Zipembedzo zitatuzi zili ndi chikhulupiliro chosagwedezeka pa kufunikira kwa ukwati ndi banja. Ndipo zimavomerezana pa utsogoleri wa mwamuna pa banja. Komabe, pali kusiyana kwakukulu pakati pa zipembedzozi, pa malire a utsogoleri umenewu. Chikhalidwe cha Chiyuda ndi Chikhristu, mosemphana ndi Chisilamu, zimawonjezera utsogoleri wa mwamuna kukhala umwini pa mkazi wake.

Chikhalidwe cha Chiyuda pa udindo wa mwamuna kwa mkazi wake chimachokera pa kunena kuti iye ndi mwini wa mkazi wake monga momwe akhalira mwini kapolo. 19 Maganizo amenewa ndi omwe akubweretsa malamulo a chigololo aja komanso kulepheretsa malumbiro a mkazi wake. Chimodzimodzinso kuchokera mmaganizo amenewa, mkazi saloledwa kulamulira pa katundu wake kapena zopeza zake. Mkazi wa Chiyuda akangokwatiwa, amalandidwa katundu wake.

Atsogoleri a Chiyuda adalangiza kuti mwamuna ali ndi ufulu wokhala ndi chuma cha mkazi wake monga momwe amachitira cha iye mwini: “Popeza kuti munthu watenga mkazi kukhala wake, akuyenera kutenganso chuma chake chonse kukhala chake”, komanso “Popeza iye adapeza mkaziyo, akuyenera kupezanso katundu wake”. 20

Motero, ukwati unali kupangitsa mkazi wolemera kukhala wosauka. Talmud imafotokoza zachuma cha mkazi motere:

“Kodi mkazi angakhale bwanji ndi zinthu? Chilichonse chomwe mkazi ali nacho ndi cha mwamuna wake. Chuma cha mwamuna ndi chake mwamunayo, ndipo chuma cha mkazi ndi cha mwamunayonso… zomwe angapeze kapena kutola m’misewu ndi za mwamuna wake. Ziwiya za mnyumba, ngakhale zinyenyeswa za mkate pa tebulo, ndi zamwamuna wake. Mkazi akaitanira mlendo kunyumba kwake ndi kumudyetsa, ndiye kuti wamubera mwamuna wake …”(San. 71a, Git 62a)

Chowona chake ndi chakuti katundu wa mkazi wa Chiyuda (yemwe sanakwatiwe) ankagwiritsidwa ntchito ngati chokopera amuna basi. Banja lachiyuda limapatsa mwana wawo wamkazi gawo la chuma cha bambo ake kuti agwiritse ntchito ngati chiwongo akamafuna kukwatiwa. Chiwongo choterechi ndichimene chinkapangitsa makolo a ana aakazi kukhala ndi nkhawaa. Bambo anali kulera mwana wake kwa zaka zochuluka ndikukonzekera ukwati wake popereka chiwongo chochuluka. Motero, mtsikana wa m’banja la Chiyuda anali chipsinjo chopanda phindu kwa bambo ake. 21

Kupanda phindu kumeneku kukumasulira chifukwa chimene chinkachititsa kuti kubadwa kwa mwana wamkazi kukhale kosakondweretsa mu Chiyuda (onani gawo la “Ana Achikazi Ngochititsa Manyazi”). Chiwongo chinali mphatso yaukwati yomwe imapatsidwa kwa mkwati mwalamulo. Mwamuna amatha kukhala mwini wa chiwongo, koma sanali oyenera kuchigulitsa. Mkwatibwi amakhala opanda  ulamuliro uliwonse pa chiwongo pa nthawi ya ukwati. Komanso, anali kuyembekezeka kugwira ntchito pambuyo pa ukwati ndipo malipiro ake onse amayenera kupita kwa mwamuna wake. Iye sankapezanso chuma chake kupatula mu njira ziwiri izi: kumwalira kwa mwamuna, kapena kutha kwa banja.  Ngati mkazi angamwalire moyambilira, mwamuna amatenga chuma chake chonse, ndipo ngati wayambilira kumwalira mwamuna, mkazi amaloledwa kutenga chuma chake chokha koma samaloledwa kutenga cha mwamuna wake.  Tidziwenso kuti mkwati nayenso amayenera kupereka mphatso yaukwati kwa mkwatibwi, komabe iye anali mwiniwake wa mphatsoyo malinga ngati akwatirana. 22

Chikhristu mpaka posachedwapa, chakhala chikutsatira mwambo womwewo wa Chiyuda. Akuluakulu achipembedzo ndi akuluakulu a boma mu Ufumu wa Chiroma wa Chikhristu (pambuyo pa Constantine) adali kufunsa mgwirizano pa katundu kuti chikhale chotsimikizira ukwatiwo. Mawanja anali kupereka chiwongo chochuluka, zomwe zinali kupangitsa kuti amuna akwatire mofulumira, pomwe makolo anali kuimitsa maukwati a ana awo akazi mpaka kudutsa nthawi, mosemphana ndi chikhalidwe. 23

Malinga ndi lamulo la Canon, mkazi anali ndi ufulu wotenga chiwongo chake ngati ukwati walephereka, kupatula ngati chifukwa chake chinali kupezeka ndi chiwerewere – pamenepo sanali kupatsidwa kalikonse. 24 Kuchokera mu malamulo a Canon amenewa, akazi okwatiwa mmaiko a ku Europe ndi America akhala akulandidwa ufulu wawo pa katundu kufikira mu zaka za mma 18th ndi 19th century.

Mwachitsanzo, ufulu wa amayi mmalamulo a Chingerezi unalembedwa ndikutsindikizidwa mu 1632, monga: “Zomwe mwamuna ali nazo ndi zake. Zomwe mkazi ali nazo ndi za mwamuna wake.” 25 Mkaziyo sanali kulandidwa chuma chokha, koma analinso kulandidwa umunthu wake. Chochita chake chirichonse chinalibe mphamvu iriyonse mmalamulo. Mwamuna wake amatha kukana malonda aliwonse kapena mphatso yomwe wapeza mkazi, kuti zilibe phindu. Munthu yemwe angapange naye mgwirizano uliwonse, anali kutengedwa kuti ndi chigawenga poti wachita chinyengo. 26 Komanso mkazi sanali kuloledwa kusuma kapena wina kusuma mu dzina lake, ndipo sanali kumveredwa ndi mwamuna wake. Mkazi wokwatiwa anali kuwonedwa ngati khanda mmalamulo. Mkazi akangokhala wa mwamuna wake basi, ndipo anali kulandidwa katundu wake, mphamvu yake pa malamulo, ndi dzina lake la kubanja. 27

Chisilamu, kuyambira mzaka za mma 7th century, chinapereka ufulu kwa akazi okwatiwa kukhala odziimira pawokha, ufulu womwe Ayuda ndi Akhristu anawalanda mpaka posachedwapa. Mu Chisilamu, mkwatibwi ndi banja lake sakuyenera kupereka chiwongo chamtundu uliwonse kwa mkwati. Msungwana wa m’banja la Chisilamu sali chipsinjo kubanja lake. Chisilamu chinamulemekeza mkazi kwambiri kotero kuti safunikira kupereka mphatso iriyonse kuti akope mwamuna yemwe akufuna kukwatiwa naye. Ndi mkwati amene ayenera kupereka mphatso ya ukwati kwa mkwatibwi. Mphatso imeneyi ndi chuma chake mkaziyo, ndipo mkwati kapena akubanja la mkwatibwi alibe gawo kapena ulamuliro uliwonse pa chumacho. Mmadera ena a Asilamu masiku ano, mphatso yaukwati yokwana madola zana limodzi ($1000) siyachilendo. Mkwatibwi amasungira mphatso zake zaukwati ngakhale atasudzulana pambuyo pake, ndipo mwamuna saloledwa gawo lililonse mu chuma cha mkazi wake kupatula chimene amamupatsa ndi chilolezo chake chaulere. 29

Qur’an yanena nkhaniyi momveka bwino:

Qur’an 4:4: “Ndipo akazi apatseni mahari awo (chiwongo) monga mphatso. Koma (akazi anuwo) ngati atakupatsani mokoma mtima chilichonse (mchiwongocho), idyani mokondwa ndi mothandizika nacho.”

Zomwe mkazi wake ali nazo komanso malipiro ake onse, zimakhala mmanja mwake chifukwa cha udindo wake womwe iye akuyenera kukwaniritsa pa ana ndi mwamuna wake. Ngakhale mkazi atakhala olemera chotani, sakukakamizidwa kukhala wothandizana nawo pabanja (popeza zosowa za pabanjapo) pokhapokha atazipangira yekha mwa kufuna kwake. Mkwati ndi mkwatibwi amatenga chuma kuchokera kwa mzake (ngati wamwalira mwamuna, mkazi atenga chuma chosiyidwacho, ndipo ngati wamwalira mkazi, mwamuna atenga chuma chosiyidwacho). Komanso, mkazi wokwatiwa Mchisilamu amadziwika ndi umunthu wake wodziimira payekha komanso dzina la kubanja komwe achokera silimachotsedwa. 30 Judge (woweruza) wina wa ku America adakambapo za ufulu wa akazi a Chisilamu kuti: “Mtsikana wa Chisilamu akhoza kukwatira kangapo, koma umunthu wake sungasungunuke ndi azimuna ake. Iye payekha ndi wodziimira, umunthu wake pamalamulo, dzina la kubanja kwake, komanso chuma chake.” 31

Kusudzulana