Wamva kale mmene Taloot anakumanira ndi asilikali a ku Palestine ndi gulu lake lochepa, ndipo asilikali ake ambiri anathawa ataona gulu la asilikali ambiri a Palestine.

Goliat anali mtsogoleri wa asilikali a Palestine ndip anali wamkulu thupi komanso wamphamvu. Iye anapita patsogolo ndikumutchalenja Taloot kuti atulutse msilikali yemwe angamenyane naye.

Mwambo wa nkhondo nthawi yakale unali woti mmodzi wa Asilikali a magulu awiri amamenyana mmalo mwa onse.

Taloot anafunsa asilikali ake ngati angapezeke yemwe angamenyane ndi Goliat, koma aliyense anaopa kupita. Taloot analonjeza kuti akwatitsa mwana wake wamkazi kwa yemwe angalowe m’bwalo. Koma palibe yemwe anapita. Izi zinamukwiyitsa Taloot poti anadziwa kuti asilikali ake anali kuopa kumenyana ndi Goliat.

Mnyamata wina anatuluka mgulu lija ndikupita kutsogolo ndipo anati amenyana ndi Goliat. Asilikali onse anamuseka chifukwa chakuchepa kwake ndipo anaganiza kuti sangakwanitse. Mnyamatayutu anali Dawud alaih salaam ochokera mumzinda wa Bethlehem. Abale ake anali asilikali ndipo iye anali wamng’ono kwambiri. Bambo ake anangomutumiza ku nkhondo kuja ncholinga choti adzikasunga zochitika za pankhondo, ndipo anamulangiza kuti asakalowelere nkhondo iliyonse.

Taloot anamuuza Dawud kuti anali okondwa ndi kudzipereka kwake, koma sakukwanira kumenyana ndi Goliat, koma iye anakakamira kuti akwanitsa; anamuwuza Taloot kuti usiku wapitawo anapha mkango womwe unasokoneza bambo ake tulo, komanso anapha chinyama cholusa, choncho asamuweruze ndi maonekedwe ake. Pamenepo Taloot anadabwa ndi kuchangamuka kwa mnyamata uja ndipo anawauza asilikali kuti ngati akhonzeka kumenya nkhondo, Allah awateteze. Ndipo anawauza  kuti amupatse Dawud chovala ndi nthungo zomenyera nkhondo, koma poti iye sanazolowere kuvala zimenezo, anawabwezera. Anayamba kutoleza timiyala nkumaika mchikwama chake. Taloot atamufunsa kuti akwanitsa bwanji kudziteteza ndi myala imeneyo, iye anayankha kuti Allah yemwe anamuteteza ku mkango amutetezanso pa nkhondoyo.

Atayamba kupita kutsogolo kuti akakumane ndi Goliat, anthu anapitiriza kumuseka. Goliat anamuopseza kuti amuduladula ndi lupanga lake, koma iye anamuuza kuti ngakhale atakhala ndi lupanga, iye amenya nkhondo mu dzina la Allah. Kenako Dawud alaih salaam anavunga mwala umene unafikira pachipumi cha Goliat ndipo nthawi yomweyo anagwa pansi asanapeze mwayi wobwezera.

Pamene mtsogoleri wawo anaphedwa ndi mwala wa Dawud, asilikali a Palestine anayamba kuthawira kumapiri. Taloot ndi asilikali onse sanakhulupilire mmene anawinira nkhondoyi. Kuyambira pamenepo, kuvutitsidwa konse mmanja mwa ma Palestines kunatha.

Asilikali anamunyamula Dawud pobwelera kwawo. Iye anasanduka kukhala olemekezeka nthawi imodzi. Talot monga mwa lonjezo lake, anampatsa Dawud mwana wake kuti amukwatire, ndipo anamusankha kukhala mmodzi mwa alangizi ake.

Dawud alaih salaam anali otchuka pakati pa ma Israel, koma kutchukako sikunampangitse kukhala kapolo wadziko; anapitilira kukhala kapolo wa Allah moti sanapite kukasangalalira kupambana kwake, koma anapita kuchipululu kukamulambira Allah.

Dawud alaih salaam anali ndi mau okongola kotero amati akayamba kupanga dhikr, mbalame, zomera ngakhale mapiri zinali kupanga naye. Allah anampanga Dawud kukhala Mtumiki ndipo anamusitsira buku la Zabur. Pamene Dawud anali kuwerenga malemba a m’bukulo, mapiri anali kuwerenga naye ndipo mbalame zinali kuvina. Allah anamudalitsanso Dawud alaih salaam ndi kumva zilankhulo za zinyama ndi mbalame.

Dawud alaih salaam anali kusala tsiku limodzi pambuyo pa tsiku lina, komanso anali kupemphera chigawo cha usiku akadzuka.

Munthawi ya Utumiki wake mumachitika nkhondo zambiri ndipo anali kuwina zonse. Anthu anamukonda Dawud ndikumuyamikira kwambiri mpaka Taloot anayamba kuchita nsanje poti anthu anli kumuyamikira kwambiri kuposa iye. Dawud anazindikira kuti zinthu sizikuyenda bwino ndipo anamufunsa mkazi wake yemwe sanali kumubisira zinthu. Iye anayankha kuti bambo ake akumuchitira nsanje ndipo akuopa kuti sakhonza kuluza ufumu wake chifukwa cha iye Dawud. Anamuuzanso kuti bambo ake akupanga plan yoipa kwa iye ndipo akuyenera kukhala watcheru nthawi zonse.

Tsiku lina Taloot anamuitana Dawud ndikumuuza kuti Canan yatumiza asilikali kuti adzathire nkhondo Israel, choncho iye akuyenera kutenga asilikali ake ndipo asakabwelereko popanda kuwina nkhondoyo. Apa Dawud anadziwa kuti imeneyo inali plan yofuna kuthana naye, ngakhale anali kudziwa kuti Canan inali ndi asilikal ambiri ndi amphamvu, anavomerabe kuti akamenyana nawo.

Dawud anamenya nkhondo ija kwa masiku angapo ndipo Allah anamuthandiza ndikuwina. Taloot anali ndi chiyembekezo choti Dawud ndi asilikali ake sangawine nkhondoyo ndipo kumeneko kukhala kutha kwake. Koma ataona mmene ma Israel anali kuchitira pomuyamikira Dawud, anadziwa kuti zolinga zake zalephereka ndipo mantha anaonjezereka.

Usiku wina Taloot anamuitana msilikali wake odalirika ndikugwirizana naye kuti amuchite chiwembu Dawud pomupha usiku womwewo. Koma mkazi wa Dawud anamvetsera kukambirana kuja ndipo anathamanga kukamuuza mwamuna wake kuti asamuke usiku womwewo.

Pamene Talot anadzadzidwa ndi nsanje kumuchitira Dawud, sanasamalenso za mwana wake yemwe anali mkazi wa Dawud.

  Gawo lachiwiri likubwera in sha Allah