Panopa dziko likuyenda chonchi:Yemwe amatsata za dziko akutengedwa kuti ndi otsogola chifukwa zikubwera mwatsopano. Ndiye otereyo kalikonse ka mu deen akumakachita mwa fashion malinga ndi mmene dziko likuyendera. 

Yemwe amagwiritsa imaan yake molimba potsatira malamulo a dewn yake, akutengedwa kuti ndi otsalira/wachimidzi chifukwa akuyendera zachikale mzaka 1,450 zapitazo … mu deen mulibe fashion.

Ndiye ngakhale ma sheikh ambiri, akuyendera fashion kusintha kwa dziko, nkumamenyetsa kukhoma malamulo a deen; kuchita manyazi kufalitsa malamulo omwe anatsitsa Allah Ta’ala kuti afalitse anthu adziyendera … kuchita manyazi kunenedwa kuti ndi otsalira pa za dziko. 

Malamulo a mu Qur’an komanso Sunnah asanduka kukhala ochita yemwe wafuna. Kusankha kusiya lamulo la Allah ndikuikapo zofuna zake. Ufulu wa pa dunia tawulowetsa mu Deen.

Allah analetsa  mu Surat Al-Ahzaab Aayah 36 kuti munthu okhulupilira asazisankhire chochita nkusiya zomwe Allah ndi Mtumiki wake analamula.

 

وَمَا كَانَ لِمُؤْمِنٍ وَلَا مُؤْمِنَةٍ إِذَا قَضَى اللَّهُ وَرَسُولُهُ أَمْرًا أَن يَكُونَ لَهُمُ الْخِيَرَةُ مِنْ أَمْرِهِمْ ۗ وَمَن يَعْصِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ فَقَدْ ضَلَّ ضَلَالًا مُّبِينًا

 

“Ndipo sikoyenera kwa wokhulupirira wachimuna ndi wokhulupirira wachikazi, Mulungu ndi Mtumiki wake akalamula chinthu, iwo kukhala ndi chifuniro pazinthu zawo. Ndipo amene akunyoza Mulungu ndi Mtumiki wake, ndithu, wasokera; kusokera koonekera.” Qur’an 33:36

Kuzisankhira zochita kusiya zomwe Allah ndi Mtumiki wake analamula ndi kunyoza Allah ndi Mtumiki ndipo zotsatira zake oteroyo amakhala osokera koonekera.

Lero deen yathu ikuyenda upside down; amuna tikusankha mavalidwe omwe anatiletsa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, tikumeta mbali yamutu ndikusiya zitsitsi mbali ina, akuti kuyenda ndi dziko. Chipongwe chakenso zimenezo amapanga Lachisanu pokhonzekera Jum’ah akuti kudzikongoletsa! Mtumiki wathu analetsa kumeta mbali ina nkusiya tsitsi mbali ina, ngakhale kipingula mbali ina analetsa. Lero Asilamu otukuka ndi zomwe akuchita.

Kudzikongoletsa Lachisanu popita kumzikiti ndikofunikira kwa amuna. Koma ndizoletsedwa kudzikongoletsa ndi machimo. Zikongoletseni momwe Allah akufunira osati momwe shaytwaan akufunira. Koma lero yemwe amadzikongoletsa potuluka mnyumba ndi muntju wamkazi, popita ki mzikiti osasiyana ndi popita kumsika.Uyenda ndi dziko mpaka liti ndiwe dothi lokhalokha pamene ulipo dziko udzalisiya! mmalo mokhonzekera moyo womwe udzakhale zaka miyandamiyanda… 

Zonsezitu tikutengera ufulu wopatsidwa kuchokera kwa oyendetsa dziko omwe akutsogoleredwa ndi Shaytwaan … ife nkumanyadira democracy (dēmos krátos) = (people, power/force to rule). 

Ndiye taitenga democracyo nkumalamulira Deen, kulowetsamo malamulo athu poti tapatsidwa kaufulu ndi timphamvu kuchokera kwa Mulooki Ddunia (mafumu a pa dziko), kuti tiwukire nato timphamvuto Malikal Mulooki fi Ddunia wal Aakhirah (Mfumu ya Mafumu kumwamba ndi pansi, Allah Ta’ala).

Kuweruza mokondera olemekezeka ndi Kupondereza anthu wamba
Ma sheikh athu padziko mwatani kodi? Atsogoleri athu mwatani?Mukumalimbana ndi munthu yemwe wachita choipa akakhala kuti ndi osadziwika komanso osawuka … ndiye anthu akumadziwira pa iyeyo kuti zomwe wachitazo ndi tchimo kuchokera mma fatuwa omwe akumavumbuluka pamenepo. Koma tsiku lotsatiralo mzanu olemekezeka, otchuka, wa ndalama ndipo odziwika dziko lonse akachita tchimo lomwelo komanso lalikulu kuposa limenelo, mumamubisa mkumawatulutsira ma fatuwa anyuwani owatseka pakamwa anthu omwe akuwonetsa kuopidwa ndi zomwe mwachitazo.Zimenezi ndi zomwe ambiri mwa atsogoleri a Chisilamu akuchita dziko lonse kulikonse.Ndalama ikulamulira zoipa Allah atiteteze.

Mtumiki salla Allah alaih wasallam analetsa zomwe zikuchitika pakati pathu lero lino, ndipo zikuchitika mopanda manyazi ndi mantha ngati kuti ndi malamulo atsopano  omwe atsika kuchokera kumitambo seven!
Allah Ta’ala analetsa kukondera popereka chigamulo. 

Mwachitsanzo anamuuza Sayyidna Daud alaih Salaam kuti aweruze pakati pa anthu awiri omwe anadza kudzamudandaulira; mmodzi anali olemera pomwe winayu anali ochepekedwa ndipo olemera anafuna kukwaniritsira cbuma chake chochuluka kale potenga chuma chonse cha ochepekedwa uja.

Mtumiki salla Allah alaih wasallam analetsa kukondera popereka chigamulo kwa olakwa
Chitsanzo ndi mzimai wina ochokera m’banja lolemekezeka la Makhzoom yemwe anaba tsiku lina, ndipo anthu anawopa kuti amudule dzanja chifukwa chakulemekezeka kwa banja lomwe ankachokera, kumachita kuti mbuyo monsemo amati munthu akaba samacherenga podula mkono. Ndiye apa anaopa kuti apanga bwanji …  mpaka anamtumiza Usama bin Zaid poti anali okondedwa kwa Mtumki, ndipo anaona kuti angakalimbe mtima kuyankhula ndi Mtumiki pankhaniyi. Mtumiki atamva nkaniyi, anakalipa ndikunena kuti:”zoona ukukhululuka pa chilango cha Allah?” kenako anaimilira ndikulalikira kwa anthu:

“Ee inu anthu, ndithu anthu ambuyo mwanu anasochera chifukwa cha mchitidwe woti munthu olemekezeka mwa iwo akaba anali kumusiya, ndipo ofowoka akaba anali kumupatsa chilango. Wallahi thumma Wallahi, akanakhala kuti Fatima mwana Muhammad (mwana wanga) ndamene waba, Muhammad akanadula mkono wake (wa Fatima)!”

Ena posachedwapa atulutsa fatuwa yololeza mkazi kuyenda yekha ulendo popanda mahram!Akuti lamulo limenelo liribe ntchito “munyengo inoyo” poti zinthu zinasintha ndipo malamulo amenewo ndi “akale”.

Atulutsa fatuwa yololeza mzimai kuvala trouser pamtunda, bola ikhale yotakasuka yosathina… akuti kalelo kunalibe matrouser poti zovala zawo pachikhalidwe chawo zinali zotakasuka … SubhaanAllah!! Inu ngati muli Asilamu mukuyemera kuvala mavalidwe a Chisilamu. Ndizabodza kuti kalekunalibe ma trouser; analoko ndipo azimai ankavala koma amuna sanali kuwaona.

Ma ulamaa amenewo adziwe kuti ali panja pa gulu la ma ulamaa aja omwe Allah anawasimba kuti ndi omwe ali owopa Allah mwa akapolo ake! 

 

إِنَّمَا يَخْشَى اللَّهَ مِنْ عِبَادِهِ الْعُلَمَاء

 

Ndithu odziwa ndi amene amamuopa Mulungu mwa akapolo ake Qur’an 35:28

Aphunzitseni anyamata mavalidwe osavuta a Chisilamu. Aphunzitseni kuipa kwa mametedwe osiya tsitsi mbali inawo.  Aphunzitseni azimai mavalidwe a hijab yachikale yomweyo yomwe ili yamadalitso ndipo yoitana Angelo a madalitso ndi chikhululuko, asiye iyo yomwe amabisalamo ma shaytwaan nthawi zonse nkumathamangitsa Angelo omupemphera chikhululuko!

Atulutsa fatuwa yololeza kugonana ndi zibwenzi usiku mwezi wa Ramadhan; akuti palibe vuto kugonana usiku pachibwenzi kapenabanja losachita nikaah, poti nsambizo sizimakhunzana ndi kusala kwa masana, koma zimangokhala x2 basi. Sunna ya ndani iyi? 

Inu simukuona kuti ngati munthu akufunsa funso limenelo ndiye kuti wakhala akuchita zinaa myezi 11 yonseyi, komano akufuna kudziwa kuti mwezi wa Ramadhan poti okwatira amaletseswa masana, nanga ife azibwenzi kupanga usiku zikhala bwanji.Ndiye poti munawaloleza kale kuchita zinaa nthawi iliyonse, mwati koma mu Ramadhan mokha osachita masana ndipo palibe vuto kuchita usiku poti mwamasula.

Tiwuzeni kuti tisamachite chiwerewere mwezi uliwonse nthawi iriyonse malo aliwonse ngakhale usiku pa chaka! chonse!Muwopeni Allah pa mafatuwa anu.