Anthu ambiri akamaliza swalah za faradh ndikumaliza kupanga ma Adhikaar, amanyamula manja awo ndikuyamba kupanga Dua pagulu kapena payekhapayekha aliyense. Ndipo pali gulu la anthu ena omwe samapanga, koma amati akamaliza kupanga ma adhkaar basi amatuluka, poti ma dua apanga mkati mwa swalaat pa sajda komanso kumapeto kwa swalaat asanapange salaam. Tatiyeni tione kuti kodi ndiziti zomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kuchita paziwiri zimenezi?

Ndatero chifukwa choti magulu onsewa akamapanga amati akutengera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, ndipo gulu lachitatu ndi laomwe sadziwa kalikonse, omwe amakhala akusokonezeka kuti atenge ziti, podziwa kuti yemwe anaphunzitsa mapempheredwe ndi mmodzi, Mtumiki ﷺ, yemwe zochita ndi zoyankhula zake sizinali kutsutsana.

Nzachidziwikire kuti Swalaat ndi ibaada yomwe imayambira Takbiratul Ihraam tili chiimire, ndipo imathera Salaam ziwiri tili chikhalire. Komanso palibe kutsutsana kulikonse pankhani ya kupanga ma adhkaar aliyense payekhapayekha pambuyo pa kupanga salaam ziwiri. Izi ndizomwe anali kupanga Mtumiki ﷺ komanso ma swahaba ake sanasinthe kalikonse.
Tsopano kumbali ya kupanga madua pambuyo pa ma adhkaar, pagulu kapena payekhapayekha, choyambilira tidziwe kuti palibe ibada yomwe munthu angachite kupatula yomwe inachokera kwa Allah Taala komanso anatiphunzitsa Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Ndipo anatiphunzitsa njira zopangira ibaada yonse yomwe anatilamula, choncho tisaonjezere kapena kupungula. Ndipo yemwe angabweretse njira ya mapangidwe a ibaada inayake posakhala yomwe anatiphunzitsa Mtumiki, adziwe kuti palibe chomwe chingalandiridwe kwa iye. Nchifukwa chake timanena kuti “Ibaada iliyonse ndiyoletsedwa kupatula ibaadah yomwe yabwera ndi umboni wosonyeza kuti inachokera mu Qura’an kapena mu Sunnah.”

Umboni wa ibaadah yomwe mu Qur’an ndi mu Sunnah mulibe, ndiwoti ibaada imeneyo ilibe umboni ndipo sikuyenera kuchitika.

Tikamafuna kupeza umboni wa ibaada inayake kapena umboni wamachitidwe a ibaada inayake, timayenera kupeza umboni wa kulamulidwa kapena kulolezedwea kwake, tisanapeze umboni wa kuletsedwa. Chifukwa ibaada inaletsedwa kale, kupatula yomwe inaikidwa kuti ndiyoyenera kuchitidwa, choncho tikamva ena akunena kuti tizipanga ibaada mwakutimwakuti, ife tisatsutse, koma tifunse komwe anazitenga, ndipo atchule mu Qur’an kapena mu Sunnah za Mtumiki kapenanso Khulafaa Raashideen ake, bola osawanamizira. Tikamva wina akuletsa, tisafunse umboni wakuletsako, koma tifufuze tokha umboni wakulolezedwa poti ndiumene ungapezeke pa ibaada.

Tsopano kupanga dua pagulu kapena payekhapayekha tikangopanga salaam pa swalaat ya faradh, omwe amachitawo sikuti anazitenga mu Sunnah ya Mtumiki ﷺ, sitinapeze umboni wolondola woti tsiku lina Mtumiki atamaliza swalaat ya Faradh ananyamula manyanja nkupanga dua. Izizi ndidzavomereza ngati pangapezeke umboni wake, in shaa Allah.

Kumbali ya swalaat, zochitika zonse za pa swalaat timazitenga kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam kuyambira pa mawu ake onena kuti

صلوا كما رأيتمني أصلي

“Pempherani ngati mmene mwandiwonera ine ndikupempherera”

Kumeneku kunali kuletsa kwa general, kubweretsa zinthu zomwe iye sanaphunzitse pa swalaat.

Choncho ndiudindo wanu ma Sheikh kuwaphunzitsa anthu machitidwe a Swalaat monga mmene Mtumiki ﷺ anali kuchitira, ndipo mukapanda kutero, kapena mukamawaphunzitsa zosemphana ndi chiphunzitso cha Mtumiki ﷺ, dziwani kuti mukulimbana ndi Mtumiki ﷺ, nkhondo yomwe simungapambane, Allah atipatse kulimba mitima pakufalitsa chilungamo.

Tatiyeni tione ndemanga za ma ulamaa olemekezeka, komanso odalirika, omwe ambiri amakhala akudana nawo chifukwa cha kukamba chilungamo kwawo. Uyu ndi Sheikh Shams Deen Abi ‘Abdillah Muhammad bun Abi Bakr Al-Zar’i Al-Dimashqiy, Ibun Al-Qayyim Al-Jawziya rahimahu Allah, yemwe anabadwa mchaka cha 691 pambuyo pa Msamuko, ndipo anamwalira mchaka cha 751 pambuyo pa Msamuko. Iye ananena mu buku lake lodziwika bwino komanso lodalirika, lotchedwa Zaadul Ma’aadi fi Hadyi Khayril ‘Ibaad, vol.1/249 kuti:

وأما الدعاء بعد السلام من الصلاة مستقبل القبلة أو المأمومين، فلم يكن ذلك من هديه (ﷺ) أصلا ولا روي عنه بإسناد الصحيح ولا حسن…

“Dua ya pambuyo pa salaam akamaliza swalaat atayang’ana ku Qiblah kapena kuwatembenukira anthu … sichinali chiphunzitso cha Mtumiki ﷺ ndipo zilibe chiyambi m’Chipembedzo komanso palibe Hadith ya Saheeh kapena hadith Hassan yokamba zimenezi.”
Akupitiriza mpaka pa page 250:

وأما تخصيص ذلك بصلاتي الفجر والعصر، فلم يفعل ذلك هو ولا أحد من خلفائه، ولا أرشد إليه أمته، وإنما هو استحسان رآه من رآه عوضا من السنة بعدها، والله أعلم. وعامة الأدعية المتعلقة بالصلاة إنما فعلها فيها، وأمر بها فيها، وهذا هو اللائق بحال المصلي، فإنه مقبل على ربه، يناجيه مادام في الصلاة، فإذا سلم منها، انقطعت تلك المناجات (لأن الصلاة تتنتهي إلى التسليمتين) وزال ذلك الموقف بين يديه والقرب منه، فكيف يترك سؤال في حال مناجاته والقرب منه، والإقبال عليه، ثم يسأله إذا انصرف عنه؟

“Ndipo Mtumiki ﷺ sanazipange zimenezi kukhala zochitika pa swalaat za Fajr ndi Asr, ngakhalenso ma Khalifa ake sanapange, komanso sanatsogolere kuti Ummah uzipanga. Koma kuti ndizomwe anaziona ena kuti ndizabwino kutero, posinthanitsa ndi ma Sunnah omwe amayenera kuchitika pambuyo pa Swalaat. Allah ndiye Mwini Kudziwa Konse.

Ma Dua onse omwe akuyenera kuchitika pa swalaat, ndiomwe Mtumiki ﷺ anali kuwachita ndipo analamula kuti tidziwachita. Ma Dua amenewatu ndiomwe amachitika pamene munthu ali mkati mwa Swalaat, osati atamaliza. Nthawi yonse yomwe munthu ali mu Swalaat amakhala kuti watembenukira kwa Mbuye wake, akulumikizana naye mwachifupi kwambiri moyenera ndi Swalaat yonse. Tsopano akangopanga Salaam ziwiri zija, pamenepo kulumikizana kotero kuja kumaduka (chifukwa swalaat imathera pa Salaam), ndipo kanthawi kameneka kuyandikirana naye kwambiri kuja kumachoka. Funso nkumati, munthu wina ndiye asiya bwanji kumupempha mukanthawi komwe ali ndi Mbuye wake chifupi kwambiri, kuisiya nthawi imeneyo kudikira kuti apange salaam, atalikirane naye, atembenukire kumbali kapena kuonetsa nkhongo Qibla, kenako nkuyamba kumupempha zofuna zake zomwe amalakalaka atamuyandikira pomupempha?”

Abale olemekezeka, tiyeni tikamva zomwe sitinazimvepo, tizikhala ndi mtima wofufuza kuona kwake, ngakhale zitakhala kuti zikuchokera kwa munthu yemwe sitimamukhulupilira, kapena yemwe timamkhulupilira. Chifukwa malamulowa sikuti agona mwaiyeyo, koma mu Qur’an ndi Sunnah ndipo munthuyo ndiwongofalitsa.

Chinenere Ibn Al-Qayyim kuti zonyamula manja nkumapanga Dua pambuyo popereka salaam pa swalaat ya faradh zilibe umboni komanso Mtumiki sanaphunzitse, kwabwera ma ulamaa ochuluka komanso ozindikira mwinanso kuposa Ibn Al-Qayyim, koma palibe ngakhale mmodzi yemwe anatsutsapo. Inu ndi ine lero lino, ilm yathu singafanane ndi ya ma Ulamaa amenewa, koma tili busy kuwatsutsa mopanda kufufuza kapena kubweretsa maumboni amtsutso wathu. Allah anatipatsa kuyankhula inde, koma tikugwiritse munjira yowongolera osati kusocheretsa.

Sheikh Muhammad bun Saalih Al-Uthaymin rahimahu Allah, omwenso ndimmodzi mwa ma Sheikh okhulupirika komanso anali olimbikira pa kuphunzitsa kudzera munjira ya Mtumiki ndi ma Sahaba ake ananena mu buku lawo la

الشرح الممتع,

vol.3/282 kuti:
رفع الأيدي بالدعاء بعد الفريضة ومسح الوجه بهما لا أصل له

“Kunyamula manja popanga dua pambuyo pa swalaat ya faradh ndikupukuta kunkhope zilibe chiyambi m’Chipembedzomu.

CHENJEZO:
Ma adhikaar, komanso ma Dua omwe amanenedwa mkati mwa ma adhkaar pambuyo pa swalah ya Faradh, amanenedwa popanda kunyamula manja, chifukwa choti Mtumiki ﷺ sanaphunzitse kutero, ndipo palibe umboni woti tsiku lina Mtumiki ﷺ ananena kuti:

اللهم أعني على ذكرك وشكرك وحسن عبادتك

atanyamula manja, palibe. Choncho ndibwino kutsata chiphunzitso cha Mtumiki ﷺ ndikusiya chikhalidwe ndi chizolowezi.

Kupanga dua kumapeto kwa swalaat mutanyamula manja, zimenezo sizili mmalamulo a Chisilamu, ndipo munthu ngati atafuna kupempha Allah (ﷻ) chinachake, apemphe ali mu swalaatimo, ndipo dua yanthawi imeneyo ikhoza kukhala yopambana kuposa kupanga atamaliza swalah. Ndibwino dua yako uziyipanga mkati kati mwa swalaat osati kumapeto ayi.
Umboni wa izi ukuchokera mu kuyankhula kwa Mtumiki ﷺ mmene ankamulongosolera Ibn Mas’ud za Tashahhud ponena kuti:

ثم ليتخير من المسألة ما شاء

“Kenako akhonza kuwonjezera kupempha zofuna zake. Hadith imeneyi ndiya saheeh ndipo ikupezeka mu Sahih Al-Bukhari #833.

Hadith imeneyi ikupereka chiphunzitso chokwanira kuti pa Tashahud ndimalo omwe munthu ungamapemphe zomwe ukufuna, amenewo ndiamodzi mwa malo opangirapo dua, osati swalaat ikatha.

Pomaliza, ndikupempha Allah kuti izi azipange kukhala njira yopangira ibaada molongosoka, koma ngati muli kulakwitsa kwinakwake, Iye akudziwa kuti sicholinga changa kulakwitsa. Kwa awo omwe akutha kuona zolakwika, ali ndi ufulu, komanso ndiudindo wawo kundikhonza, kuti tiwauze anthu zokhazo zomwe ndizolondola. الدين النصيحة Chipembedzo nkulangizana.