KODI PALI DUA YOPEZERA MWAMUNA/MKAZI WABANJA?
Tidziwe kaye kuti dua ndi chani.
Imeneyi ndi ibaadah komanso njira imodzi yodziyandikitsira kwa Allah chifukwa munthu umadzionetsa kwa Iye kuti popanda Iyeyo sungakhale kanthu.
Ndiye munthu umapempha chilichonse poti mwini wake ananena kuti “ndipempheni ndipo ndikupatsani”.
Ma dua alipo omwe ananenedwa kuti tidzipanga in special times. Ma dua amenewa akupezeka mu Qur’an komanso mma Hadith,,,mwachidule ma dua onse omwe mukuwadziwa aja.
Koma pali ma dua ena omwe amapangidwa pofuna kuthandizidwa zofuna zako za nthawi imeneyo, ndipo ma dua amenewo sanalembedwe…koma Allah amawalandira.
Pali Hadith yoti Allah amakwiya ndi munthu yemwe sakumupempha. Chifukwa zimapezeka kuti wagwera mmavuto chifukwa cholekelera osamupempha Allah.  Monga banja,  chuma, ana ndi zina.
———
Banja ndi chinthu chofunikira kwambiri mmoyo wa munthu. Choncho munthu amayenera kupempha Allah kuti apeze munthu wodalirika kuti zonse zikhale zodalitsika komanso akhale osangala mmoyo wake.
Koma ngakhale palibe dua yokhayo yomwe inanenedwa ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam kapena mu Qur’an kuti munthu akamapanga apeza banja, munthu ukhonza kumapempha mmene umapemphera zina zonse,  kuti akupatse mwamuna/mkazi wabwino. Mukhonza kumapanga ma dua monga ma dua awa, omwe ma imaam ena anawavomerez:
اللهم زوجني رجلاً صالحا تقر به عيني وتقر بي عينه يا ذا الجلال والاكرام.
“Allahumma zawwijni rajulan swaalihan, tuqirru bihi aini wa tuqirru bii ainuhu, yaa dhal jalaal wal ikraam”.
Oh Allah ndikwatitseni mwamuna/mkazi wabwino oti akhale osangalatsa diso langa komanso ndingale osangalatsa diso ake, Oh inu amene muli Wamkulu komanso Olemekezeka”
———-
اللهم إنى أريد أن أتزوج فقدر لي من الرجال من هم اعف واحفظهم لي في نفسي ومالي وأوسعهم رزقاً واعظمهم بركة وقدر لي ولداً طيباً تجعل له خلقاً صالحاً في حياتي ومماتي.
“Allahumma inni ureedu an atazawwaja, faqaddir lii mina rrijaali man hum a’aff, wa ahfadhuhum lii fi nafsi wa maali, wa awsa’hum rizqan wa a’dhwamhum barakah, wa qaddir lii waladan twayyiban, taj’al lahu khalqan swaalihan fii hayaati wa mamaatii”.
“O Allah, ndithu ine ndikufuna ndikwatire, choncho ndipatseni mwamuna/mkazi yemwe ali odzisunga komanso oti andisunge ine ndi chuma changa,  mumudalitse ndi rizq komanso madalitso ochuluka.  Ndipatseni (kudzera mwa iyeyo) ana bwino,  akhale amakhalidwe bwino pamene ndili moyo komanso ndikadzamwalira”.
——–
Pali ma dua enanso ambirimbiri.
Chachikulu kuonesetsa kuti mukupanga nthawi yabwino yomwe dua imayankhidwa, monga after swala iliyonse, after adhan ndi iqaamah, during sajdah,  nthawi tahajjud ndi nthawi zina zambiri.
Usiku uli ndi hour imene Msilamu akaswali ma rakat awiri or more nkupempha zabwino, Allah amalandira directly. Choncho tahajjud ndi nthawi yabwino yopangira madua amenewa.
******
ALLAH ATIPANGE KUKHALA ODALIRA IYE PA ZOFUNA ZATHU KOMANSO OKHUTIRA PA ZOMWE WATIPATSA… Ameen