Chiwerewere ndi tchimo muzipembedzo zonse. Baibulo linaika chilango cha imfa kwa wachiwerewere wamwamuna ndi wamkazi (Levitiko 20:10).

Chisilamu chimalanganso chimodzimodzi wachiwerewere wa mwamuna ndi wamkazi (24: 2).

Komatu ngakhale zili choncho, tanthauzo la chiwerewere mu Qur’an nlosiyana kwambiri ndi tanthauzo la mu Baibulo; Malinga ndi Qur’an, chiwerewere ndi kupezeka kwa mwamuna wokwatira kapena mkazi wokwatira pazochitika za osakwatira (kugonana).

Pomwe Baibulo limangowelengera chiwerewere cha mkazi wokwatiwa ndi mwamuna osakwatira kuti ndi chiwerewere (Levitiko 20:10, Deut 22:22, Miyambo 6: 20-7: 27).

“Mwamuna akapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake, mwamuna ndi mkaziyo, onsewo afere pamodzi. Motero uzichotsa oipawo mu Isiraeli.” (Deut 22:22).

“Munthu wochita chigololo ndi mkazi wa munthu wina, wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Mwamuna ndi mkazi amene achita chigololowo aziphedwa ndithu.” (Levitiko 20:10).

Malinga ndi tanthawuzo la m’Baibulo, ngati mwamuna wokwatira agona ndi mkazi wosakwatiwa, sipakhala kulakwika kulikonse. Mwamuna wokwatira yemwe wachita chiwerewere ndi mkazi wosakwatiwa, onsewo sawerengedwa kuti achita chiwerewere. Tchimo la chiwerewere limapezeka pamene mwamuna okwatira kaya osakwatira, wagona ndi mkazi wokwatiwa. Pamenepo mwamuna amakhala kuti wachita chiwerewere, ngakhale atakhala kuti ndiwosakwatira, ndipo mkaziyo amakhala kuti wachita chiwerewere. Mwachidule, chiwerewere ndi mchitidwe uliwonse wakugonana kumene kungachitike ndi mkazi wokwatiwa. Ndipo kwa mwamuna wokwatira sichiwerengedwa kuti ndi tchimo la chiwerewere, malinga ndi Baibulo.

Kodi nchifukwa chani izi zili choncho? Malingana ndi Encyclopaedia Judaica, mkazi amatengedwa kuti ali pansi pa mwamuna wake kumbali zonse za moyo wake, ndipo chiwerewere chomwe angachite mkaziyo, kumakhala kumulakwira mwamuna yekhayo, pomwe akachita mwamuna, sakhala kuti walakwira mkazi wake poti sali pansi pa ulamuliro wake. 15 Izi zikutanthauza kuti ngati mwamuna agonana ndi mkazi wokwatiwa, ndiye kuti wamuchita chinyengo mwamuna mzake (mwini mkazi yemwe wagonana nayeyo), kotero ayenera kulangidwa pachifukwa chimenecho basi, osati chifukwa chakuti wamuchita chinyengo mkazi wake.

Kufikira lero lino mu Israeli, ngati mwamuna wokwatira wachita chibwenzi ndikugonana ndi mkazi wosakwatiwa ndikubereka ana mmenemo, ana amenewo amakhala ovomerezeka (si apathengo), poti mkazi anali osakwatiwa. Koma, ngati mkazi wokwatiwa wachita chibwenzi ndi mwamuna wina, kaya wokwatira kapena wosakwatira, mpaka wabereka ana mu chibwenzimo, anawo samangokhala apathengo chabe, koma amakhalanso oipa (bastards), ndipo akakula samaloledwa kukwatira akazi a Chiyuda, koma ma bastard anzawo kapena obwera kuchokera maiko ena.  Kuletsedwa kumeneku kumaitilira kwa anawo, komanso ana awo, zidzukulu zawo, kufikira mibadwo khumi (10) yakutsogolo kwawo, mpaka tchimo la chiwerewere cha azigogo awo lija lidzafowoke. 16

Koma Qur’an ikufotokoza momveka bwino ubale wa pakati pa mkazi ndi mwamuna omwe ali pabanja motere:

Qur’an 30:21: “Ndipo zina mwazizindikiro zake (zosonyeza chifundo chake kwa inu) ndiko kukulengerani akazi a mtundu wanu kuti mukhazikike (mitima yanu) kwa iwo, ndipo adaika pakati panu chikondi ndi chisoni. Ndithu, mzimenezi muli zizindikiro kwa anthu amene amalingalira.”

Ichi ndi chiphunzitso cha Qur’an pa banja: chikondi, chifundo, ndi bata, osati kukhala ndi zikhalidwe ziwiri.

Malumbiro