Kutulutsa zinthu za mu Mzikiti
Sizololedwa kutulutsa zinthu za mu mzikiti kukadzigwiritsira ntchito malo ena osakhala munzikiti momwemo.
Kubwereka mkeka, kapena Qur’an kaya mabuku aliwonse komanso china chirichonse chomwe chinaikidwa mu mzikiti kuti chidzigwiritsidwa ntchito mmenemo, ndizosaloledwa kuchitulutsa nkukagwiritsa ntchito malo ena monga mmadrasa, kupatula ngati mzikiti wina uli ndi zambiri ndipo wina ulibe kalikonse, nzololedwa kugawa zina kudzipititsa munzikiti winawo.
Kafir Kulowa mu Mzikiti kukakonza zina ndi zina
Palibe vuto kafir kulowa mu mzikiti ndicholinga chokakhonza (kukapanga mainatenance) malo ena ake. Koma apezeke omuyang’anira wa Chisilamu, asakhale yekha kapena ma kafir okhaokha.
Kukongoletsa Mizikiti
Mu Hadith yochokera kwa Ibn Abbas radhia Allah anhu:
لتزخرفنّ كما زخرف اليهود والنصارى
“mudzakongoletsa ngati mmene amakongoletsera Ayuda ndi Akhristu…”
kukongoletsa kwake kofanana ndi momwe amakongoletsera a Yuda ndi a Khristu mma tchalitchi mwawo, komanso kukongoletsa komwe kumatangwanitsa anthu oswali. Pomwe kukongoletsa komwe sikumatangwanitsa oswali koma kumapereka kukhanzikika kwa mtima mmalo molingana ndi nyengo zonse,  kulibe vuto.
Masiku ano mupeza mu mzikiti akongongoletsamo mopyola muyeso polembalemba zinthu mmakoma, ku qibla agobagoba ndi ma aayah kotero kuti oswali maso amakhala busy kuwerenga zomwe zagobedwazo, komanso ena amakongoletsa poika zinthu za mtengo wapatali ndi chikhulupiliro choti kumaononga chuma pokongoletsa mzikiti, komwe kuti kulakwitsa. Enanso amaika zithunzi mmizikiti, zachipachikire kapenanso za kanthawi kochepa malinga ndi zochitika zomwe zikuchitika pa tsiku lina lake. Zimenezi ndi zolakwika.
Munthu pambuyo pa kuswali ma swalaat angapo wapeza kuti anali ndi najs, abweze swala zonsezo?
Munthu ngati wapeza najs pachovala chake pambuyo pa kuswali ma swalaat angapo, asabweze maswalaatiwo. Chimodzimodzi akanakhala kuti anadziwa kuti ali ndi najs asanaswali koma anaiwala kuti achotse mpaka waswali, asabweze swalatizo.
Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaswalitsa ma Swahaba tsiku lina atavala nsapato. Ndipo ali mkati mwa swalaat anadzavula nsapato zija. Ma Swahaba ataona kuti Mtumiki wavula nsapato, anavulanso zawo. Atamaliza kuswali, Mtumiki anawafunsa ma Swahaba chifukwa chimene anavulira nsapato zawo, ndipo anati “takuonani inu Mtumiki mutavula ndiye ife takutsatirani”. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Jibril anandifikira ndikundiuza kuti munsapatomu muli zoipa, choncho ndinavula…”
Mtumiki salla Allah alaih wasallam atadziwa kuti analowa ndi nyansi pa swalaat anachotsa ndikupitiriza swalaat, sanadukize nkuyambiranso, chifukwa sanali kudziwa kuti anali ndi nyansi.
Ndiye apa kwa munthu yemwe sanadziwe za najs yomwe wanyamula munsapato zake, mu trouser, kaya mumkanjo,,,mpaka waswali; swalat yakeyo ndi yolondola ndithu. Ndipo ngati wadziwa pamene ali mkati mwa swalaat, achotse najsiyo ngati zingatheke kuchotsa mosasokoneza swalaat ndikupitiriza swalaat. Koma ngati sakwanitsa kuchotsa, mwina najs ili mmalaya, adukize swalaatiyo ndikuchotsa najs kapena kusintha malayawo nkuyambira swalaat yake.
Kuchokeratu mu hadith imeneyi, taphunziranso umboni wina woti Mtumiki salla Allah alaih wasallam sanali kudziwa zobitsika. Allah Ta’la anamuuza kuti awauze anthu kuti iye sadziwa zobitsika:
قُل لاَّ أَقُولُ لَكُمْ عِندِي خَزَآئِنُ اللّهِ وَلا أَعْلَمُ الْغَيْبَ وَلا أَقُولُ لَكُمْ إِنِّي مَلَكٌ إِنْ أَتَّبِعُ إِلاَّ مَا يُوحَى إِلَيَّ
“Nena: “Ine sindikukuuzani kuti ndili nazo nkhokwe (za zabwino za Mulungu kotero kuti nkukupatsani chimene mwafuna). Ndipo (sindikukuuzani) kuti ndikudziwa zamseri, (za Mulungu kotero kuti nkukufotokozerani zomwe zingakufikeni pamalonda anu monga momwe mwafunira kuti ndikuuzeni.) Ndiponso sindikukuuzani kuti ine ndine mngelo (nkumandifunsa kuti, “Bwanji ukudya pomwe uli mngelo?”) Ine sinditsata china koma zomwe zikuvumbulutsidwa kwa ine…”
Mtumiki salla Allah alaih wasallam sankadziwa zobitsika, ndipo sangapereke mavuto kapena chithandizo kwa aliyense. Anamuuzatu Allah Ta’la kuti awauze anthu kuti:
قُلْ إِنِّي لَا أَمْلِكُ لَكُمْ ضَرّاً وَلَا رَشَداً –  قُلْ إِنِّي لَا أَمْلِكُ لَكُمْ ضَرّاً وَلَا رَشَداً
“Nena: “Ine ndilibe udindo wokupatsani mavuto kapena chilungamo (ndi zabwino).” Nena: “Ine palibe anganditeteze kuchilango cha Mulungu (ngati nditamnyoza) sindingapeze malo (othawira kuchilango chake) kupatula kwa Iye.”
Iye ndi munthu analengedwa ndi Mulungu ‘Azza wa Jalla … zimampeza zomwe zimawapeza anthu monga matenda, njala, ludzu, kutentha, kuzizira. kusangalala, kudandaula, ndi zina zonse, monga mmene ananenera mwini wake “ndithu ine ndi munthu ngati inu; ndimaiwala monga mmeen inu mumaiwalilira…”
Ndiye uthenga uwu upite kwa omwe amamupempha Mtumiki salla Allah alaih wasallam kuti awachotsere mavuto awo, awathandize, awapatse zovuna zawo…kumaganiza kuti Mtumiki amadziwa zobitsika. Allah Ta’la  akunena kuti:
قُل لَّا يَعْلَمُ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ الْغَيْبَ إِلَّا اللَّهُ
“Nena: “Palibe amene alipo kumwamba ndi pansi akudziwa zam’seri (zomwe zisanadze) Kupatula Mulungu basi.”
Choncho munthu yemwe ali ozindikira bwinobwino samapempha posakhala kwa Allah Ta’ala yekha ndipo sayezamira kupatula kwa Allah. Sapempha chithandizo ndi zina zonse kwa wina koma kwa Allah.
Posafuna kutalikitsa nkhani, tanena kuti yemwe sanadziwe kuti waswali ndi najs, swalat yakeyo ndi yolondola. Yemwe anadziwa kuti anali ndi najs koma anaiwala kuchotsa mpaka waswali, swalat yakeyo ndiyolondola.
Koma yemwe waswali opanda wudhu moiwala kapena mwadala, akuyenera kupanga wudhu ndikubweza swalaat. Chimodzimodzinso yemwe wadya nyama ya ngamira mosadziwa kut ndi nyama ya ngamira mpaka waswali ndikuzindikira kuti inali nyama ya ngamira pambuyo pa swalaat, akuyenera kupanga wudhu ndikubweza swalaatiyo chifukwa waswali opanda wudhu.
Apa tikutha kuona kusiya kwa pakati pa yemwe waswali ndi najs komanso yemwe waswali opanda wudhu
Munthu ngati wapezeka ali ndi Janaba ya kutulo ija, ndiye wadzuka asakudziwa kuti ali ndi janaba mpaka wapanga wudhu ndikuswal Al Fajr, kenako nkuzindikira kuti pa zovala zake pali janaba yomwe yachitika kutulo, akuyenera kusamba ndikubweza swalaat chifukwa waswali ndi janaba.
>Majmu’ Fatawa wa Rasaail Sheikh Ibn Uthaymin … >Fataawa Nurun ‘alaa Ddarbi