Anthu ena amaganiza kuti Da’wah (kuitanira kwa Allah) palibe yemwe angapange kupatula ma ulamaa okhaokha, ndipo omwe akuphunzira kwa ma Ulamaawo sakukakamizidwa kupanga Da’wah. Mutithandiza bwanji pa zimenezi? 
 
Sikuti ndi maganizo chabe, koma ndizoona. Da’wah sangapange munthu aliyense kupatula yemwe ali ozindikira. Tiyeni tione pawiri malinga ndi mmene kufunikira kwa Da’wah kuliri. Pali zinthu zina zomwe amazidziwa aliyense, ndipo akuyenera kuchita da’wah pa zinthu zoterozo osati ma Sheikh okha. Munthu aliyense akuyenera kulamula zabwino ndikuletsa zoipa malinga ndi mmene akudziwira zinthuzo. Mwachitsanzo kumulamula mkazi wako ndi ana kuti adziswali, sizikufunika kuti ukhale Sheikh. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
“Alamuleni ana anu kuswali pamene akwanitsa zaka 7 (zakubadwa), ndipo muwameneye (powakakamiza) akakwana zaka 10” Sahih Sunan Abi Dawud (495).
Ananenanso kuti:
“Aliyense mwainu ndi m’busa (muyang’aniri) ndipo m’busa aliyense adzafunsidwa za ubusa wake (udindo wake woyan’ganira)” Sahih Al Bukhari (853)
Ntchito ya uyang’aniri ndiko kulamula zabwino ndikuletsa zoipa. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
“Yemwe waona choipa mwainu achotse ndi dzanja lake, akapanda kukwanitsa (achotse) ndi lirime lake, akapanda kukwanitsa (achotse) ndi mtima wake” Sahih Muslim.
Choncho yemwe sakudziwa (alibe ‘ilm, si Sheikh), ali ndi udindo wa kutsogolera banja lake komanso anthu ena kuntchito zabwino monga swalaat, zakaat, kutsatira malamulo a Allah, kutalikira machimo komanso kuyeretsa mtima ku machimo, adzileranso ana ake munjira ya kutsatira Allah. Zimenezi ndiye zofunika kwa iye ngati ali osaphunzira poti zimenezi ndi zodziwika kwa liyense.
Pomwe fatuwa, kulongosola kuti izi ndi halal ndipo izo ndi haram, kulongosola za Tawheed ndi Shirk; zimenezo sakuyenera kuchita aliyense kupatula ma Ulamaa, anthu omwe anaphunzira bwinobwino za malamulo a Chisilamu.
الأجوبة المفيدة عن أسئلة المناهج الجديدة
س10 ص40