Kusintha dzina la bambo ndikutenga la mwamuna wake pambuyo pa kukwatiwa
Mkazi kusintha dzina labambo ake ndikutenga la munthu wina wake ndi kulakwa kwakulu.
Dzina la bambo limalongosola chibale cha kobadwira (lineage),, tsopano mkazi akasintha dzina la bambo ake ndikutenga la mwamuna wake, ndiye kuti  lineage yake waisintha pamenepo ndipo zikusonyeza kuti bambo ake tsopano ndi mwamuna wakeyo. Chifukwa dzina lako likatsatana ndi la munthu wina zimatanthauza kuti ndi bambo omwe anakubereka. Likatsatana ndi la bambo ako, zimatanthauza kuti ndi agogo ako. Izi ndizodziwika kwa aliyense chipembedzo chirichonse komanso pachikhalidwe cha anthu onse.
Tatiyeni tione chitsanzo izi: 
Mtsikana uyu ankatchedwa “Fatima mwana wa Muhammad” chifukwa choti amenewo ndi bambo ake.
Ndipo ngati angachotsepo “mwana wa…” ndikutsala “Fatima Muhammad”, zikutanthauza kuti Fatima ndi mwana wa Muhammad, chifukwa dzina lomwe labwera pambuyo pa dzina lamunthu popanda mlumikizi wolongosola chibale, ndiye kuti ndi la bambo ake.
Ndiye masiku ano tili ndi chizolowezi choti Fatima Muhammad akakwatiwa ndi Ali, akusintha dzina la bambo ake ndikuikapo la mwamuna wake, kukhala Fatimah Ali tsopano. Kapena asiya dzina la bambo ake pamalo pakepo, koma aonjezera la mwamuna wake kutsogoloko monga Fatima Muhammad Ali, kukhala ngati Ali ndi bambo a Muhammad tsopano.
Mkazi okwatiwa akhonza kugwiritsa ntchito maina onse pambuyo pa dzina lake (la bambo ake ndi la mwamuna wake) ngati angatchule ubale .. monga:
“Fatima mwana wa Muhammad mkazi wa Ali (Fatima bint Muhammad zawjatu Ali)”
kapena “Fatima Muhammad zaujatu Ali (Mrs. Ali)”
Koma osangoti “Fatima Muhammad Ali”. Imeneyo ndi mistake yomwe ambiri timachita, monga mukuonera pamenepo zikutanthauza kuti Fatima ndi mwana wa Muhammad, Muhammad ndi mwa wa Ali.
Ubale wa munthu umachokera kwa bambo, ndipo umayenda mu line ya azigogo ake malinga ndi mmene anabelekerana … mu chain chimenechi asapezeke wina oti sanaberekedwemo; lisapezeke dzina la mwamuna  wamkazi mu chain cha azibambo a mkazi. Mwamuna wakeyo ali ndi makolo ake, nayenso kumeneko kuli chain chomwe chikulumikiza azigogo ake, ndipo sangapezeke yemwe sanaberekedwe mu chain chimenecho.
Mwamuna ngati dzina lake liri Ali mwana wa Abu Talib, Abu Talib mwana wa Abdul Mutwalib, imeneyo ndi biological chain palibenso kulowetsa wina wapanja. Chimodzimodzi mkazi, ngati dzina lake liri Fatima mwana wa  Muhammad, Muhammad mwana wa Abdullah, likhale choncho osasinthanso, pasapezeke kuwachotsapo bambo ake ndikumulowetsa mwamuna wake .. pasapezeke kuwachotsa agogo nkumulowetsa mwamuna wake.
Kunena kuti Fatima Ali ndi mistake. Kunena kuti Fatima Muhammad Ali ndi mistake yaikulu Mchisilamu, chifukwa mwasandutsa Ali (husband) kukhala biological father (chifukwa biological father mwamchotsa pa malo ake). Kapenanso mwasandutsa Ali (husband) kukhala grandfather wa mkazi (chifukwa mwachotsa pa malo ake ndikuikapo mwamuna wanu.
Aliyense alemekeze ubale wakwawo, asasinthe chifukwa cha kukwatiwa. Kulemekeza banja kusafike podula ubale. Kudula ubale ndi tchimo lalikulu lofunika ochitayo alitalikire ndikupanga tawbah asanamwalire.
Munthu aliyense azidziwika ndi dzina la bambo ake omwe anamubala, kenako bambo a bambo ake, kenako azigogo … koma osati mwamuna wake. Mwamuna wakeyo sim’bale wake. Ana ake ndamene akuyenera atchulidwe dzina la mwamunayo chifukwa imeneyo ndi lineage yawo ,,,osati ya mkazi.
Kudula dzina la bambo mu lineage ya mkazi ndikumene kukupangitsanso kuti ubale wa mbali ya bambo usamadziwike, poti ana amangodziwa mai awo ndi bambo awo basi.
Zimenezi anadziyambitsa azungu omwe salemekeza mzimai,,, anabweretsa chikhulupiliro choti mkazi akakwatiwa ndiye kuti basi akhonza kumusintha mmene angafunire mpaka dzina la bambo ake kuchotsa. Izi tinatengera poti mzungu anatigula kalekale ndipo pano timadzigulitsa tokha potengera zikhalidwe zawo zopanda tanthauzo mu chikhalidwe ngakhale mu deen. Timaona ngati kupanda kutenga zikhalidwe za azungu tikutsalira, osadziwa kuti tikudzinyozetsa tokha.
Ena amanena kuti ngati anapereka mahar ali ndi ufulu kumusintha mkaziyo. Uku nkulakwitsa kwakukulunso, ndipo ndi umbuli, chifukwa mahar ndi swadaqa osati kulipira kapena kugula mkazi!!
Mtumiki salla Allah alaih wasallam anakwatira azimai angapo, ndipo mzimai aliyense ankatchulidwa dzina la bambo ake, palibe amene anasintha nkutchulidwa dzina la Mtumiki. Mtumiki anali ochokera ku banja lolemekezeka komanso iye ndi olemekezeka padziko, banja lake ndilolemekezeka kuposa mawanja onse, ndipo ndi banja limodzi lokhalo lomwe linadalitsidwa poti dziko lonse lapansi simadutsa 1 second osalipemphera zabwino:
“Allahumma swalli alaa Muhammad wa alaa aali Muhammad”
komatu azikazi ake sanatenge dzina lake nkusiya maina a bambo awo ngakhale kuti azibambo ena anali makafir… akazi a Maswahaba chimodzimodzi.
Lero azimai akuona kuti azimuna awo ndi olemekezeka kuposa azibambo awo,,, ndi olemekezeka kwambiri kuposa kulemekezeka kwa mwamuna wa akazi a Mtumiki sallaAllahalaihwasallam.
Chisakhalenso chikondi mpaka kusintha ubambo. Palibe mkazi yemwe amakonda mwamuna wake padziko pano kuposa momwe akazi a Mtumiki anali kumukondera mwamuna wawo …  koma sanatenge dzina lake nkusiya maina a abambo awo.
Komanso kodi mwamunayo akamwalira kapena banja likatha mkazi nkukwatiwa ndi wina, azingosinthabe dzina?
Werenganinso: