Bodza lachinayi:
“Mitala imachepetsa ma Rizq”
Lina mwa maina a Allaah ndi Ar-Razzaaq (Wopereka ma Rizq).
Tikamakamba za ma Rizq, tikukamba chirichonse chimene munthu amapeza pano pa dziko lapansi ndipo Mwini ma rizq amenewa ndi Allaah osati ife anthu. Tamvani mmene Iye akuyankhulira mu Qur’aan (Suurah Huud 11:6):
وَما مِنْ دَآبَّةٍ فِي الْأَرْضِ إِلَّا عَلَى اللَّهِ رِزْقُهَا.
Palibe nyama yomwe ili padziko lapansi kupatula kuti Allaah adaipatsa ma rizq ake.
Pa chifukwa ichi, ma rizq a Allaah sangamuphonye munthu chifukwa cha kusafuna kwa anthu ena. Ndipo ngakhale kuti anthu ena atsekereze njira zoti wina asapezere ma rizq ake, Allaah adzamupatsabe munthuyo, popeza  zimenezo ndi zimene Iye adalemba kale. Ndipo ma rizq a mwamuna sangapunguke chifukwa choti akukhala ndi anthu ambiri, kapena wakwatira akazi angapo, kapena wabereka ana ambiri.
Malinga ndi kuti Allaah wawapanga anthu mosiyana, anawapatsanso ma rizq osiyana wina ndi mzake. Ena amawapatsa ambiri, ndipo ena amawapatsa ochepa – ndipo munthu sangadye ma rizq a munthu wina.
Tikawona mu Sunan Ibn Maajah, #2144; mu kuyankhula kwake Mtumiki (ﷺ) mu Hadiith ya Jaabir Ibn ‘Abdullaah, iye adati:
أَيُّهَا النَّاسُ اتَّقُوا اللَّهَ وَأَجْمِلُوا فِي الطَّلَبِ فَإِنَّ نَفْسًا لَنْ تَمُوتَ حَتَّى تَسْتَوْفِيَ رِزْقَهَا وَإِنْ أَبْطَأَ عَنْهَا.
Eh inu anthu! Muopeni Allaah ndipo khalani osapyola malire posakasaka ma rizq; chifukwa palibe mzimu umene umamwalira pokhapokha utalandira ma rizq ake, ngakhale atati akuupeza mwa pang’ono pang’ono.
Komanso Mtumiki wa Allaah (ﷺ), kudzera mu Hadiith ina ya ‘Abdullaah Ibn Mas’uud (Swahiih al-Bukhaari, #3208), adati:
إِنَّ أَحَدَكُمْ يُجْمَعُ خَلْقُهُ فِي بَطْنِ أُمِّهِ أَرْبَعِينَ يَوْمًا، ثُمَّ يَكُونُ عَلَقَةً مِثْلَ ذَلِكَ، ثُمَّ يَكُونُ مُضْغَةً مِثْلَ ذَلِكَ، ثُمَّ يَبْعَثُ اللَّهُ مَلَكًا، فَيُؤْمَرُ بِأَرْبَعِ كَلِمَاتٍ، وَيُقَالُ لَهُ: اكْتُبْ عَمَلَهُ وَرِزْقَهُ وَأَجَلَهُ وَشَقِيٌّ أَوْ سَعِيدٌ‏.‏ ثُمَّ يُنْفَخُ فِيهِ الرُّوحُ.
Ndithudi chilengedwe cha wina aliyense mwa inu chimasonkhanitsidwa m’chiberekero cha mayi wake mu masiku okwana makumi anayi (40); kenako pakatha masiku ena 40, munthuyu amakhala ‘alaqah (m’bulu wa magazi owundana); kenako pakathanso masiku ena 40, munthuyu amakhala mudhghah (mnofu); kenako Allaah amatumiza Mngelo yemwe amamulamula kuti alembe zinthu zinayi. Iye (mngelo) amayalamulidwa kuti: “Lemba ntchito zake, ma riziq ake, tsiku lake la imfa, komanso kuti adzakhala wa mwayi kapena tsoka (kumbali ya chipembedzo).” Kenako mzimu umauziridwa mwa iye (munthuyu pakatha masiku 120).
Aliyense womvetsetsa Aayah komanso ma ahaadith amenewa sangakhale wodandaula kuti mwamuna ngati watenga mkazi wina, ndiye kuti ma rizq adzapunguka mwa mkazi woyambayu.
Ndipo umboni ndi wochuluka kuti, pambuyo poti ali ndi ma rizq ake okhazikika, ntchito zabwino zimene iyeyu akugwira zimaonjezeranso ma riziq ake:
وَمَن يَتَّقِ ٱللَّهَ يَجْعَل لَّهُۥ مَخْرَجًا – وَيَرْزُقْهُ مِنْ حَيْثُ لَا يَحْتَسِبُ
Ndipo amene angakhale ndi Taqwaa mwa Allaah, Iye adzamupangira njira yotulukira (mu masautso). Ndipo adzamupatsa ma rizq kuchokera mu njira zimene iye samayembekezera. (Suurah At-Twalaaq 65:2-3)
Ndipo mu Musnad Ahmad (vol. 2, tsamba 332, Hadiith #205), ‘Umar Ibnil Khattwaab adafotokoza kuti Mtumiki wa
Allaah (ﷺ) adati:
لَوْ أَنَّكُمْ تَتَوَكَّلُونَ عَلَى اللهِ حَقَّ تَوَكُّلِهِ، لَرَزَقَكُمْ كَمَا يَرْزُقُ الطَّيْرَ، تَغْدُو خِمَاصًا وَتَرُوحُ بِطَانًا
Mukadati mukudalira mwa Allaah kudalira kwenikweni, akanakudyetsani ngati momwe amazidyetsera mbalame; izo zimatuluka mzisa zawo zili ndi njala ndipo zimabwerera zitakhuta.
Tizindikirenso kuti chilichonse chimene chili cha uchimo, chimapungula ma rizq a munthu akamachichita. Mtumiki wa Allaah (ﷺ), kudzera mwa Thawbaan (Sunan Ibn Maajah, #4022), adati:
إِنَّ الرَّجُلَ لَيُحْرَمَ الرِّزْقَ بِالذَّنْبِ يُصِيبُهُ.
Ndithudi munthu amamanidwa ma rizq (oonjezera) chifukwa cha machimo amene amawachita.
Choncho, yemwe wakwatira akazi awiri, atatu kapena anayi, amakhala kuti wachita chinthu chabwino chimene sichingapungule ma rizq ake mu njira ina iliyonse. Ndipo Allaah amamutsegulira makomo a mitendere yake mosavuta.
Pomwe uyu wochita chiwerewere, nthawi zonse amamanidwa madalitso (rizq). Zinthu zimayamba kukhala zovuta pa iyeyu; amayamba kukhala mu moyo wa nkhawa nthawi zonse, amaononga ndalama, ndipo kulikonse komwe amatembenukira amapeza kuti makomo atsekedwa.
Ndiye ma rizq sangapunguke chifukwa cha mitala; m’malo mwake amaonjezereka malinga ndi mmene adasimbira ma Swahaabah:
‘Abdullaah Ibn Mas’uud mu Tafsiir Al-Qurtwubiy (volume 12, tsamba 241) komanso Tafsiir Ibn Kathiir (volume 6, tsamba 51); adati:
الْتَمِسُوا الْغِنَى فِي النِّكَاحِ.
“Funanifunani kulemera kudzera mu ukwati.”
Umar Ibnil Khattwaab adati:
عَجَبِي مِمَّنْ لَا يَطْلُبُ الْغِنَى فِي النِّكَاحِ، وَقَدْ قَالَ اللَّهُ تَعَالَى: إِنْ يَكُونُوا فُقَراءَ يُغْنِهِمُ اللَّهُ مِنْ فَضْلِهِ.
Amandidabwitsa yemwe safunafuna kulemera kudzera mu ukwati, chikhalirecho Allaah adati: “Ngati ali osauka, Allaah adzawalemeretsa kudzera mu chuma Chake.” [Tafsiir Al-Qurtwubiy (volume 12, tsamba 241) komanso Tafsiir Ibn Kathiir (volume 6, tsamba 51)]
Suurah An-Nisaa’ 4:3
وَإِنْ خِفْتُمْ أَلَّا تُقْسِطُوا۟ فِى ٱلْيَتَٰمَىٰ فَٱنكِحُوا۟ مَا طَابَ لَكُم مِّنَ ٱلنِّسَآءِ مَثْنَىٰ وَثُلَٰثَ وَرُبَٰعَۖ فَإِنْ خِفْتُمْ أَلَّا تَعْدِلُوا۟ فَوَٰحِدَةً…
Choncho, kwatirani amene akusangalatsani mwa akazi; awiri, atatu, kapena anayi. Koma ngati mukuopa kuti simukukwanitsa kuchita chilungamo (pakati pa akazi angapowa), basi kwatirani mmodzi…
TIYENI TICHOTSE NKHAWA ZATHU
Kodi inu ngati mkazi wa Chisilamu, mungamve bwanji mwamuna wanu atakuwuzani kuti akukwatira mkazi wina potsatira Aayah imeneyi?