“ndipo akakufunsa akapolo anga za ine, ndithu ine ndili pafupi ndimayankha Dua ya opanga dua (kuitana kwa oitana)” 
Chisilamu chinalongosola ma condition/zofunika kuti kuti Dua iyankhidwe, komanso chinafotokoza zomwe zimaletsa kuti Dua iyankhidwe.
Komanso chinafotokoza myambo yofunika kutsatira pochita Dua komanso nthawi zomwe dua imayankhidwa mosavuta…
Tsopano Dua ikamapanda kuyankhidwa, zimachitika chifukwa cha kusowekera condition mma condition opangitsa kuti Dua iyankhidwe, kapena kupezeka zoletsa kuti Dua iyankhidwe.
Komanso zimatheka kuti iwe opempha ukufuna kuti Dua yako iyankhidwe mmene ukufunira osati mmene Allah akufunira…nchifukwa chake akunena mu Qur’an 2:216 kuti
كُتِبَ عَلَيْكُمُ الْقِتَالُ وَهُوَ كُرْهٌ لَّكُمْ وَعَسَى أَن تَكْرَهُواْ شَيْئاً وَهُوَ خَيْرٌ لَّكُمْ وَعَسَى أَن تُحِبُّواْ شَيْئاً وَهُوَ شَرٌّ لَّكُمْ وَاللّهُ يَعْلَمُ وَأَنتُمْ لاَ تَعْلَمُونَ
“Mwina mukhonza kuchida chinthu pomwe chili chabwino kwa inu, kapena kuchikonda cho the chomwe chili choipa kwa inu”
Choncho nthawi zina munthu amatha kupempha chinthu chomwe akuchiona kuti chimuthandiza, koma Allah akudziwa kuti chinthu chimenecho sichimuthandiza, kapena kuti chimuthandiza mukanthawi kochepa kwambiri ndipo kwinako ndi mavuto okhaokha…choncho Allah amatha kukupatsa chabwino kwambiri kuposa chomwe wapempha chija, koma chifukwa cha kusadziwa, munthu amayamba kudandaula kuti nchifukwa chani Allah sakundiyankha ma Dua, nchifukwa chani Allah akundipatsa zomwe sinnapemphe?
Tatiyeni tiwone chitsanzo cha kubadwa kwa Sayyidina Isa alaih Salaam (Yesu):
Mkazi wa Imran anapempha kwa Allah kuti ampatse mphatso ya mwana wamwamuna kuti akhale otumikira mnyumba ya Allah, koma Allah anamupatsa mwana wamkazi, osati wamwamuna monga mmene ankamufunira iye. Ndipo anamupatsa dzina loti Mariam.
Komatu mzimai anadandaula, ndipo zinali zochititsa manyazi ku banja limeneli.
Patadutsa zaka 12-14, mwana uja anabereka mwana wamwamuna nakhala Isa alaih Salam.
Taonani mmene Allah anayankhira Dua ya mkazi wa Imran…anaona kuti mwana wamwamuna yemwe akupemphedwa panopayu, nnthawi yake yoti adzapezekere sikuyenera kukhala inoyo, choncho uyu poti akupempha mwana, ndimdalitsa ndi mwana wamkazi yemwe adzabale mwana wamwamuna yemwe akumufuna pakalipanopayu, bdipo nthawi imene adzabadweyo idzakhala yoyenera komanso adzatumikira nyumba yanga ndikuwongola Ummah.
Choncho kuchokera mu chitsanzo chimenechi, tidziwe kuti Allah amayankha ma Dua onse, ndipo samabweza manja omwe akwezedwa pompempha, popanda kanthu. Koma yankholo limakhala malinga ndi zomwe munthu wapempha, malinga ndi mmene wapemphera, malinga ndi nthawi yomwe wapemphera, malinga ndi malo, komanso seriousness yako popemphapo monga kukhala ndi chitsimikizo komanso imaan, kugonjera kudzipereka kuti Allah akupatsa.
Komanso munthu adzipempha zomwe zilizoyeneradi kwa iye panthawiyo, osati kupempha zomwe iwe mwini palibe chomwe ukuchitapo,  kuti zingogwa kumwamba. Ngakhaletu mvula timapempha
Allah ndi olemera ndipo ali ndi china chirichonse komanso samapondereza munthu. Akunena mu Surat Al Baqarah 186
وَإِذَا سَأَلَكَ عِبَادِي عَنِّي فَإِنِّي قَرِيبٌ أُجِيبُ دَعْوَةَ الدَّاعِ إِذَا دَعَانِ فَلْيَسْتَجِيبُواْ لِي وَلْيُؤْمِنُواْ بِي لَعَلَّهُمْ يَرْشُدُونَ
“ndipo akakufunsa akapolo anga za ine, ndithu ine ndili pafupi ndimayankha Dua ya opanga dua (kuitana kwa oitana)” 
Komanso akunena mu Surat Yunus aayah 44 kuti
إِنَّ اللّهَ لاَ يَظْلِمُ النَّاسَ شَيْئاً وَلَـكِنَّ النَّاسَ أَنفُسَهُمْ يَظْلِمُونَ 
“ndithu Allah samapondereza chinthu kwa anthu, koma anthu amadzipondereza okha”
Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena mu Hadith yolemekezeka kuti *”Allah amamukwiyira munthu yemwe samamupempha iye”*
Zonsezi zikusonyeza kuti Allah samakana Dua ya kapolo wake ngati wakwaniritsa zonse zoyenera popempha kwa Iye.
Kwa ife ndikupempha … kuyankha tidzingomusiyira Mwini kudziwa nthawi yoyankhira. Chachikulu tidzionesetsa kuti tikudziwa zomwe tikupanga pomupempha Allah, osachita ngati tikupempha bambo athu.
Komanso tipemphe mmene tingathere osakaikira chifukwa kungokaikira kokhako kumaononganso njira ya Dua.
Kuchokera kwa Saeed AlKhudri radhia Allah anhu, Mtumiki Muhammad Salla Allah alaih wasallam anati
“Msilamu yemwe angapemphe popanda ntchimo lirilonse, komanso popanda kudula ubale, Allah amamuyankha kuzera mu imodzi nwa njira izi:”*
“Amamuyankha pompopompo”
“Amamusungira nkudzamupatsa zabwino zochuluka Tsiku Lomaliza”
“Kapena amamuchotsera zoipa zofanan ndi zomwe akupemphazo”. Anthu anati “tichulukitse”, iye anati “Allah achulukitsa”
kudziwa konse ndi kwa Allah
Allah atiteteze mu usiku umenewu.
Wassalam alaikum warahmatullah wabarakaatuh
wenganinso izi: Tawbah