Ibn Qudaamah mu Al-Mughniy, (vol. 8, tsamba 151) adati:
وَقَدْ اشْتُهِرَ بينَ النَّاس وجودُ عَقْدِ الرَّجُلِ عن امرأتِه حينَ يَتزوَّجُها. فلا يَقْدِرُ على إتْيانِها، وحَلُّ عَقْدِه، فيَقْدِرُ عليها بعدَ عَجْزِه عنها، حتى صار مُتواتِرًا لا يُمْكِنُ جَحْدُه. ورُوِىَ من أخْبارِ السَّحَرَةِ ما لا يكادُ يُمْكِنُ التَّواطُؤ على الكَذِبِ فيه.
Ndithudi ndizodziwika pakati pa anthu kuti mwamuna amatha kusiyana ndi mkazi wake (kudzera mu ufiti) iyeyo akakwatira, moti iyeyo amalephera kugonana ndi mkaziyo. Koma matsengawa akachotsedwa, mwamuna uja amayamba kukwanitsa kugonana naye mkazi wake. Izi ndizodziwika kwambiri kotero kuti anthu sangakane (kuti sizimachitika). Pali uthenga wochuluka wokhudza ufiti ndipo ndizovuta kuti anthu agwirizane pa chinthu cha bodza (kuti ufiti kulibe ngati mmene ena amanenera).
Zimatheka ndithu mkazi woyamba kuchitadi matsenga pa mwamuna wake kuti asamakwanitse kugonana ndi mkazi wachiwiri. Kapena mwina mkazi woyambayu kumuchitira matsenga mwamuna wake kuti akamalowa m’nyumba ya mkazi wachiwiriyu, iye azinyansidwa, kukhala wosasangalala komanso kumamuwona mkaziyo kuti sali wofunikanso. Palinso akazi ena, omwe mwamuna angawakwatire pambuyo poti ali ndi mkazi kale, amachita matsenga pa mwamunayu kuti aziwakonda kwambiri kuposa mkazi wake woyamba.
Zonsezi amachita akaziwa ndi kusazindikira ndipo iwo amaikidwa mugulu la ma kuffaar (anthu okanira). Aliyense wochita ufiti amakhala kuti watuluka mu clChisilamu. Tamvani kuyankhula kwake Allaah mu Qur’aan (Suurah Al-Baqarah, 2:102):
وَاتَّبَعُوا ما تَتْلُوا الشَّياطِينُ عَلى مُلْكِ سُلَيْمانَ وَما كَفَرَ سُلَيْمانُ وَلكِنَّ الشَّياطِينَ كَفَرُوا يُعَلِّمُونَ النَّاسَ السِّحْرَ وَما أُنْزِلَ عَلَى الْمَلَكَيْنِ بِبابِلَ هارُوتَ وَمارُوتَ وَما يُعَلِّمانِ مِنْ أَحَدٍ حَتَّى يَقُولا إِنَّما نَحْنُ فِتْنَةٌ فَلا تَكْفُرْ فَيَتَعَلَّمُونَ مِنْهُما مَا يُفَرِّقُونَ بِهِ بَيْنَ الْمَرْءِ وَزَوْجِهِ وَما هُمْ بِضارِّينَ بِهِ مِنْ أَحَدٍ إِلَاّ بِإِذْنِ اللَّهِ وَيَتَعَلَّمُونَ مَا يَضُرُّهُمْ وَلا يَنْفَعُهُمْ وَلَقَدْ عَلِمُوا لَمَنِ اشْتَراهُ مَا لَهُ فِي الْآخِرَةِ مِنْ خَلاقٍ.
Iwo adatsatira zomwe ma Shayaatwiin (asatana) adawapatsa (zonama zokhudza ufiti) mu nthawi ya ulamuliro wa Solomon. Ndipo Solomon sadakanire, koma ndi ma Shayaatwiin amene adakanira, powaphunzitsa anthu ufiti ndipo izi zidafikira ku Babulo pa angelo awiri, Haaruut ndi Maaruut. Koma palibe mwa angelowa amene adaphunzitsa anthu pokhapokha adawauza kuti: “Ife ndi mayesero, choncho musakanire (pophunzira ufitiwu kwa ife). Ndipo kuchokera mwa iwo (angelowa), anthu adaphunzira chomwe chimalekanitsa (kuthetsa banja la) mwamuna ndi mkazi wake, koma iwowo (anthuwo) sadapereke vuto pa aliyense (kuchokera mu ufitiwu) kupatula kudzera mu chilolezo cha Allaah. Ndipo iwo adaphunzira zomwe zimawaononga osati kuwabweretsera phindu. Ndipo ndithudi iwowo ankadziwa kuti ogula ufitiwo sadzakhala ndi gawo m’moyo womwe uli nkudza.
Apa Allaah akutiuza mosapsatira kuti ufiti ndi kufr (kukanira) ndipo amene amauchita ufitiwo ndi kaafir. Ndipo Msilamu yemwe amalimba mtima kuchita izi alibe gawo mu moyo womwe ukubwerawo. Malo ake okakhazikika ndi ku Moto basi.
Choncho, iwowo adziwe kuti ufitiwo sungagwire ntchito pa mwamuna wawo ngati Allaah sadafune. Ndipo mwamuna kungozindikira kuti mkazi wake (kaya ndi woyamba kapena wachiwiri) akuchita ufiti, banja akuyenera kulithetsa chifukwa mkaziyo ndi kaafir.
Ndipo amuna asaope kuti mkazi woyamba achita ufiti akatenga mkazi wachiwiri, komanso mkazi wachiwiri asaope mkazi woyamba kuti amuchitira ufiti. Allaah mu Surah At-Tawbah 9:51, akuyankhula pomuuza Mtumiki Wake (ﷺ) pamodzi ndi Asilamu okhulupirira kuti:
قُلْ لَنْ يُصِيبَنا إِلَاّ مَا كَتَبَ اللَّهُ لَنا هُوَ مَوْلانا وَعَلَى اللَّهِ فَلْيَتَوَكَّلِ الْمُؤْمِنُونَ
Nena: “Palibe chimene chingatichitikire kupatula chomwe Allaah adatilembera; Iye ndi Mtetezi wathu, ndipo kwa Allaah ndi kumene amadalira okhulupirira.”
Pa chifukwa ichi, munthu asalephere kuchita mitala powopa zikhalidwe za awa ochita matsenga ndi ufiti popeza iwowa ndi opanda pake.