Fodya ndi chimodzi mwa zinthu zomwe zangobwera posachedwapa ndipo mbuyomu kunalibe. Nthawi ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam kunalibe kugwiritsa ntchito fodya, komanso mbuyo mwakemo nthawi ya Atumiki onse kunalibe. Nthawi ya ma Shawabanso kunalibe fodya, ngakhalenso nthawi ya ma taabieen kunalibe. Komanso nthawi ya ma Imaam olemekezeka kunalibe fodya. Fodya anayamba kudziwika mzaka za mu 10th century pambuyo pa msamuko wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, ndipo maiko a Chisilamu fodyayu anayamba kuwoneka ku Egypt ndi maiko ena. Choncho pakuti zangoyamba posachedwapa, anthu anakamba zosiyanasiyana pa nkhani yofuna kudziwa kuti kodi mu CHisilamumu fodya ali pati, poti Mtumiki sanakumane ndi fodya komanso ma SWahaba ndi ma imam onse omwe timawadalira aja sanakumane ndi fodya. Kodi ndi ndani amene angatilongosolere zoona zenizeni za fodya kuti ndi haram kapena makrooh kapena jaaiz?

Zinthu zikafika pamenepo tsopano timapita pa aaya yonena kuti:

فَإِنْ تَنَازَعْتُمْ فِي شَيْءٍ فَرُدُّوهُ إِلَى اللَّهِ وَالرَّسُولِ إِنْ كُنْتُمْ تُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ ذَلِكَ خَيْرٌ وَأَحْسَنُ تَأْوِيلًا

“Ngati mutatsutsana pachinthu chilichonse, chibwezeni kwa Mulungu ndi Mtumiki wake, ngatidi mukukhulupilira Mulungu ndi tsiku lomaliza, kutero ndibwino; Ndipo zotere zili ndi zotsatira zabwino.” Al Nisaai 59

Choncho tiyendera Qur’an ndi Sunnah poti zinthu ziwiri izi zinalongosola lamulo la chilikonse chomwe chinalipo panthawiyo, chomwe kunalibe komanso chomwe chidzapezeke mtsogolo. Palibe chomwe Qur’an ndi Sunnah inasiya osalongosola, ndipo izi umboni wake ndi Surah Al Maaidah 3

الْيَوْمَ أَكْمَلْتُ لَكُمْ دِينَكُمْ وَأَتْمَمْتُ عَلَيْكُمْ نِعْمَتِي وَرَضِيتُ لَكُمُ الْإِسْلَامَ دِينًا

Lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu ndipo ndakwaniritsa pa inu chisomo changa. Ndakusankhirani Chisilamu kukhala chipembedzo chanu

Tiyambe nkhani yathu ndi kuona mmene fodya aliri.

Fodya amaononga thupi, komanso ndi chimodzi mwa zinthu zoipa. Zoipa komanso zoononga thupi zones ndi haram kuchokera mu Qur’an. Koma ngati zitakhala kuti nzosapereka mavuto ndipo zili ndi phindu linalake, kapena kuti zimathandiza kuchira ku matenda ena ake, zimenezo zikhala zololedwa.

Ndisanayambe kulongosola, tidziwitsane kuti munkhaniyi timvamo izi:

Chiyambi cha Tabago (Tobacco) fodya

Zomwe zimapezeka mu Fodya

Chislamu chimati bwanji pa lamulo la kusuta

Maumboni okwanira okupanga kusuta kukhala Haraam

Ma ulamaa anati chani pankhani yakusuta

Mavuto omwe kusuta kumabweretsa ku umoyo wamunthu

Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:

 لَا ضَرَرَ وَ لَا ضِرَارَ

Hadith yaifupi kwambiri koma tanthauo lake lalikulu kwambiri, tanthauzo lomwe timabweretsa pa hadith imeneyi silikwanira, mwachidule hadithiyi imatanthauza kuti usazipondereze (kuzichitira zoipa kapena kuzipweteka) komanso usapondereze ena (powachitira zoipa) …

Apa haram ikutha kutulutsidwapo chifukwa madokotala onse padziko lapansi anagwirizana kuti kusuta kumawononga moyo wa osutayo komanso onse amene utsi wafodyayo wawafikira. Ndiye kuti apa wazipondereza powononga moyo wako kapena kuzipha mwadaladala komanso kupha ena osalakwa. Palibe yemwe angatsutse lero lino kuti fodya amawononga moyo.

Ndisanafotokoze ma umboni akuyipa kosuta, tiyeni tiwone dzina la Tobacco fodya linabwera bwanji nanga zinayambira kuti?

Chiyambi Cha Tobago (Tobacco) Kapena Kuti Fodya Pa Chichewa

Tobago ndi mbewu yomwe imachokera mu gulu la Aubergine (Eggplant) kapena kunena kuti mabiringanyo pachichewa chobwerekera kuchokera chiluya,,, indetu, dzina loti biringanyo linachokera kuliwu la chiluya (Arabic) lomwe ndi

بَاذِنَجان – Badhinjaani

Ndipo gulu limeneli linatchedwa ndidzina loti Tabago chifukwa choti zinkadzalidwa kapena kumera kwambiri mdera lina lotchedwa Tobago lomwe limapezeka ku South America mu ka chilumba kotchedwa Trinidad and Tobago, lomwe lachita malire ndi India, ndipo ndi imodzi mwa ma state aku America.

Chifukwa choti zimadzalidwa kwambiri ku Tobago, anthu ankaitcha mbewu imeneyi kuti “mbewu yaku Tobago ija” mpakana dzina linakwanira kukhala Tobago chifukwa cha dera lomwe anali kudzalidwa, komanso kuchuluka kwa anthu osuta omwe anali kupezeka mukachilumbaka.

Zikulongosoredwanso mma history kuti kunali ngalande zomwe zinkakumbidwa zomwe munkadutsa ma pipe omwe anthu ankasutira, ngati mmene anthu amachitira akamasuta shisha. Azungu aku Europe anayamba kutenga mbewu ya Tobago ija kupititsa kwawo, ndipo Christopher Columbus ndiyemwe akuoneka kuti anali oyambilira kupititsa masamba a fodya ku Europe, komanso oyambilira kudzala mbewuyi ku Europe anali President Jan Newcot; iye anadzala ku State House ndipo atafunsidwa kuti ndi mtengo wanji uwu, anati ndi Tobago. Koma anthu ankalephera kuchita pronounce dzinali ndipo ankati Tobacco, mpakana lero dzina la fodya linasanduka kukhala tobacco.

 Kodi Nanga Mufodya Mumapezeka Zichani?

Mufodya mumapezeka zinthu za poizoni zopitilira mazana awiri, 200 (poisonous substances) zomwe zimasiyana malingana ndi mtundu wa fodya komanso njira ya masutidwe ake, komanso mmasamba afodya mumapezeka Alkalinities wa poison monga Nicotine ndi poison osiyanasiyana yemwe anthu sanamutulukire pakadali pano. Ma poisonous chemicals oopsa kwambiri monga alkalinity omwe amapezeka mu fodya, amatchedwa aviatrix omwe ndi poison owopsa kwambiri. Kafukufuku akuwonetsa kuti poisoniyu akalowa mu thupi lamunthu atha kumwalira mwachangu, ndipo mmasamba a fodya owuma mumapezeka 82% wa poisoniyu. Utsi omwe umatuluka munthu akamasuta umafalitsa poisoniyu komanso kumuwonjezera mphamvu kamba kakuwotchedwa komwe kumachitika.

Mu fodya muli poison wochuluka woti kuti timulongosore yense zingatitengere nthawi.

Tiyeni Tiwone Lamulo Lakusuta Mchislamu

Kusuta fodya ndi haram. Kugulitsa, kugawa, kulandira; zonsezo ndi haram ndipo zikuchokera mma umboni odziwika bwino komanso odalirika, mu Qur’an komanso mu Sunnah mpakananso mmawu ama ulamaa athu, Allah awachitire chifundo.

Indetu, zidakwa za fodya pamodzi ndi anthu ena omwe amapindula kuchokera mu business ya fodya, amatsutsa zoti fodya ndi haram akuti chifukwa choti sadayambe awerenga mu Qur’an kuti fodya ndi haram, kapena mau aliwonse achindunji oletsa kusuta fodya monga mmene analetsera zina monga chiwerewere, mowa ndi zina zotero. Akuti poti fodya sanamutchule mu Qur’an, ndiye kuti si haram koma makrooh!

Dziwani kuti chinthu chimatha kukhala haram mu Qur’am momwemu popanda kuchitchula dzina, koma kuletsedwa kumadza pagulu ndipo chinthuchomwe tikufuna kudziwacho chimakhala mgulumo. Ndipo izi kwa omwe amakonda kuwerenga Qur’an ndikumaimvesetsa, amakumana nazo ndithu akamawerenga.

Umboni Kuchokera Mu Qur’an Komanso Sunnah

Tiyambe Ndi Qur’an Yolemekezeka:

Allah Ta’la akunena pa Sura 7:157 kuti:

وَيُحِلُّ لَهُمُ الطَّيِّبَاتِ وَيُحَرِّمُ عَلَيْهِمُ الْخَبَآئِثَ

“Zaloledwa kwa iwo zonse zabwino ndipo zaletsedwa kwa iwo zonse zoipa.”

Tikawonetsetsa tipeza kuti utsi womwe umatuluka munthu akamasuta ndi woipa kwambiri, komanso ndi umene umabweretsa mavuto kumoyo wa munthu. Kuwonjezera apo umabweretsa fungo loipa. Tangoganizani mmene amanunkhira mkamwa munthu osuta fodya, ngakhale atakhala kuti tsiku limenelo sadasute, koma chongokupumirani mumasowa mtendere.

Mmalo ena pa Qur’an 2:195, Allah Ta’ala akunena kuti:

ولا تلقوا بأيديكم إلى التهلكة

“Musaziyike ndi manja anu kuchiwonongeko”

Tikawonesetsa, utsi wafodya umatipereka kumatenda oopsa komanso okupha, monga TB, Cancer ndi ena ambiri. Pa Qur’an 4:29, Allah Ta’ala akunena kuti:

ولا تقتلوا أنفسكم

“Musaziphe nokha”

Kusuta fodya ndiko kuzipha wekha kumeneko, kamba kamatenda omwe amabwera kwa iwe osutawe, komanso kwa anthu ena omwe ukuwawulutsira utsi wakowo.

Pa Qur’an 2:119 pamene Allah Ta’ala akunena kuti:

وإثمهما أكبر من نفعهما

“…ndipo zabwino zake nzochepa kwambiri kuposa zoyipa zake zomwe ndizochuluka.”

Potengera kuipa kwa zolezeretsa monga mowa, tikudziwa bwino lomwe kuti fodyanso amatha. Utsi wafodya ulibe ubwino uliwonse koma kuwononga kokhakokha, kodi izi sizikukwanira kuti kusuta fodya kukhale haram?

Allah Ta’ala akunenanso mu Qur’an 17:26-27 kuti:

ولا تبذر تبذيرا…إن المبذرين كانوا خوان الشياطين

“…ndipo usamwaze chuma chako mosakaza, ndithudi omwaza chuma chawo moononga ndi abwenzi a satana.”

Munthu owononga chuma chake pogula fodya, komanso kusakaza chuma munjira iriyonse, amasanduka abwenzi a satana asakudziwa. Anathu omwe amamukulira mtima Mulungu amanena mosimbwa kuti: “chuma ndi change ichi ndipo ndili ndi ufulu wochgwiritsa nytchito yomwe ndafuna, ndisiyeni ndidyelere thukuta langa…” Ena akamamva ma Sheikh akuwalangiza za kuwopsa kwa kuwononga chuma mwachisawawa, amayankha kuti: “ma sheikh nsanje, akufuna nafe tifanane ndi iwowo, tisakhale ndi ndalama monga mmene iwowo aliri, akutiletsa kugwiritsa ntchito ndalama zathu…” Dziwani kuti kuteroko sikulimbana ndi munthuyo, koma Allah.

Allah Ta’ala akusimba za chakudya cha anthu akumoto onga amenewa, pa Qur’an 88:6-7 kuti:

ليس لهم طعام إلا من ضريع…لا يسمن ولا يغنى من جوع

“Anthu akumoto sakakhala ndichakudya china kupatula minga (za mmitengo yak u moto) zomwe sizikawanenepetsa kapena kuthetsa njala”

Fodya alibe phindu lirilonse mthupi lamunthu kupatula mavuto, kuwononga thupi komanso kupha kwapang’onopang’ono, ndi slow poison amene uja ndithu. Yemwe anganene kuti fodya amathetsa njala kapena amanenepetsa ndi munthu yekhayo yemwe walezera ndi fodyayo, ndipo posafuna kusiya akhonza kuyankhula zimenezo.

Kodi zonsezi sizingakhale umboni wokwanira kuti kusutako kukhale koletsedwa?

Imeneyo inali Qur’an, tsopano tiyeni tiwone

Umboni Ochokera Ku Sunnah

Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti

لا ضرر ولا ضرار

“usazipatse mavuto wekha komanso usapatse mavuto anthu ena, usazipondereze wekha komanso usapondereze ena.”

Ndiye utsi wafodya umamuwononga mwini osutayo komwe kuli kuzipondereza yekha, komanso kumawawononga ena omwe utsiwo ukuwafikra.

Anthu sasamala, amangosutira pagulu ngakhale mnyumba. Akatero amununkhize mkazi kukamwa .. kuwapondereza anthu ena kumeneko .. kuwapha ndi matenda anthu osalakwa.

Mu hadith ina Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti

إن الله كره لكم ثلاثا قيل وقال وكثرة السؤال وإضاعة المال

“Allah amadana nazo mwa inu zinthu zitatu ,kukonda kuyankhula zopanda pake ,kuchulukitsa mafunso, kuwononga chuma pazinthu zopanda pake

Ndiye kusuta kumangowononga chabe ndalama zako pazinthu zopanda pake.

Mtumiki salla Allah alaih wasallam akunenanso kuti

من تحسى سما فقتل نفسه، فسمه في يده يتحساه في نار جهنم خالدا مخلدا فيها أبدا

“Munthu yemwe angazitengere poison nkuzipha yekha, akafika tsiku lachiweruzo poison wakeyo ali mmanja ndipo adzikamwetsedwa kumoto komwe akakhale muyaya.”

Mmene talongosolera kale kuti mu fodya mumapezeka poison yemwe amapha munthu, ndiye kuti kusutanso ndikuzipha kumeneko komwe munthu osuta aadzatenge ndudu zakezo mpaka kumoto komwe azikazunzidwa nazo wakwemba sona chakanyakule achikanundu wawowo kumoto kuchakapedweje ipwetesi ya ndudusyo,,,alipikanile yele.

Mumiki salla Allah alaih wasallam akunenanso kuti

من كان يؤمن بالله واليوم الأخر فلا يؤذ جاره

“Munthu amene wakhulupirira mwa Allah nditsiku lomaliza savutitsa oyandikana naye

Mukamasuta fodyayo mumavutitsa naye akazi anu, abale anu komanso ma neighbor anu, oyandikana nawo malo okhala. Komansotu mumavutitsa Angelo amene amawayandikira anthu omwe akuswali, pamene inu muli pambali pa osasuta fungo lamkamwa mwanu liri buu mukangotsekula kamwa; kusokoneza anzanu

Mu Hadith ina Mtumiki salla Allah alaih wasallam akunena kuti:

لا تزول قدما عبد حتى يسأل عن عمره فيم أفناه وعن علمه فيم فعل فيه وعن ماله من اين اكتسبه وفيم أنفقه وعن جسمه فيم أبلاه  

“Mapazi akapolo wa Allah sakasuntha Tsiku la Chiweruzo mpaka atafunsidwa zinthu izi; moyo wake anaugwiritsa ntchito bwanji? Maphunziro ake anawagwiritsa bwanji ntchito? Chuma chake anachipeza bwanji ndipo anachiwononga bwanji? Nanga thupi lake analigwiritsa ntchito bwanji?”

Ndiye m’bale wafodyawe uziganizire kuti ukadzafunsidwa mafunso amenewa udzayankha chani? Udzayankha kuti ndalama yako unaigwiritsa ntchito bwanji? Moyo wako, nanga thupi lako?

Lero lino ukhonza kuyankha mafunso amenewo pompa, poti ine ndiotumidwa kudzakuchenjeza, koma pamaso pa Allah ukayankha chani m’bale wanga? Usaganize kuti zikatheka kumunamiza kapena kumunyengelera Mbuye wako? Ukakayankha kuti ndalama zako unawonongera kugula fodya zikakukomera patsikulo? Ukakafunidwa kuti cancer yomwe unavutika nayo ija unaitenga kuti, wakhonzeka k\zokayankha kuti unamutenga mu fodya? Wakonzeka zoti TB yakoyo unaitengera ku fodya? Kodi iwe Allah sanakuchenjeze za kudziwononga thupi? Sanakuchenjeze za kuika moyo wako pachiwonongeko? Sanakulangize zakudya ndikumwa zabwino zokhazokha? Unali kuti padziko lapansi pamene ochenjeza ankachenjeza iwe nkumayankhula motumbwa kuti ukudyelera chuma chako?

Amenewotu ndiye maumboni kuchokera mu Qur’an ndi Sunnah. Zija zomwe ambiri amanena kuti mu Qur’an sadaletse kusuta fodya, Mtumiki sadaletse kusuta fodya, chifukwa cha kusadziwa kuti kodi kuletsedwa kwa chinthu mu Sharia kumabwera motani. Kodi ma aayah ndi ma Hadith amenewo angawaike pati pankhani ya fodya?

Allah atiwonjezere kuzindikira

Tatiyeni tsopano tiwone kuti ma Ulamaa anati chani pakhani ya kusuta?

Anthu ena amanena kuti ma Ulamaa anagwirizana kuti kusuta ndi makrooh chabe (zoipa), osati haram. Komai ne funso langa limabwera ndiloti kodi ma ulamaa ake ati amenewo omwe ananena kuti fodya ndi makrooh? Ine ndikamafufuza zokamba za ma Ulamaa, ndimayambira ma Ulamaa ochokera mma Taabieen ndi ma Taabi’ Taabieen, kenako omwe adadza pambuyo pawo olungama. Choncho tiyeni tiwone kuti ma Ulamaa ochokera mma madh’hab anayi aja anati bwanji pankhani imeneyi?

Madh’hab a Hanafiyy, mu buku lotchedwa

تنقيح الجامدية

Anati: “ngati zatsimikizika kuti utsi omwe ndudu imatulutsa umamuwononga munthu, ndiye kuti kusuta kukhala Haram. Lero sitinganene kuti kusuta ndikwabwino chifukwa aliyense amadziwa kuti kusuta kumawononga moyo, choncho kusuta ndi haram”.

Madh’hab a Shaafi’yy, mu buku lotchedwa

بغية المسترشدين

Anati: “Ndi haram kugulitsa ndudu, kapena mwachidule fodya ndiwoletsedwa kwa amene amasutayo komanso kupereka kwa wina wake, ngakhale kulima  ndi haram, chifukwa fodya ndizoziwika bwino kuti ndi oyipa. Mu fodya muli kuwononga chuma komanso kubweretsa halaal kukhala haram.

Madh’hab a Hanbaliyy anati, “ndizachidziwikire kuti Mtumiki salla Allah alaih wasallam komanso ma Ulamaa, analongosola momveka kuti ndi haram, choncho kusuta ndi haram.

Madh’hab a Maalikiyy anati: “ndizoletsedwa imam kukhla munthu osuta fodya komanso kugula, kugulitsa, kusuta ngakhale kugawa fodyayo ndi zoletsedwa.”

Madh’hab onsewa palibe yemwe ananena kut kusuta ndi makrooh, koma anati ndi haram.

Mavuto Omwe Kusuta Kumabweretsa

Kusuta ndikoipa kwambiri, ndipo kwina mwa kuyipa kwakusutaku kuli motere:

Kusuta kumapha: Unduna wa za umoyo ku America unalongosola kuti pafupifupi anthu 100 amamwalira kamba kakusuta.

Kusuta Kumaononga mpweya: Kafukufuku akusonyeza kuti kusuta kumabweretsa chiwopsezo kumoyo wa munthu, moti akasuta ndudu imodzi atakhala nyumba pakatha 4 hours amafanana ngati wa suta ndudu 10 zomwe zimawononga osutayo komanso omwe angalowe nyumbamo amakhunzidwa.

Fodya wa mumphuno amawononga top layer yamkati: mwamphuno: Munthu amatha kumva kuyabwa mphuno, zomwe zimapangitsa kumva kuwawa, ndipo zimatha kupitilira mpaka kukalowa mmakutu, ndipo makutu amatha kukhunzidwa ndikubweretsa mavuto a kusamva komanso munthu amatha kudwala topical cancer

Tifumbi tafodya:  Nditowopsa kwambiri moti zimawononga mkamwa komanso timayambitsa esophagitis, komanso ma enzymes obweretsa malovu amachuluka, zomwe zimapangitsa munthu osuta kulavula pafupipafupi, ndipo mkamwa mumawuma zomwe zipangitsa munthu kulephera kuyankhula zonveka pagulu. Izitu mumadziona zikuchitika. Mkamwa mwa osuta fodya mumapepera fodya akafikapo.

Kusuta kumawononga mapapo: Choncho munthu amapuma movutika monga tanena kale mu fodya mumapezeka ma poisonous chemicals ngati Nicotine yemwe amawononga ma lung tissues, ndipo zotsatira zake ndi izi:

  • Kuchepa kwa percentage amapupidwe pa second imodzi
  • Kuchepa kwa volume yampweya mu expiratory system kapena kuti exhalant.
  • Kuchepa kwa mpweya olowa, zomwe zimapangita kudyeka kwa mapapo, choncho magazi oyipa amayenelera mmapapu omweno amasokoneza chitetezo cha mthupi. Choncho osuta amakhala prone kapena exposed ku matenda osiyanasiyana.
  • Zimayambitsa cancer wa mmapapu
  • Kusuta kumawononga mtima wamunthu, zomwe zimabweretsa mavuto ku mtima pamapopedwe amagazi nthupi
  • Kusuta kumachepetsa oxygen mthupi la munthu chifukwa chazimpweya zoipa zomwe munthu amalowetsa mthupi lake
  • Misempha ya pamtima imadzadza utsi omwe umalepheretsa misemphayi kugwira ntchito yake bwino.

Mavuto Omwe Amapezeka Mma Blood Vessels (mmisempha ya magazi) Kamba Kakusuta

Chifukwa cha utsi womwe umadzadzana mmablood vessels, zimapangitsa munthu kukanika kuyenda kamba koti magazi sayenda mokwanira komanso magazi ake awonongeka; zimenezi zimabweretsatso kulumala kosayembekezereka.

Mavuto Omwe Amabwera Ku Ma Sense Organs Kamba Kakusuta

Munthu osuta concentration imamuchepera; memory imathawathawa kwa osuta, zomwe zimapangitsa munthu kuyiwala pafupipafupi.

Kusuta kumawononga maso

Kusuta kumawononga makutu

Makomedwe a chakudya amathawa kwa osuta

Kusuta kumasokoneza njira zomwe mkozo umadutsa komanso munthu amakanika kuchita banja lake moyenera kamba kakufooka kwa thupi komwe kumadza kamba kakusuta

Kusuta kumapha njira zobelekera, ndipo mkazi atha kupatsidwa vutoli ndi mwamuna wake osuta mkusanduka osabereka.

Chilakolako chimachepa, ukalowaso nyumba suchedwa kutopa

Kuyipa Kwa Kusuta Kwa Mayi Oyembekzera Komanso Kamwana Kobadwako

Kusuta kumabweretsa ma miscarriages/mitayo komanso kubadwitsa ana masiku asanakwane.

Kusuta kumabweretsanso imfa za ana mchikuta.

Kusuta kumapangitsaso mayi kuvutika panthawi yobereka.

Kusuta kumapangisa ana kubadwa ndi matenda monga Asthma; Ana amabadwa olumala kamba kakusuta kwa mayi kapena bambo nyumbamo.

Ana amatha kubadwa osawona, osamva, kapena osayankhula

Ana amatha kubadwa ndi scale yotsika kambiri zomwe zimapangitsa kuyikidwa mmagetsi kuti akhwime.

Tisamale ndikusuta chifukwa utsiwo ukawafikira anthu ena ndiye kuti mwawapatsa mavuto komanso matenda. Akakhala mayi oyemebezera ndiye kuti mwamupha pamodzi ndi mwana yemwe asanabadwe. Nanga nanga yemwe akuyembekezera mapasa? Dziwani kuti tikayankha tsiku lachiweruzo kumavuto omwe tinapereka kwa ena!!

Ndiye osuta onse akuyenera kumuwopa Allah Ta’la ndipo ayesetse njira iriyonse kupanga tawbah ndikusiya kusuta ndikumagwira ntchito zomwe zingawatalikitse ku chilakolako cha fodya.

Fodya ndi haram

Wasalaam Alaikum warahmatullah wabarakaatuh