Swalat ya Jum’ah simaswalidwa ngati anthu sanakwane jamaah (gulu). Koma ma chicfukwa cha kusapezeka umboni wochokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam osonyeza chiwelegero chenicheni cha anthu omwe akukwanira kupanga jamaah, ma ulamaa pambuyo popanga ijtihaad yawo anasiyana zoyankhula. 
 
Imaam Al Shaafi’ ndi Ahmad bun Hanbali anapeza kuti Jum’ah imakwanira kuyambira anthu achimuna 40. Ndipo ngati anthu alipo 40 akuyenera kumaliza onsewo swalat ya Jum’ah popanda kupunguka. Nailul Awtwaar vol 6/248. 
Ndipo Madh’hab a Imaam Abu Hanifa anapeza kuti Jum’ah imakwanira kuyambira anthu achimuna atatu (awiri otsatira ndipo mmodzi imaam) ngakhale atakhala a paulendo kapena kudwala, chifukwa jamaah pachirichonse imayambira pa anthu atatu, ndipo Jmaah ndi lamulo lofunikira pa Jum’ah. Ndipo madh’hab a Maalik anati akuyenera kukwana anthu 12 osawelengera imaam komanso asakhale a paulendo kapena kudwala, akhale anthu a pamudzi okwaniritsa chiwelengero chimenecho, osati a paulendo kapena odzapanga malonda mumsika, komnanso amalizire limodzi ndi imaam, ndipo ngati chiwelengero chilipo ndendende 12, ndipo mmodzi wa iwo swalat yake yaonongeka, ndiye kutiu jumah yonse mumzikiti umenewo yaonongeka chifukwa choti chiwelengero chapunguka
Pankhani imeneyi ma imaam anasiyanapo ndipo zokamba zilipo zambiri pafupifupi 15, koma maganizo omwe ali otchuka omwe ambiri amatengera ndi amenewo. 
Ma imaam ena monga Sheikhul Islam ibn Taimiya anasankha zoti Jum’ah athu atatu imakwanira kukhala jama’ah, ndipo izi ndizomwe ma ulamaa ambiri anatenga.
 
Tatiyeni buku la صحيح فقه السنة ج1/593, pamutu woti
العدد الذي تصح به الجمعة” 
akunena kuti:
“Swalatul Jum’ah ndi imodzi mwa swalaat za Faradh zomwe Allah analamula, ndipo ndi imodzi mwa ma slogan a Chisilamu. Ndipo yemwe angaonjezere lamulo mmalamulo otheketsa kuti jamaah ya Jumah iloledwe, akuyenera kubweretsa umboni. Koma ngakhale kuti palibe umboni ngakhale umodzi pa chiwerengero cha jamaah ya Jum’ah kuchokera kwa Mtumiki salla Alaih wasallam, zodabwitsa ndi zoti zoyankhula zilipo zambiri pa kuganizira kwa chiwelengero cha Jumah mpaka zinakwana 15! Mauwa akupezeka mu Fat’hul Baari Sharhu Sahih Al Bukhari, Al Haafidh bun Hajar anatero mu vol.2/490,.
Komatu zonsezo zilibe umbon kupatula yemwe ananena kuti: “Jamaah ya Jum’ah imakwanira ndi chiwelengero cha anthu omwe amakwanira pa ma jamaah ena onse”. Ma condition akutheka kwa Ibaada akuyenera kubwera kuchokera mmaumboni a swareehatan, koma kubweretsa condition yopanda nayo umboni wochokera komwe ibaadayo inalamulidwa, ndikulakwira Allah Ta’la ndi Mtumiki wake, omwe analamula ibaada. Palibe Ibaada yomwe inalamulidwa nkusakwanira ma condition ake moti mpaka anthu kumakhala akusemphana zokamba ena kuyendera izi ena zina. Chiwelengero cha Jumah chikanakhala kuti nchofunika kukhala special, akanatifotokozera mopanga kukuluwika kulokonse kuti ibaada tidzipanga moapanda kupunguka kulikonse.”
 
Pomaliza, ndikufuna ndikutsimikizireni kuti tikamati ma imaam anasemphana, sizimatanthauza kuti ena analakwitsa ena analondola. Chifuklwa zimapezeka kuti amene amalalikira kuti Jum’ah imafunika anthu 40, omwe amakhulupilira zoti imafunika anthu 12 amakana kuti ayi sichoncho koma 12. Omwe amakhulupilira kuti anthu atatu, amakanira kuti omwe amaenea kuti anthu12 kapena 40 akulakwitsa. Mapeto ake anthu amapanga magulu chifukwa cha madh’ab, kupezeka kuti akusalana mmizikiti, kumati ife ndi a Shafi, zachimwenyezo ayi (powanena a Hanafi). Ndipo ena amafika ponena kuti Mmalawi aliyense amatsatira Shafi, ndipo yemwe satsatira Shafi si Mamalawi, akutenga za chimwenye. Subhaana Allah. Ma Imaam awa sikutitu anali Atumiki, sikuti anali perfect samalakwitsa ayi… Tikamasiyana muzochitika, tisamathamangire kuwapachika ma Imaam omwe anatilongosolera zomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam ankachita. Koma tiyeni tizame mmaphunziro kuti tipewe ma fitna mu deen. Tiphunzire zochokera mu Qur’an ndi Sunnah, zomwe anali kuphunzira ma Imaam onsewo.
 
Tidziwe kuti onse amene anadza pambuyo pa Mtumiki salla Allah alaih wasallam (ma Sahaba), komanso onse amene anadza pambuyo pa ma Sahaba (ma Tabiena) komanso onse amene anadza pambuyo pa ma Tabiena (ma Taabie taabieen), sanasiyane pa kugwiritsa ntchito chiphunzitso cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam, achina Shafi Maliki Hanbali, Abu Hanifa amenewa sanasiyane kalikonse, chifukwa iwo amatenga kuchokera ku Madh’hab a Salafi (madh’hab a Mtumiki ndi ma Swahaba ake) .. koma pambuyo pa mibadwo itatu yolungama imeneyi mpamene panadza anthu omwe anayamba kugwiritsa ntchito maganizo awo mu deen ya Allah subhaanah wa Ta’la. Komatu Allah Ta’la watiuza mu Qur’an malo ambirimbiri kuti kodi tidzitsatira ndani? Mu Surah Aali Imran akunena mu aayah 31 kuti
 
ُقل إِن كُنتُمْ تُحِبُّونَ اللّهَ فَاتَّبِعُونِي يُحْبِبْكُمُ اللّهُ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ذُنُوبَكُمْ وَاللّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ
Nena: (iwe Mtumiki) “Ngati inu Mukumkonda Allah, tsatani ine; Allah akukondani ndikukukhululukirani machimo anu. Ndipo AllahNgokhululuka, Ngwachisoni.”
 
Mu Surah Al Nisaai aayah 59 Allah Ta’ala akutiuza omwe tikuyenera kuwatsatira mu deen, akunena kuti
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُواْ أَطِيعُواْ اللّهَ وَأَطِيعُواْ الرَّسُولَ وَأُوْلِي الأَمْرِ مِنكُمْ فَإِن تَنَازَعْتُمْ فِي شَيْءٍ فَرُدُّوهُ إِلَى اللّهِ وَالرَّسُولِ إِن كُنتُمْ تُؤْمِنُونَ بِاللّهِ وَالْيَوْمِ الآخِرِ ذَلِكَ خَيْرٌ وَأَحْسَنُ تَأْوِيلاً
E inu amene mwakhulupirira! Mumvereni Mulungu ndiponso Mumvereni Mtumiki, ndi omwe ali ndi udindo painu. Ngati Mutatsutsana pachinthu chilichonse, Chibwezeni kwa Mulungu ndi Mtumiki Wake, Ngatidi mukukhulupirira Mulungu ndi tsiku lomaliza, kutero ndibwino; Ndipo zotere zili ndi zotsatira zabwino.
Akunenanso mu Surah Al Nur aayah 63 kuti
فَلْيَحْذَرِ الَّذِينَ يُخَالِفُونَ عَنْ أَمْرِهِ أَن تُصِيبَهُمْ فِتْنَةٌ أَوْ يُصِيبَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ
Achenjere amene akunyozera lamulo Lake kuti mliri ungawapeze, kapena kuwapeza chilango chowawa.
Mu Surah Al Hashr aayah 7 akunena kuti
وَمَا آتَاكُمُ الرَّسُولُ فَخُذُوهُ وَمَا نَهَاكُمْ عَنْهُ فَانتَهُوا
Ndipo chimene wakupatsani Mtumiki, chilandireni; ndipo chimene wakuletsani chisiyeni.
Komanso ma aayah ena. Ma Hadithinso alipo ambiri pankhaniyi. Monsemo akutitsimikizira kuti yemwe angapande kutsatira Mtumiki ndiye kuti ali mu chionongeko. Ngati tikutsatira Imaam, tionetsetse kuti zomwe tikutenga kwa iyezo anadzitenga mu Qur ‘an kapena kwa Mtumiki. 
 
Masiku ano anthu ambiri anasokonekera komanso ma sheikh ambiri anawasokoneza anthu pankhani ya ma imaam a madh’hab, zomwe zinapangitsa kuti anthu ambiri adzingotsatira mwa umbuli nkumati ine ndimatenga za Imam Shafi basi, ine Hanbali Maliki Hanafi, asakudziwa kuti kodi zimenezi nzichani … kutsatira ma imaam kunafika potianthu amatha kunyoza zomwe ananena Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Penanso ma Hadith amatha kubisidwa osabweretsedwa poyera, pofuna kuti zomwe anazolowera anthu zidzipitilira, nkhani yake madh’hab. Kuononga sunnah ya Mtumiki chifukwa chopanga taqleed imaam. 

Tatiyeni tione kuti ma imaam amenewa anatisambira bwanji mmanja amene timangotsatirafe.

 

Imaam Abu Hanifa rahimatullah anati:
إذا صح الحديث فهو مذهبي.
“Nkhani ikakhala yoona, Hadith iliyonse yoona ndi madh’hab anga” Kutanthauza kuti ma Salaf Saalih amenewa anali kutenga kuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam

Imaam Malikinso anati 

كل يُؤخذ من كلامه ويُرد إلا صاحب هذا القبر 

kapenanso mu kunena kwina

 ما من أحد إلا وهو مأخوذ من كلامه ومردود عليه إلا رسول الته يَة 

Aliyense zolankhula zake zimatha kutengedwa ndipo zimabwezedwa kwa iyeyo (kukanidwa), kupatula zochokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Kutanthauza kuti ngati imaam Malik mau ake sanalumikizane ndi zokamba za Mtumiki salla Allah alaih wasallam, tisawatsate. Koma iye monga mujtahid, apeza thawab imodzi pa kulimbikira kwake. Koma ngati mau akewo ali olondola, apeza thawab ziwiri chifukwa cha kulimbikira kwake, komanso kulondola kwake. Ndiye anasamba mmanja ponena kuti aliyense zolakhula zake zimakhala zoona kapena zolakwika kupatula Mtumiki, kutanthauza kuti nayenso akusamba mmanja kuti sakuyenera kutsatidwa mu zolankhula zake ngati zilibe umboni wochokera kwa yemwe zoyankhula zake zimakhala zoona zokhazokha sizikhala zabodza (Mtumiki)

Imaam Shafi’i rahimahullah ta’ala anayankhulanso chimodzimodzi kuti 

إذا صح الحديث فهو مذهبي.

Anayankhula  zofanana ndi Abu Hanifa ngakhale kuti awiriwa sanakumane. Ma imaam onsewa sanali kutsutsana, sanali kusemphana pazokamba zawo chifukwa onse madh’hab awo anali Madh’habu Nnabawiyya, Madh’hab a Mtumiki salla Allah alaih wasaalm ndi maswahaba ake ridhwaanullah taaa alaihim. Koma kupezeka kuti inu ndi ine tyikukokanakokana mpaka kusamukirana mmizikiti, chifukwa chotsatira ma imaam osiyana…pomwe eni akewo anali kugwirizana ndipo amatsatira zimodzi. Imaaam Shafi’i yemweyu anayankhula kuti 

إذا رأيتم كلامي يخالف الحديث فاعملوا بالحديث واضربوا بكلامي الحائط

mukaona kuti mau anga akusutsana ndi hadith, gwiritsani ntchito hadith ndipo muwamenyetse mau anga kukhoma, musawagwiritse ntchito.  

Tsopani Imaam Ahmad bun Hanbali anati: 

لا تقلدني ولا تقلد مالكاً، ولا الشافعي, ولا الثوري , وتعلّمْ كما تعلمنا, وقال : لا تقلد في دينك الرجال, فإنهم لن يسلموا من أن يغلطوا

Akuwasambira mmanja anthu amene amapanga taqleed zopanda umboni kuti: Musatsatire, musapange taqleed, musatsatire ine, musamutsatire Shafi’, ngakhale Maliki, ngakhale Al Thawri…koma phunzirani monga momwe ife tinaphunzilira. Ananenanso kuti: Usatsatire mu Deen yako anthu, chifukwa iwowo sali otetezedwa mu kulakwitsa. Akutiuza kuti tidzitenga malamulo kuchokera komwe ma imaam amenewa anali kutenga. Ngati tikutenga kuchokera kwa iwowo, tidziwatsatira mpaka tipeze kuti zikuchokeradi mu Qur’an ndi Sunnah, nddipo tikapeza kuti ndi zoyankhula zawo komanso zikusemphana ndi Qur’an ndi sunnah, tisadzitenge koma tifufuze zochokera mmalamulo.

Abale olemekezeka, tidziwe kuti kalekale kwambiri, kumayambiliro kwa Shariah ya Chisilamu, pamene kunalibe ma imaam omwe tikudzisankhirawa, anthu sanali kusonkhanira imaam wina wake kuti adzimutsatira zokamba zake, ayi. Aliyense anali kulimbikira kufunafuna zochokera mu Qurna ndi Sunnah. Koma tsopano izizi lero lino zinabwera chifukwa cha kusankhana basdi. Ndipo palibe Imaam yemwe anayambitsa zoti adzitsatidwa iyeyo zoyankhula zake, analibe nthawi imeneyio chifukwa onse anali otsatira madh’hab a Salaf Swaalih (madh’hab a Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndi ma Swahaba ake. Koma lero zomvetsa chisoni kwabwera kusankhana, mpaka madh’hab a ma Imaam onse anayi aja anthu akuwaona kuti ndi osochera, powanyoza nkumati salafi ndi zichani..salafi ndi anthu oipa..salafi salafi salafi…akumaganiza kuti Salafi ndi madh’hab omwe anapezeka pambuyo pa madh’hab a achina Shafi…sakudziwa kuti Salaf ndi madh’hab oyambilira ndipo ndi okhawo omwe anali kutenga Imaam Shafi, Malik, Hanbal, Abu Hanifa ndipo anali kuitanira madh’hab amenewa a Salaf Swaalih (Madh’hab a Mtumiki ndi ma Sahaba ake). Ndiye lero lino tidziwe kuti ma Imaam anayi onsewa ndi ophunzira kuchokera mmadh’hab a Salafi Swaalih (omwe ndi madh’hab a Mtumiki ndi ma Swahaba).

Ndi zambiri zomwe ndingafotokoze pankhani imeneyi ndipo nkhani ikhonza kutalika, koma chomwe ndingapemphe nchoti zoyankhula zangazi zikhale key wa khomo lanu lolowera mu kusakasaka maphunziro owonjezera kuti tidzidziwe zenizeni. Tisaimire pompa ayi chifukwa maulaliki awa zoyankhula zathu zimakhala zochita kusankha malinga ndi topic, koma tiyeni tilimbikire kufufuza maphunziro tisanayambe kugwiritsa ntchito zomwe tangomva. 

Ndikupempheni kuti mumverenso audio yomwe tinafotokoza pang’ono kwambiri zokunza ma Imaam anayi omwe ndi eni ake a Madh’hab anayi amenewa, mmenemonso mwina mukhonza kupezanso phindu kagawo kena.

Ndibwerezenso mau a Imaam Ahmad kuti zonse zomwe ndayankhulazi mukhonza kupezeka ma mistake malinga ndi kuti ndine munthu zoyankhula zanga sizingakhale zoona zonse, koma cholinga changa nkufuna kuti zikhale zoona..choncho ngati mungapezemo zabwino, tengani ndipo falitsani kuti ena apindule. Koma ngati mungapezemo zolakwika, ndikhonzeni ndipo mupeza thawaab zothandizana ku zinthu zabwino, ndipo ine ndili okonzeka kubwelera ku zoyankhula zanga ndi kukhonza mistakeyo moonekera. Pakuti pamwamba pa ozindikira palinso ozindikira kuposa iwo, ndiop kuzindikira konse ndi Allah Ta’la.