya Ma Arab. Ma Arab anali kuchoka madera osiyanasiyana chaka chilichonse  ndi cholinga chofuna kukapanga miyambo ya Hajj komanso kukapeleka nsembe zosiyanasiyana ku mafano awo omwe anali ponseponse mnyumba ya Ka’bah. Pambuyo pa kubwera kwa chipembedzo cha chisilamu, miyambo ndi malamulo a Hajj omwe amachitika lero lino anakhazikitsidwa mchaka cha chisanu ndi chiwiri (7) pambuyo pa msamuko wa Mtumiki (sa) kuchoka ku Makkah kupita ku Madina. Panthawi imene mzinda wa Makkah unatsegulidwa mwatsopano ndi kukhala mchilamulo cha chipembedzo cha chisilamu mchaka chachiwiri, Mtumiki wathu Muhammad salla Allah alaih wasallam anayima mnyumba ya Ka’bah ndipo anayiyeretsa nyumba ya Ka’bah ku mafano omwe anali mkati mwake. Iye anayamba ndi kuphwanya mafano omwe anali mnyumbayi uku akulankhula mokweza mawu awa: “Chowonadi chadza ndi bodza lapita ndi kuthetsedwa”. Kenaka iye analamula kuti mafano onse aphwanyidwe ndi kuswedwa. Umu ndi m’mene nyumba yolemekezeka ya Ka’bah inayeretsedwera kuchoka ku mafano ndikukhalanso nyumba yomupembedzeramo Mulungu m’modzi yekha kudzera m’mapemphero komanso popanga miyambo ya Hajj.

Kukakamizidwa Kwake

Hajj ndi mchitidwe wa miyambo ya kapembedzedwe ka pagulu omwe umachitika chaka chilichonse, omwe Asilamu amene ali ndi zowayenereza ndipo akhoza kukwanitsa kupanga ulendo opita ku ulendo omwe anthu amaukonza kuchokera mbali zonse za dziko lapansi kupita ku Makkah amapita, gwero komanso tsinde la chipembedzo chomwe chinabvumbulutsidwa kwa Mneneri wathu Muhammad mtendere ndi madalitso zikhale pa Iye.

Umenewu ndi mchitidwe owonekera poyera wa kupembedza omwe umasonyeza mgwirizano ndi kusasiyana kwa Asilamu kuchokera kumbali zonse za dziko lapansi ndi cholinga chimodzi chomwe ndi kupangira limodzi miyambo ndi zichitochito zomwe zimachitika ndi cholinga chofuna kupeza chisoni, chifundo komanso mtendere ndi chisangalalo cha Allah Mbuye wa zolengedwa zonse.

Ku Makkah anthu onse omwe amakapanga Hajj, amayima mofanana, olemera kapena osauka, Atsogoleri ndi olamuliridwa, Ophunzira ndi osaphunzira, akuda ndi oyera. Kumeneko onse amavala zovala zoyera ndipo onse amakhala mozungulirana zomwe zimasonyeza kugwirizana komanso umodzi omwe iwo ali nawo mwa Allah Mwini wa zolengedwa zonse.

Kumeneko zolinga zawo zimakhala zofanana ndipo zotsatira zake zimawalimbikitsa ndi kuwapatsa iwo mphamvu zogwilira ntchito limodzi pofuna kukwaniritsa ubwino mokomera munthu wina aliyense.

Hajj ndi yokakamizidwa kwa Msilamu wina aliyense otha nsinkhu yemwe ali ndi zomuyenereza ndipo akhoza kukwanitsa kupanga ulendo opita ku Makkah mu thanzi ndi chuma.

Hajj siyokakamizidwa kwa anthu ena osakhala Asilamu, Ana komanso amisala omwe nzeru zawo sizikugwira ntchito malingana ndi momwe ananenera Mtumiki wathu Muhammad mtendere ndi madalitso zikhale pa Iye yemwe ananena kuti:

Cholembera (Chomwe chimalemba zochita za anthu padikira chigamulo chochokera kwa mwini lamulo) sichigwira ntchito kwa anthu atatu: Munthu amene akugona kufikira atadzuka, mwana mpakana atatha msinkhu, komanso wamisala mpaka atachila ku misala yakeyo”.

Kukhala ndi zokuyenereza pa chuma komwe kumampanga munthu kuti Hajj ikhale yokakamizidwa kwa iye, kumatanthauza kukhala ndi zokuyenereza zotha kupanga ulendo opita ku Makkah kukapanga miyambo ya Hajj komanso kukhala ndi chithandizo chokwanira cholisiyira banja,  azibale komanso onse omwe umawayang’anira ndikuwathandiza. Lamulo limeneli silikuwakhudza anthu omwe ndi mzika za mzinda  wa Makkah chifukwa choti kumeneko ndi kwawo ndiponso chifukwa choti nyumba ya Ka’bah ali nayo pafupi ndipo zokonzekera zawo zimakhala zochepa.

Ngati munthu atapanga Hajj ali mwana zimenezi sizingamuteteze iye kuti asadzakhale okakamizidwa kupanga Hajj atakula. Ngati ana atapitila limodzi ndi makolo awo ku Hajj ndipo sangakwanitse kupanga miyambo ya Hajj pa iwo okha, makolo kapena ayang’aniri awo akhoza kuwapangira miyambo imeneyi.

Munthu amene angamwalire asanapange Hajj amakhululukidwa ngati azibale ake atamupangira iye mudzina lake. Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti: “Fulumirani kupanga Hajj yanu chifukwa palibe mwa inu amene akudziwa zimene zingamuchitikire mtsogolo “. Komanso munthu amene wakalamba kwambiri kapena ali ndi matenda osachiritsika, akhoza kupeza munthu oti akamupangire Hajj. Koma tiyenera kudziwa kuti kumupangira munthu wina Hajj sikoloredwa kwamunthu amene akumupangira nzake pokhapokha ngati munthuyo  anadzikwaniritsira kale yekha lamulori.

Kukakamizidwa kwa Hajj kunanenedwa ndi Qur’an yolemekezeka motere:

“Ndithudi Mulungu walamula anthu kuti akachite Hajj mnyumbayo, amene angathe kukonza ulendo wonka kumeneko” (3:96-97) .

Komanso malingana ndi Hadith’ ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam, Abdullah Ibn Umar radhia Allah anhu ananena kuti anamumva Mtumiki salla Allah alaih wasallam akunena kuti:

“Chisilamu chamangidwa ndi nsanamila zisanu: Kuchitira umboni kuti palibe wina oyenera kupembedzedwa mwachowonadi koma Allah ndikuti Muhammad ndi kapolo ndi mtumiki wake, Kuyimika mapemphero, Kupeleka chopeleka, Kukachita Hajj ndi kusala m’mwezi wa Ramadhan”. Inarandiridwa ndi Bukhar ndi Muslim”.

Komanso Nasaai analandira Hadith’ yomwe ikunena ku Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti: “Hajj ndi Umrah (Hajj yaying’ono) ndi Jihad (Kumenyera mu njira ya Allah) kwa okalamba, ofowoka ndi akazi”.

Komanso Abu Hurairah analandira Hadith’ yomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti: “Yemwe angapange Hajj popanda kuwononga popanga choyipa chilichonse, adzabwelera kwawo pambuyo pa kumaliza kwake Hajj opanda tchimo lililonse ngati mwana obadwa kumene”. Inalandiridwa ndi Bukhar ndi Muslim”.

Hajj ndi yokakamizidwa kamodzi pamoyo wamunthu, koma kwa amene angapange powonjezera pamenepa amapanga choncho chifukwa cha kudzipeleka komanso kufuna kwake.

Nkhani inachokera kwa Abdulla Ibn Abbas kuti Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena tsiku lina mu kulankhula kwake Iye ananena kuti: “O inu anthu! Hajj ndi yokakamizidwa kwa inu choncho chitani (Hajj), m’modzi mwa Asilamu yemwe dzina lake ndi Al-Aqrah Ibn habis anafunsa: Mtumiki wa Allah! Chaka chilichonse? Mtumiki anati: “Ngati nditatero, ndiye kuti ikhala chikakamizo chomwe chili pansi pa mphamvu zanu. Hajj iyenera kuchitika kamodzi pamoyo ndipo amene angapange koposera kamodzi adzakhala kuti akupanga izi mwakufuna kwake”.

Malingana ndi Hadith’ iri pamwambayi, Hajj ndi yokakamizidwa kamodzi pamoyo wamunthu. Izi zidzakhala zowathandiza kwambiri anthu omwe ntchito zawo ndi zofunikira kwambiri ndipo palibe amene angayime m’malo mwawo pogwira ntchito zimenezo. Choncho izi zikusonyeza kuti Hajj iyenera kuchitika kamodzi pamoyo kwa anthu omwe zintchito zawo zimayima ngati iwo palibe.

Koma kwa anthu omwe zintchito zawo sizofunikira kwambiri ndipo anthu ena akhoza kukwanitsa kuyendetsa ntchito zimenezo ngati iwo atapita ku Hajj, palibe vuto lililonse kwa iwo kupanga Hajj m’mene angafunire ngati ali oti akhoza kukwanitsa kulipira maulendo onsewa komanso kuwasiyira mabanja awo zonse zofunika pamoyo wawo panthawi yonse ya kusapezeka kwawo chifukwa cha maulendo awo okapanga Hajj.

Kwa onse amene angakwanitse kupanga Hajj koposera kamodzi, ayenera kumvetsera ndi kupezerapo mwayi ndi uthenga omwe uli mu Hadith’ ili pansiyi: “Yemwe amapanga Hajj kamodzi, amakwaniritsa zofuna zake, ndipo amane amapanga kachiwiri Amamufunitsitsa Mbuye wake, ndipo amene amapanga Hajj yake kachitatu, thupi lake ndilotetezedwa ku moto”.

Kusiyana kwa Hajj ndi Umrah

Pamene Hajj iri yokakamizidwa komanso imachitika m’miyezi yodziwika yomwe ndi Shawwal komanso DhulHijjah, Umrah (Hajj yaying’ono) imachitidwa mukufuna kwa munthu ndipo ilibe nthawi yake yeniyeni pachaka ngati m’mene iriri Hajj. Komanso Umrah siyimalira kuyima pa Arafah. Izi zikutanthauza kuti Umrah siyimatenga malamulo a Ihram pofuna kupanga Hajj usanafike mwezi wa Ramadhan. Koma Ihram ya Umrah imatha kuchitika nthawi ina iliyonse makamaka m’mwezi wa Ramadhan.

Mitundu ya Hajj