Bodza lachitatu:
“Mitala imayambitsa matenda”
Nkhani ya mitala idazunguliridwa ndi zokamba zambiri zomwe sizili zolondola. Kwa ena mwa akazi amene mwamuna wawo wagwidwa akugonana ndi mkazi wina, iwo samakhumbanso kuti akhudzidwe (akhale limodzi ndi mwamuna wawo) chifukwa amaopa kuti mwamunayo awapatsira matenda. Iwo amavutika ndi maganizo odziwona kuti mwina sakukwanira, ndipo nsanje imakula mwa iwowo, chikaiko pa mwamunayo chimakwera chifukwa nthawi zonse amakhala akumukaikira pamene wayankhula kuti akuwafuna.
Ndipo izi zimakhalanso zovuta kwambiri pa iwowa akakhala kuti mwamunayo wakwatira mkazi wina, yemwe adzipita kunyumba kwake mosazemba. Chifukwa iwowa m’maganizo mwawo amati mitala iwabweretsera matenda osiyanasiyana.
Anthu omwe adazindikira kuti chiwerengero cha Asilamu chikuchuluka kudzera mu mitala adapeka bodza loti mitala imabweretsa matenda opatsirana pogonana monga chindoko, chizonono, mabomu komanso edzi ndi cholinga choti Asilamu, makamaka achikazi, awope kuvomera kukhala pa mitala.
Mukachita kafukufuku mupeza kuti mwamuna amene ali pa chiwopsezo Cha kutenga matenda opatsirana pogonana ndi uyu yemwe amagonana ndi akazi oti sanawakwatire. Pomwe mwamuna amene wakwatira akazi awiri, atatu kapena anayi; sakhala ndi nkhawa chifukwa amadziwa mmene akazi akewo aliri ndipo akaziwonso amadziwana momwe alili.
Tidziwe kuti pali kusiyana pakati pa chiwerewere ndi banja. Chimene Allaah wachiloleza sichingafanane ndi chimene Iye wachiletsa. Chomwe Allaah waloleza chimakhala ndi ubwino wambiri kuposa mmene anthu timaganizira. Ndipo chomwe Allaah wachiletsa chimakhala ndi kuipa kwakukulu kuposa mmene ife anthu tingaganizire.
Chiwerewere mwamuna amagonana ndi mkazi woti sakudziwa mayendedwe ake kuseliku. Ndipo mwamuna wachiwerewere asamaganize kuti iyeyo alipo yekha amene amagonana ndi mkazi woyendayendayu. Izi ndi zimene mwina anthu amaganiza pa nkhani ya mitala kuti mwamuna akamagonana ndi akazi awiri ndiye kuti pakhala matenda opatsirana mu njira yogonana. Malinga ndi kuganiza kolakwika kwa anthu, ambiri amayesa kuti mitala ndi ya anthu okonda chiwerewere. Tidziwe kuti mitala ndi banja osati chiwerewere ndipo mitala siimangopangidwa mwa chisawawa ngati mmene amuna ochimwawa amachitira ndi akazi oyendayenda.
Mitala imachitidwa mwadongosolo ngati mmene mwamuna amakwatirira mkazi woyamba. Ndondomeko yonse imene iyeyo adaitsata ya Sharii’ah pokwatira mkazi woyamba, akuyeneranso kuitsatira ndondomekoyo potenga mkazi wachiwiri. Sizili zoyenera kungokwatira mkazi mwamsanga posafufuza mbiri yake, khalidwe lake, thanzi lake (kumbali ya matenda) komanso zinthu zina ndi zina zimene zingampangitse iyeyu (mwamunayu) kukhala bwino ndi akazi angapo.
China mwa zinthu zofunikira kuyang’ana ndi mbali ya ukhondo wa mkaziyu ndi khalidwe lake. Kuchokera mu khalidwe lake, mwamuna azindikira kuti mkaziyu si wachimasomaso zomwe zingakhale zabwino pa iyeyu ndi mkazi woyambayu. Chifukwa mkazi wa chimasomaso adzati mwamunayu akachoka pakhomo nkupita kwa mkazi wake wina, iyeyu azibweretsa chibwenzi pakhomopo zomwe zili zinthu zonyasa kwambiri pamaso pa Allaah. Komanso mwamunayu akuyenera kuyang’anitsitsa kuti mkaziyo ndi wa ukhondo. Chisilamu sichigwirizana ndi munthu wa uve amene sadzisamalira bwino thupi lake komanso wosalabadira umoyo wake.
Pamene mwamuna wafuna kumukwatira mkazi, zili zofunikira kuti munthawi yomwe iyeyu wakakumana ndi womuyang’anira mkaziyo (waliy), akuyenera kuti apitenso ndi mkaziyo pamodzi ndi waliy wakeyu kuchipatala kuti akadziwe mmene mkaziyo aliri m’thupi lake. Izi zimachotsa chikaiko mwa mkazi woyambayu komanso mwa mwamunayu.
Ndipo ndizofunikira kuti mkaziyo asabise mmene alili kumbali ya matenda ena amene angathe kubweretsa vuto kwa mwamunayo ndi mkazi wake woyambayo.
Mtumiki wa Allaah (ﷺ), kudzera mu Hadiith ya Yahya Al-Mazaaniy komanso ‘Abdullaah Ibn ‘Abbaas, akufotokoza kuti:

لَا ضَرَرَ وَلَا ضِرَارَ

“Osabweretserana choipa komanso osabwenzera (kubwereza) choipa.”
Hadith imeneyi tiipeza mu Muwattwa’ Maalik, vol. 4, tsamba 1078, hadith 2758; Musnad Ash-Shaafi’iy, tsamba 224; komanso Musnad Ahmad #2865.
Choncho, matenda onse amene munthu angathe kupatsira mnzake kudzera pogonana akuyenera kunenedwa banja lisanachitidwe. Mkazi ayankhule mawu oti: “Ndili ndi nthenda yakutiyakuti,” komanso mwamuna anene nthenda yomwe ali nayo. Ndipo mopanda chikaiko, ngati mwamuna wakwatira mkazi kudzera mu njira imeneyi, palibe zodandaula matenda ngati amenewa chifukwa mkazi amene ali pa mitala ndi wa ukhondo ngati momwe aliri mkazi yemwe sali pa mitala.