Buku la Fazail e Amaal (Fadhwailul A’maal)

فضائل الأعمال

“Maubwino a Ntchito za Bwino”

“Sheikh Muhammad Zakariya Kandhlawi”

download source

Buku la Fadhaailul A’maal (فضائل الأعمال), lomwe pachiyambi linkatchedwa Tablighi Nisaab (تبليغي نصاب) mu chi Urdu ndipo mu chi Arab: Nisaabu Al Tabligh (نصاب التبليغ), linalembedwa ku India ndi Muhammad Zakariya Al Kandahlawi.

Bukuli liri ndi mitu yosiyanasiyana yokamba za ntchito zabwino zomwe anadzilemba kuti a Jama’atu Tablighi adzitsatira. Choncho linasanduka kukhala buku lawo lodalirika kwambiri pambuyo pa Qur’an monga mmene aliri mabuku a Al Bukhari ndi Muslim kwa Ahlu Sunnah.
Bukuli amaliwerenga akasonkhana, komanso amaliphunzitsa mma madrasa ndi mminzikiti.
Kumayambiliro chifukwa choti linalembedwa mu Urdu, silinafalikire mmaiko a ma Arabs, koma maiko okhawo momwe munkapezeka a Jama’atu Tabligh monga India, Pakistan ndi Afghanistan.
Sheikh Hammoud AlTuwaijari ananena mu Al Qaulul Baleegh page 11 kuti:
“..Ndipo buku lomwe liri lofunikira kwambiri kwa Jama’atu Tabligh ndi Tablighi Nisaab lomwe analemba mmodzi wa atsogoleri awo dzina lake Muhammad Zakariya AlKandahlawi ndipo amalisamalira ndikulilemekeza kwambiri, komanso amalikudza monga mmene Ahli AlSunnah amalemekezera mabuku awiri  Sahih AlBukhari ndi Sahih Muslim komanso mabuku ena a Hadith. Choncho a Tabligh analipanga bukuli kukhala lodaliridwa pakati pawo komanso kobwelera posakasaka malamulo a seen ndi maumboni. Kunena mosabisa,  malinga ndi mmene liliri bukuli, tikalifasilira tipeza kuti muli zambiri za shirk,  bid’ah komanso nkhani zosadziwika pochokera … mulinso ma hadith abodza ndi ofooka”. Sheikhwo akutero.
Sheikh Shamsdeen Al Afghani akulongosola mu buku lawo lotchedwa Juhood Ulamaail Hanafiya fi Ibtwaal Aqaaidil Qubooriya vol. 2/776:
“Ma ulamaa akuluakulu a Deoband (India) ali ndi mabuku awo omwe amawalemekeza, koma mkati mwakemo muli zisokonezo zochuluka, ndipo analitchula buku la NissabTabligh komanso njira za Tabligh. Ngakhale bukuli liri choncho,  anthu awa a Deoband sanalengedze za kulipewa buku limeneli kapena kuwachenjedza anthu, kusiya kupanga print, kugulitsa ndi kugula…”
Izi zikupezeka mu Fatawa Lajnat Daaimah vol.2/97.
Ma ulamaa akuluakulu a ku Deoband(India) Ali ndi mabuku omwe amawalemekeza kwambiri,  koma ndi mabuku amend Ali osokonekera chifukwa mumapezekamo bid’ah komanso shirk yambiri. Limodzi mwa mabukuwo ndi Fadhaailul A’maal. Bukuli ngakhale ku Indiako limadxiwika kuti ndi losocheretsa, koma sanasiye kupamga print ndikulifalitsa komanso kugulitsa, mma bookshop.
Committee yailulu younika ndi kutulutsa ma fatwa ya Fataawa Allajnati Aldaaimah onayankha fumso my (Majmu’at Thaaniyah vol. 2/97) lokhunza munthu yemww anali kukhala ku Britain ndipo ankafuna kulowa gulu la tabligh, koma ali mkati mwa kuwerenga mabuku a tabligh anapeza buku limeneli ndipo linamudabwitsa kwambiri pa zomwe limakamba pa page 113, mutu #5 (malinga ndi buku lomwe anali nalo iyeyo), nkhani ya munthu wamalonda yemwe anamwalira ndipo anagawa chuma chake pakati pa ana ake … ndipo anasiya pambali pa chuma chake chambiri, tsitsi la mmutu mwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam lomwe  mwana wake wamng’ono anasankha kuti atenge mmalo mwa chuma China chilichonse. Ndipo akuti mkulu wake, yemwe anasankha chum osati tsitsi,  anasauka koopsa patantha kanthawi kochepa ndipo was tsitsi uja anasanduka olemera kwambiri. Pambuyo pa kumwalira kwa wamng’ono uja amene anasankha tsitsi uja, mmodzi wa ma swaaliheen (ochita zabwino) anaona Mtumiki salla Allah alaih wasallam akumuuza kuti: “yemwe ali ndi vuto apite kumanda a sheikh uyu (amend anatenga tsitsi uja) ndipo akapemohe Allah Ta’la pa mandapo, dua yake ikayankhidwa”. Izi zikupezeka mu Fadhaailul A’maal, komanso buku lina lotchedwa “Taarikh Mashaaikh Jatthat” page 232.
Imeneyo ndi shirk yaikulu, chifukwa Mtumiki sanasiye tsitsi lake kuti tidzipezeramo zofuna zathu, ndi kwa Allah kokha kumene tingapemphe kudzera mumbiri zake za Allah, maina ake, koma osati kudzera mwa munthu yemwe anamwalira kapena tsitsi lake.
Pankhani imene ndakamba kale ya munthu wa ku Britain ija,  anafunsa ma sheikh funso ili:
Kodi yemwe analemba buku limeneli akuyenera kukhala Msilamu kapena ayi? Chifukwa zomwe analembazi zilibe imboni mu Quran ngakhale mma hadith,  komanso ndi shirk yaikulu.
Ndipo anayankhidwa motere:
Zomwe zikupezeka mu buku limeneli komanso nkhani yomwe walongosolayo ndi bid’ah yaikulu komanso ndi zisocheretso zomwe shariah imakana…ziribe umboni kuchokera my Quran ngakhale my Sunnah za Mtumiki. Ndipo palibe yemwe anganene, komanso palibe yemwe angakhulupilire kapena kutsatira zimenezo kupatula yemwe ali osochera pa chikhulupiliro chake
Chikhulupiliro choti tsitsi la Mtumiki lidakalipo komanso yemwe angasungireyo akhala olemera….
Chikhulupiliro cha kuona Mtumiki kutulo akumulangidza zopanga dua ku manda amunthu….
Zonsezo ndi zabodza komanso zopanda umboni.
Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti: ndithu shaytwaan samandifanizira ine … tsopano zingatheke bwanji Mtumiki kulamula kuti ukapange dua pa manda a munthu, kumachita Mtumiki yemweyo pamene anali moyo analetsa kupanga dua pamanda a munthu komanso anachenjedza,  kuchenjedza kwenikweni. Komanso Mtumiki analetsa kulemekeza Atumiki ndi anthu ochita zabwino,  kulekeza kopyola muyeso komchitisa munthu kugwera ku shirk,  komanso kupanga dua kudzera mwa iwo pambuyo poti amwalira. Mtumiki salla Allah alaih wasallam sanamwalire nkusiya seen asanaikwaniritse….palibe chomwe sanalongosole Mtumiki mu deen.
Kukhulupilira zoti dua imayankhidwa pa manda ndi bid’ah ndipo ndi cholango choopsa chifukwa ndi shirk yaikulu poti ukupempha pa manda mmalo mwa Allah Ta’la. Ndipo kukhulupilira kuti mavuto kapena mtendere zimabwera chifukwa cha manda,  imwneyo ndi shirk chifukwa opwreka mavuro ndi mtendere ndi Allah yekha.
Izi ndi zina mwa zomwe zikupezeka m’bukuli
Mulinso chikhulupiliro choti ma swaaliheena anthu ochita zabwino, omwe satsatira za dziko,  samafa….koma kuti mizimu yawo imangosamutsidwa kuchoka malo kupita kwina,  ndipo akaikidwa mmanda amakhala akugwira ntchito ya kuthandiza anthu omwe amakhala akupita kukapempha,  monga mmene anali kuchitira asanamwalire.
Izitu ndi zina mwa zikhulupiliro zoonongeka za Sufi. Alive nazo umboni, ndipo mukati mufufuze maumboni a zomwe bukuli likukamba,  mupeza kuti ndi zoletsedwa zokhazokha. Ma aayah ndi ma Hadith ambiri amanena kuti munthu aliyense padziko pano amamwalira tawerengani Surah Al Zumar aayah 30, Surah Al Anbiyaa aayah 34-35
Komanso ma hadith opanda chikaiko alongosola kuti munthu aliyense akamwalira ntchito zake zimaduka kupatula zitatu: maphunziro ake oti amthandize  mmanda komanso ku aakhirah,  mwana wake wabwino kuti adzimpangira ma dua,  swadaqa yopitilira.
Komanso maliro mmanda paokha sangapange chodzithandiza kapena kuwapatsa mavuto,,,, choncho sizingatheke kuthandiza ena kapena kuwapatsa mavuto.
Kudzera mmaumboni amenewa,  tipeza kuti nzoletsedwa kupempha chithandizo chakuthana ndi mavuto a mu umoyo kwa wina wake, makamaka zinthu zoti palibe yemwe angakwanitse koma kwa Allah mmodzi yekha.
Kupempha anthu okufa ndi shirk yaikulu.
Yemwe angakhale ndi chikhulupiliro choti choterocho ndiye kuti watuluka mu njira yoongoka,  ndipo akuyenera kupanga tawbah yeniyeni ndipo atsimikize kuti sadzabweleranso ku ntchito yoipayi.
Pomaliza, a Jamaat Tabligh omwe amapezeka mmaiko a ma Arabs, akasonkhana amalikweza buku la Riyaadhu Saliheen. Ndipo maiko ena osakhala a chi Arab amalikweza buku la Hayaatu Swahaabah ndi Fadhaailul A’maal. Mabuku awiriwo (Hayaatu Swahaaba ndi Riyaadh Swaliheen) ndi mabuku abwino ndipo ndi ovomerezeka ndi shariah,  mulibe za bid’ah.  Koma linalo ndiye ngozi pa aqeedah chifukwa ladzadza ndi bodza,  nkhani zopeka,  ma hadith ofooka komanso zompekera Mtumiki.
Mwachidule,  ma Ulamaa onse otsatira Sunnah ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam akhala akuchenjedza za bukuli,  lomwe limatchedwa kuti Tablighi Nisaab kapena Fadhaailul A’maal kuti sizololedwa kwa Msilamu aliyense *kulimbana nkuwerenga bukuli ndi chikhulupiliro choti muli zabwino, koma adziwerenga mabulu abwino pambuyo pa Qur’an,  komanso mabuku omwe olemba ake ndi ma ulamaa a Sunnah ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam
Pomwe buku lomwe liri ndi bodza, bid’ah shirk….Msilamu sakuyenera kulipezera malo mumtima make ngakhale munzeru zake.
Allah ndi odziwa zonse