Kuchokera kwa Ibn Abbas radhia Allah anhu:

Mtumiki wa Allah (ﷺ) amatuluka mnyumba mwa mkazi wake, Juwayriyyah – dzina lake koyamba linali Barrah, koma anasintha – pamene Mtumiki anatuluka, Juwayriyyah anali pamalo opemphelera mpaka pamene anabwelera.

Mtumiki anamufunsa: kodi wakhala uli pamemphero osadukiza? Iye anati: Inde. Mtumiki anati: mmene ndimachoka ndayankhula mau atatu, ndipo utatu uwayeze pa scale ndiau onse omwe wakhala ukuyankhula panthawi imeneyo, mau ainewa alemera kwambiri kuposa akowo. (Ndayankhula kuti): “Subhaanallahi wa Bihamdih, ‘adada khalqihi wa ridhwaa nafsihi wa zinata ‘arshihi wa midaada kalimaatih”

Tanthauzo
“Watamandika Allah, ndikuyamba ndi kumuyamika pachiwerengero cha zolengedwa zake, komanso Chisangalalo chake chabwino, ndi kulemera kwa ‘Arsh (Kama) yake yaufumu ndi ink (kudzadza) kwa Mawu ake.”
Sunan Abi Dawud 1503

Shaddad bin Aus radhia Allahu anhu anati:

Mtumiki wa Allah (ﷺ) anati, “Dua yomwevili yabwino kwambiri popempha chikhululuko (Sayyedul Istighfaar) ndikunena kuti:
“‘Allahumma Anta Rabbi, la ilaha illa Anta, khalaqtani wa ana ‘abduka, wa ana ‘ala ‘ahdika wa wa’dika mastatwa’tu, a’udhu bika min sharri ma swana’tu, abu’u laka bini’matika ‘alayya, wa abu’u bidhanbi faghfir li, fa innahu la yaghfirudh-dhunuba illa Anta”.

Tanthauzo
“Ee Allah! Inu ndinubuye wanga. Palibe Mulungu woona kupatula inu. Munandilenga ine, ndipo ndine Kapolo wanu, ndipo ndagwiritsa pangano lanu mmene ndingathere. Ndikudzitchinjiriza mdi inu Kuchokera ku zoipa zomwe ndachita, Ndikutsimikizira maubwino omwe mwandininkha. Ndipo ndikuvomereza machimo anga. Ndikhululukireni ine poti palibe wina wokhululuka koma inu nokha.”

“Yemwe angapange dua imeneyi mwachitsimikizo masana, ndipo wamwalira kusanade, adzakhala mmodziwa a ku Jannah. Ndipo ngati mmodziwa inu anganene dua imeneyi ndichitsimilizo usiku mkumwalira kusanache, adzakhala mmodziwa anthu ali Jannah”.
[Al-Bukhari].