Bodza lachiwiri (2/1) 
“Mitala imayambitsa ufiti”
Akazi ena amaopa kuvomera kukhala mkazi wachiwiri, wachitatu kapena wachinayi chifukwa choti adamva zoti mkazi woyamba amachita matsenga kapena ufiti kuti awapatse mavuto akazi amene mwamuna wake angamakwatire. Komanso amuna ena amaopa kukwatira mkazi wachiwiri poganiza kuti mkazi wawo woyamba atha kuwachitira matsenga kapena kuwamwetsa mankhwala oti apepere.
Pa Chisilamu timakhulupirira kuti ufiti ulipo. Izi adayankhula Allaah mu Qur’aan komanso Mtumiki (ﷺ), mu ma ahaadith ochuluka, adaphunzitsa njira zimene munthu angadzitetezere ku ufiti. Tikabwera mu kuyankhula kwake, Imaam Al-Quraafiy mu Kitaab Al-Furuuq lil Quraafiy, (vol. 4, tsamba 149) adati:
السِّحْرُ لَهُ حَقِيقَةٌ وَقَدْ يَمُوتُ الْمَسْحُورُ أَوْ يَتَغَيَّرُ طَبْعُهُ وَعَادَتُهُ، وَإِنْ لَمْ يُبَاشِرْهُ وَقَالَ بِهِ الشَّافِعِيُّ
وَابْنُ حَنْبَلٍ.
Ufiti ulipodi ndipo munthu amene wachitiridwa ufiti (matsenga) atha kumwalira, kapena atha kusintha mmene amachitira zinthu zomanso chikhalidwe chake – angakhale kuti iyeyo sanakhudzidwe. Izinso adayankhula Ash-Shaafi’iy ndi Ibn Hanbal.
Mu kufotokoza kwake, Ibn Al-Qayyim Al-Jawziyyah mu At-Tafsiir Al-Qayyim, tsamba 571 adati:
والسحر الذي يؤثر مرضاً وثقلاً وعقلاً وحبّاً وبغضاً موجود، تعرفه عامة الناس، وكثير من الناس عرفه ذوقاً بما أصيب به منهم.
Ufiti umene umapangitsa anthu kudwala kapena kudandaula, kapena womwe umawapangitsa iwo kukonda angakhalenso kudana ndi chinthu china chake kapena munthu wina wake; ulipo ndithu ndipo ndi wodziwika kwa anthu onse. Anthu ambiri atha kuchitira umboni zomwe ufitiwu umachita.