Nthawi zambiri timakhala tikulimbikira kuchenjeza za bid’ah chifukwa ndi chinthu choopsa mu deen kuposa kuchita tchimo. Msilamu aliyense akuyenera kuidziwa bid’ah mokwanira kuti aipewe.
Komanso monga momwe tikudziwira, cholinga chathu chachikulu ndi kuwongolerana ku Aqeedah ya Mtumiki salla Allah alaih wsallam, zinazo pambuyo. Munthu akuyenera kudziwa malamulo a swalaat, koma ngati Aqeedah yomwe ikusunga swalaatiyo ili yosochera (ngati ali wa bid’ah), swalat yakeyo sidzamuthandiza kalikonse. Ngati mzimai akuvala hijab, akudziwa malamulo onse a hijab koma akuchita shirk, akuchita bid’ah; hijab yakeyo singamupindulire Mchisilamu. Choncho tisamadabwe kuti nthawi zambiri timakamba za Aqeedah (Chikhulupiliro); chifukwa choti munthu adzalowa kumoto ngati adzapezeke kuti Aqeedah yake ndi nyansi zokhazokha ngakhale ntchito zinazo zitalongosoka.
Lero tatiyeni tione kusiyana kwa Al Mubtadi’u (Opeka mu Deen/Wa bid’ah) ndi ‘Aaswi (Ochita Machimo).
Onsewa adzalangidwa. Koma kodi yemwe adzalangidwe kwambiri kuposamzake ndi ndani?
Tikudziwa kuti tchimo ndi chani, komanso ochita tchimo ndi ndani, ndipo tikudziwa kuti tchimo limakhala bwanji. Tikudziwanso kuti bid’ah ndi chani, nanga ochita bid’ah ndi ndani, komanso bid’ah imakhala bwanji.
Tidziwe kuti munthu wa bid’ah ndiye amene adzalangidwe koopsa kuposa wochimwa pazifukwa izi:
a. Bid’ah ndiyoopsa kuposa tchimo. 
b. Shaytwaan amakonda bid’ah kwambiri kuposa mmene amakondera machimo. 
c. Ochita machimo amatha kulapa, kupanga tawbah, chifukwa amadziwa kuti wachimwa. Pomwe ochita bid’ah zimakhala zovuta kuti apange tawbah, chifukwa amakhala akukhulupilira kuti ali mu chilungamo ndipo akuchita chifuniro cha Allah, komanso palibe vuto. Choncho ndi mmene imafalikira bid’ah, zoti ngakhale kumuuza munthu kuti zimenezo ndi bid’ah sizimamveka … na’udhu Billaahi min sharril ma’swiyah wal bid’ah … nchifukwa chaketu ma Ulamaa amakhala akuchenjeza za bid’ah, amakhala akuchenjeza za kukhala pamalo pamene wa bid’ah akupereka ulaliki kapena maphunziro a deen; chifukwa kumeneko kumakhala kufalitsa bid’ah yomwe ndi yoopsa mu deen.
Pa mfundo imeneyi, Imaam Sufyaan Al Thawri rahimahu Allah anati: Bid’ah ndiyokondedwa kwa shaytwaan kuposa tchimo; chifukwa tchimo limachitiridwa tawbah, pomwe bid’ah simachitiridwa tawbah. Musnad bun Al Ja’d (1885), Majmu’ul Fatawa (11/472).
Ananenanso kuti Ndithu Allah amatchinga tawbah ya munthu wa bid’ah Sahiha (1260).
Imaam Al Hasan Al Basri Rahimahullah anati: Usakhale ndi munthu wa bid’ah; chifukwa iye adwalitsa mtima wako (akupatsa matenda ozindikira deen mozondoka). Al I’tiswaam (1/172), Al Bida’u wa Nnahyu Anha (p54).
Kuchokera pa mau a ma Ulamaa ochepa okhawa, komanso ma Ulamaa ena ochokera mma Taabieen ndi ena aposachedwapa, tikumva kuti ndithu bid’ah sichinthu choseweretsa, si zinthu zomadzinyadira pochita, komanso tisanyengelere munthu wa bid’ah aliyense; timudzudzule directly, akatikanika timusiye ndipo tiwachenjeze anzathu za munthu oteroyo moonekera ngati mmene timamuchenjezera munthu za dzenje lomwe liri kutsogolo kwake kuti asagweremo.
Allah atichitire chisoni ndikutiwonetsa njira ya haqq
الأجوبة المفيد عن أسئلة المناهج الجديدة – س5 ص26