الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ وَجَعَلَ الظُّلُمَاتِ وَالنُّورَ ۖ ثُمَّ الَّذِينَ كَفَرُوا بِرَبِّهِمْ يَعْدِلُونَ
Pamene chaka cha anzathu a chi Roma chomwe timagwiritsa nawo ntchito chatha, tiyeni tione mbali ina ya calendar imeneyi.
Inde, ife Asilamu tilibe nazo phindu, kupatula kuti pachiyambi tinayamba kugwiritsa nawo ntchito mpaka kuiwala calendar yathu yomwe ndi yovomerezeka pamaso pa Allah Subhaanah wa Ta’ala komanso dziko lonse, ndipo mbiri yake ndi yapamwamba.
Nzofunikira kwambiri kuti tidziwe mbiri ya calendar imene timagwiritsa ntchito tsiku ndi tsiku, poti calendar imeneyi ndi ya chipembedzo ndipo ife Asilamu chifukwa choti timayendera yomweyi muzintchito, mmasukulu komanso mmoyo mwathu watsiku ndi tsiku, chomwecho timakhalanso tikulowelera nawo muzochitika zachipembedzo cha chi Roma mkati mwakemo. Choncho apa tikadziwa tikhala tikudziwa kuti ndi phindu lanji pomwe timapezamo. Nanga ndi malire anji amene tili nawo pogwiritsa ntchito calendar imeneyi.
Calendar imeneyi inatchedwa kuti Roman Calendar chifukwa ndamene anaikhonza. Kenako anadzaisintha Julius Caesar ndipo inatchedwa kuti Julian Calendar.  Kenako anadzaisintha (edit) Pope Gregory XIII ndipo inatchedwa Gregorian Calendar
Nanga myezi yakeyi imatanthauza chani?
Chaka chathu chomwe chimagwirizana ndi Qur’an komanso Sunnah ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam, akunena Allah mu Qur’an kuti
إِنَّ عِدَّةَ الشُّهُورِ عِنْدَ اللَّهِ اثْنَا عَشَرَ شَهْرًا فِي كِتَابِ اللَّهِ يَوْمَ خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْض
Ndithu chiwerengero cha miyezi kwa Allah ndi myezi 12, (kuyambira) tsiku lomwe analenga kumwamba ndi pansi. Surah Al Tawbah Aayah 36.
Ndiye ichi ndi chizindikiro chachikulu chosonyeza kuti calenda ya Chisilamu ndiyopambana
Koma kodi nchifukwa chani ndikuti calendar iyi nja chi Roma?
Myezi yonse yomwe timaidziwayi ndi ya chi Roma. Kodi miyezi ya pa chaka cha chi Roma imatanthauza chani? Nanga zinayamba bwanji?
Kwenikweni chaka cha chi Roma kunalibe ndipo chinakhonzedwa ndi mafumu a ku Rome mosinthasintha. Oyambilira kukhonza anaika miyezi 10 yokha, ndipo anadza ena nkuonjezera myezi iwiri kukhala 12. Ndipo chiwelengero cha masiku chinali chikupungildwa ndi kuonjezeredwa , nchifukwa chake timaona nthawi zina mwezi uthera 28, 29, 30, 31.
Koma tsopano nchifukwa chani zimenezi timadzitcha kuti ndi myezi kumachita maina amenewa samagwirizana ndi mwezi wakumwamba?. Uwutu ndi umboni wina woti calendar ya Chisilamu ndi imene ili yothandiza aliyense padziko pano chifukwa ndiyokhayo yomwe mwezi umayendera limodzi ndi mwezi wakumwamba. Ukaoneka, date imakhala 1. Pomwe myezi ya chi Roma simagwirizana ndi mwezi wakumwamba.
Maina a zomwe amati myezi ya January Febriary …anachita kukhonzedwa ndi anthu, ndipo amasintha malinga ndi zilankhulo. Choncho apa tiona maina enieni (a original) a myeziyi:
Martius “March”
Aprilis “April”
Maius “May”
Junius “June”
Quintilis “July”
Sextilis “August”
September “September”
October “October”
November “November”
December “December”.
Mwezi woyamba unali March. Ndipo miyezi yomwe ikupezeka mu nthawi yozizira (January,  February) inalibe maina panthawiyo chifukwa choti nthawi imeneyi za ulimi sizinkayenda.
Numa Pompilius, mfumu yachiwiri ya Rome mchaka cha 700 BC (Isa alaih salaam (Yesu) asanabadwe, adaonjezera myezi iwiri:
Januarius “January”
Februarius “February”
Pachiyambi, monga ndanenera kale, chaka chinkayamba ndi Martius “March”, ndipo Pompilius anasintha January kukhala mwezi woyamba. Mkuluyu anasinthanso chiwerengero cha miyezi ina nkumathera ma number osagawika ndi 2 (odd numbers).
Awatu sikuti anali Atumiki a Mulungu kuti tinene kuti amalondola ndipo zinali zovomerezeka kwa iwo kugawa masiku a Mulungu chonch. Koma anali kupanga ijtihaad yawo nthawi imeneyi.
Mchaka cha 46 BC (Isa alaih salaam (Yesu) asanabadwe), Julius Caesar anasinthanso calendar ya chi Roma ija (Roman calendar) nkukhala (Julian calendar), ndipo anasintha chiwerengero cha masiku a myezi ina nkukhala 29,30,31…
KOMANO NANGA MAINA OMWE TIKUMAWANYADIRA LEROWA ANACHOKERA KUTI?
Maina a miyezi anachokera ku maina a milungu ya Aroma, ina ku maina a mafumu ndipo ina malinga ndi number yomwe mweziwo ukupezekera.
Tiyeni tione mwezi umodzi umodzi
January
Unatchulidwa potengera Mulungu wa Aroma wachiyambi ndi mathero, kapena makomo ndi zitseko. Ndipo chizindikiro chake ndi nkhope ziwiri zomwe zayang’ana mbali zosiyana. 
Dzina la mulunguyu ndi *Janus*. Ankapembedzedwa kumayambiliro kwa nthawi ya kukolola, kudzala, chikwati, kubadwa komanso kumayambiliro a zochitika zina ndi zina za mu umoyo wa munthu.
Eyetu ndi mwezi umene Asilamu ambiri pakali pano ali nawo busy kusangalala kuti awulowa  (gateway to 2019).
February
Dzina limeneli linachokera ku dzina la mulungu wakale wa chi Italian, Februus, kapenanso ku chisangalalo chimene ankachita ma Romans nthawi imeneyi chodziyeretsa chotchedwa february.
March
Mweziwu unatchulidwa potengera dzina la mulungu wa nkhondo wa Aroma otchedwa Mars.
April
Kuchokera kwa Aphrodite mulungukazi wa ma Greek kumbali ya za chikondi ndi kukongola. Ku Rome ankadziwika ndi dzina loti Venus.
Komanso ena amati April anachokera ku dzina loti Aprilis (aperire) “kutsegula”. Chifukwa choti ndi nyengo imene maluwa amatsegula.
May
Kuchokera kwa Maiesta, mulungukazi wa ma Roman kumbali ya ulemu.
Mchilankhulo cha French yakale, amatchedwa Mai. Ndipo mu English yakale amatchedwa Maius koma yatsopano ndi Maia. Ndipo mu Latin mweziwu umatchedwa Maius mensis “mwezi wa Maia”.
June
Kuchokera kwa Juno. Mulungukazi wamkulu wa Rome kumbali ya maukwati komanso azimai. Anali mlongo wake wa Jupiter ndipo ankadziwika ku Greece kuti Mulungukazi Hera.
July
Umenewu ndi mwezi womwe Julius Caesar anabadwa. Ndipo anautcha July mchaka cha 44 BC, chaka chomwe anaphedwa, kuchokera ku dzina lake “Jul _ius_. Koma kale unkatchedwa kuti Quintilis (mwezi wachisano) kuchokera pa March paja.
August
Mweziwu pachiyambi unkatchedwa Sextilis (kuchokera ku sextus, “six”), koma dzina linasinthidwa popereka ulemu kwa mfumu yoyamba ya Rome, Augustus Caesar (chifukwa myayi yake yambiri inkachitika mmwezi umenewu).
September
Kuchokera ku number seven yomwe mweziwu unali, kusanabwere January ndi February. septem, “seven”.
October
Kuchokera ku number eight…octo, “eight”
November
Kuchokera ku number nine…novem, “nine”.
December
Kuchokera ku number ten…decem, “ten”.
N.B: mau oti (-ber) pa maina monga Septem-ber, Octo-ber, Novem-ber, Decem-ber, ndi ongoonjezera, kutanthauza kuti (-wachi..) Mwezi wachi seven…etc
Ndiye omwe akumati Happy New Year 2018, akusangalalira kubwera kwa mulungu wawo,  Janus, mulungu wawo wa kumayambiliro kwa zinthu, monga chaka.
Pomaliza ndikuti;
إِنَّ عِدَّةَ الشُّهُورِ عِنْدَ اللَّهِ اثْنَا عَشَرَ شَهْرًا فِي كِتَابِ اللَّهِ يَوْمَ خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْض
Ndithu chiwerengero cha miyezi kwa Allah ndi myezi 12, (kuyambira) tsiku lomwe analenga kumwamba ndi pansi. Surah Al Tawbah Aayah 36.
Imeneyo ndiye calendar ya Msilamu yomwe ikudziwika kwa Allah. Ndiye zomvetsa chanasa ndi chisoni chomwe,  lero lino Msilamu sadziwa myezi yomwe ili yodziwika kwa Allah, koma akudziwa myezi 12 yomwe ili yodziwika kwa Julius Caesar (Kaisara) … Abale za Kaisara zisiyeni Kaisara,  za Allah zitengeni nkudziika pamtima…
Titero kuti ngati tilibe kuchitira mwina koma kugwiritsa ntchito calendar yachi Romayi powelengera nthaw zathu, titero koma osadumpha malire athu, monga mmene ndanenera kumayambilito kuti tisiye zochitika zawo zomwe zimachitika pachaka chirichonsezo, chifukwa zimenezo ndi mbali ya ibaada yawo; ife tili ndi ibaada yathu yofunika tiidziwe myezi yonse 12 ndikuizolowera, osati mwezi wa Ramadhan okha, kapena masiku 10 a Dhul Hijja okha.
Zolakwika zilizonse muzoyankhula zanga sicholinga, ndipempha Allah akhululuke komanso musadzitenge ngati zolinga zanga.
wassalam alaiku warahmatullah wabarakaatuh