Chiyambi chenicheni cha Ijtimaa’ Padziko Lonse

Ijtimaa’ inayambitsidwa mchaka cha 1944 ndi gulu la Jamaat Tablighi, jamaat yomwe inayambitsidwa ndi Sheikh Muhammad Ilyas Al-Kandhlawi. Ijtimaa’ inayamba ngati gawo limodzi lofunikra mu zochitika za Jamaat Tablighi padziko lonse, chifukwa “imathandiza miyoyo ya Asilamu ngakhalenso anthu ena omwe amapezeka pa kusonkhanako”.

Dzina loyambilira linali Tablighi Ijtema (تبليغي اجتماع) Ndipo dzina lina ndi Aalmi Ijtema (عالم اجتماع) {ikakhala yokhonzedwa dziko lonse}.

Anthuwa anayamba ngati kagulu ka anthu ochepa omwe anali ozindikira, ndikumasonkhana mumzikiti.

Pa zaka zokwana 40, malo otchedwa ‘Tongi’ anali malo omwe anasankhidwa kuti Asilamu azisonkhana.

Iwo adayambitsa Ijtimayi mu ndondomeko yoti.

1- idzikhala pa chaka chilichonse.

2- masiku ake akhale atatu.

Pomaliza pake amakhala akutumiza magulu mmalo osiyanasiyana kukalalikira za deen ndi zomuwopa Allah.

Omwe amayendetsa pa chaka ndi a Jamaat Tablighi, mabungwe komanso ma madrasa. Ijtimaa’ imeneyi imachitika masiku atatu pa chaka chirichonse malinga ndi mmene a TJ (Tablighi Jamaat) anakhonzera mu ndondomeko zawo. Ndipo imachitika kwambiri mmaiko aku Asia makamakama anzathu a Chimwenye, komanso maiko ena a Chisilamu.

Chiyambi cha Ijtimaa ku Malawi

Kuchokera mu zokambirana zomwe zidachitika pakati pa ma Sheikh okwana 20, anagwirizana kuti Ijtimaa yomwe imachitika pa chaka si mwambo wovomerezeka mChisilamu, koma ndi mwambo wopeka (bid’ah).

Kukambiranaku kusanayambike, mmodzi mwa ma Sheikh analongosola mbiri ya Ijtimaa ku Malawi motere:

Ijtimaa ndi nsonkhano womwe Aslamu amachita pa chaka kamodzi, ndipo umatenga masiku atatu kuyasmbira Lachisanu pakutha pa swalaat ya Jum’ah mpaka Lamulungu kummawa.

Mlendo olemekezeka wake amakhala mmodzi mwa anthu odziwika bwino pa ndale kapena mkulu wa boma, monga mtsogoleri wadziko, nduna kapena wandale otchuka aliyense posayang’ana za chipembezo chake; bola akhale wotchuka mu ndalemo.

Pokonzekera mwambowu, komiti yopanga madongosolo onse a za mwambowu imasankhidwa. Komiti imeneyi ndiyomwenso imagwira ntchito yopempha chithandizo mmabungwe a Chisilamu komanso ku Boma. Kumapeto kwa mwambo wonse, komitiyi imapeza mwayi wogawana ndalama zomwe zatsalira pamwambowu.

Mwambowu umakhala ndi mutu womwe ma Sheikh osiyanasiyana amakhala akulalikira ku anthu amene abwera pa malopa.

Ijtima poyambilira itabwera ndi Amwenye idakanidwa chifukwa choti anali a Tablighi, koma ma Sheikh a chikuda atabweretsa Ijtimayi kuchokera ku Tanzania, ayi ndithu idatengedwa nkuitsatira mopanda kusintha kulikonse kosemphana ndi Amwenye, monga kuchita masiku atatu, pachaka, komanso kuyamba Lachisanu pambuyo pa Jum’ah ndikutha Lamulung kummawa.

Komwe inayambira Ijtima’ko, a Tablighi anaipanga kukhala ya azibambo okha, iwo ndamene amaloledwa kupita ku Ijtimaa monga momwe salolera azimai kuyenda Tablighi. Koma kuno kwathu Ijtima imeneyi poyambilira inkachitika pamodzi azibambo ndi azimai, potengera ku Tanzania; chifukwa kumeneko amapangira pamodzi amuna ndi akazi omwe. Nchifukwa chake Ijtima ya 2012 ku stadium ya ku Blantyre anzathu aku Tanzania adaitanidwa ndipo adabwera ndi azimayi awo omwe.

Ma Sheikh a ku Malawi kuno ataona zoipa zomwe zimachitika ku Ijtimaa chifukwa cha mchitidwe wophatikizanawu, Alhamdulillah adaika chiganizo choti azimai asamapite ku Ijtima ya azibambo, koma azibambo ali ololedwa kupita ku Ijtima ya azimayi. Ndipo patadutsa kanthawi Azimai adayamba kupanga Ijtimaa yapawokha.

Ref:

  • Ijtema as a New Islamic Pilgrimage – Bulbul Siddiqi
  • The Biswa Ijtema– Nina Björkman
  • Biography of Maulana Iliyas– Maulana Abul Hasan Ali Nadvi
  • Zokambirana za ma Sheikh 20 a ku Malawi

Pomaliza, Ijtimaa’ simwambo wochokera mu Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam, komanso si mtundu uliwonse wa mapemphero Mchisilamu.