Olemba:
Abu Shareef C Hanaqooqee
Mu Qur’aan mulibe chikaiko komanso kutsutsana kwa ndime (ma aayah/ma verse), monga mmene ena amaganizira.
Tisonkhanitsa ndime zimene anthu achikunja ngakhalenso Asilamu anzathu ena amakhala asakuwamvetsa, mpaka amafika pokhulupilira kuti Qur’an imazitsutsa yokha.
Choncho lero tiona ndime zimene zikukamba zoti anthu aku Moto samadzayankhula ngakhale kupereka chidandaulo, ndipo kwa ena zimaoneka kuti zikutsutsana ndi ndime zina zomwe zimakamba zoti anthu a kumoto azidzayankhula motere motere.
Apa pakufunika tifatsepo ndithu kuti timvesetse bwino kusapezeka kwa kutsutsana kwa ndime zimenezi. Koma choyamba
tipereka chitsazo cha ndime izi kuchokera mu Surat Al Mursalaat (35-36):
ﻫﺬﺍ ﻳﻮﻡ ﻻ ﻳﻨﻄﻘﻮﻥ ‏(٣٥‏) ﻭﻻ ﻳﺆﺫﻥ ﻟﻬﻢ ﻓﻴﻌﺘﺬﺭﻭﻥ …
Tanthauzo:  (35) Ili ndi tsiku lomwe sadzalakhula (anthu aku Moto) (36) ndipo sadzapatsidwa chilolezo (choyankhulira) kuti apereke madandaulo awo
Tikaona mu ndime zimenezi, tipeza kuti akusimba za anthu aku Moto kuti kulibe kuyankhula kwa iwo, komaso sazapatsidwa mwayi kuti apereke madandaulo awo.
Izi ndi ndime zomwe zatiuza kuti kulibe kuyankhula. Nanga ndime zina za Qur’an zikuti bwanji?
Tatiyeni tione ndime zochokera mu Surat Al Shu’araa (97-99):
ﺗﺎﻟﻠﻪ ﺇﻥ ﻛﻨﺎ ﻟﻔﻰ ﺿﻼﻝ ﻣﺒﻴﻦ ‏(٩٧) ﺇﺫ ﻧﺴﻮﻳﻜﻢ ﺑﺮﺏ ﺍﻟﻌﺎﻟﻤﻴﻦ ‏(٩٨‏) ﻭﻣﺂ ﺃﺿﻠﻨﺂ ﺇﻻ ﺍﻟﻤﺠﺮﻣﻮﻥ ,
Tanthauzo: (97) Ndikulumbira Mulungu, ndithu tidali mukusokera koonekera. (98) Pamene timakufananitsani ndi Mbuye wazolengedwa. (99) Ndipo sadatisokeretse (aliyense) koma oyipa okha basi (ndamene anatisocheretsa).
Izo ndi ndime zomwe zikusimba mmene adzikanenera anthu aku Moto.
Tisaiwale kuti tikuzama zokhudza kuyankhula anthu aku Moto .. Kodi ndime zimenezi zikutsutsana?
Yankho lake Ayi, sizikutsutsana, ndipo Qur’aan singamazitsutse yokha ngati mmene achikunja amanenera pamodzi
ndi Asilam ena, ndipo sizidzatheka.
Note:
Mu ndime imeneyi kutsogolo kwake, anthu omwewa azanena kuti awonjezereni amenewa (amene adatisocheretsa wa chilango chochuluka).
Tsoka kwa amene amalimbikitsa anthu bidi’a, kuwaphunzitsa anthu kusochera … adzakutchulani komanso kukupempherani moto, chilango chochuluka. Tiyeni tipewe kusocheretsa anthu … Makani tisiye.
Kuchoka mu ndime zimenezi tikupeza mawu omwe adzayankhule anthu amenewa … ndipo zitsanzo za ndime zina ndi zambiri, tiyeni tioneso china apa:
ﺭﺑﻨﺎ هؤﻵﺀ ﺃﺿﻠﻮﻧﺎ … ﺍﻵﻳﺔ
Surat Al A’araf verse 38
Pambuyo pakuti Allah wanena kuti anthu ndi ma jinn onse ochita zoipa adzalowa mu chimbaula (kumoto), adzayakhula: O Allah mbuye wathu awa adatisokeretsa.
.
Za ma aayah amenewa, Imaam Ahmad ﺭﺣﻤﻪ ﺍﻟﻠﻪ anatchula ndime zambirimbiri mu buku lotchedwa ﺍﻟﺮﺩ ﻋﻠﻰ ﺍﻟﺠﻬﻤﻴﺔ ﻭﺍﻟﺰﻧﺎﺩﻗﺔ page 61.
Ndipo ngati tikufuna kudziwa zambiri mmayankho a ndime zina, tikhoza kuona tafseer ya ﺃﺿﻮﺍﺀ ﺍﻟﺒﻴﺎﻥ, mmenemo afotokoza bwino zimenezi.
Yankho la nkhani yathuyi tiyankha kudzera mmagawo atatu;
Gawo Loyamba
loyamba ndilimene Imaam Malik anatiuza kale mu buku lomwe lija. Tiyeni tione mayankho athu, ndipo poyankha zimenezi Imaam Malik anati: “ndithu pa tsiku la Qiyaamah padzakhala anthu ena azidzayankhula, ena samadzayankhula. Pamenepo ndiye kuti kusayankhula kuja kupita kwa awo, ndipo kuyankhula kuja kupita kwa awoso. 
Gawo Lachiwiri
Ndithudi kusayankhula apa akusonyeza kuti sadzayankhula chifukwa kusayankhula kwawo kulibe mphindu.
Gawo Lachitatu
Ndithu iwo adzasiya kuyankhula pamene kudzayankhulidwe kwa iwo kuti: ﺍﺧﺴﺌﻮﺍ ﻓﻴﻬﺎ ﻭﻻ ﺗﻜﻠﻤﻮﻥ … Surat Al Mu’uminuun verse 108.
Allah adzati: khalani chete m’menemo monyozeka, ndipo musandiyankhule.
Apa ndipamene kuyankhula kudzathe. Kusonyeza kuti ndime zina zija zikukamba  kuyankhula komwe azidzayankhula mawu awa
asanayankhulidwe kwa iwo, ndipo ndime zinazo zikukamba kusayankhula komwe Allah waletsa kuti “khalani chete mmenemo ndipo musandiyankhule.” Ndipo kuwiringula kudzathera pamenepo; palibe madandaulo kapena kuyankhula. Ndipo qur’aan yatiuza zimenezi:
ﻭﻭﻗﻊ ﺍﻟﻘﻮﻝ ﻋﻠﻴﻬﻢ ﺑﻤﺎ ﻇﻠﻤﻮﺍ ﻓﻬﻢ ﻻ ﻳﻨﻄﻘﻮﻥ ..
Ndipo mawu onena za kuonongeka adzatsimikizidwa pa iwo chifukwa cha chinyengo chawo (chodzichitira) okha . Ndipo sadzawiringula (sadzayankhula) Surat An Naml verse 85
Ndipo chidzatsale kwa iwo ndi kubuula ngati abulu..
ﻭﻟﻢ ﻳﺒﻖ ﺇﻻ ﺍﻟﺰﻓﻴﺮ ﻭﺍﻟﺸﻬﻴﻖ .
Palibe chidzatsale kwa iwo koma kubuula ngati mmene apangira bulu. (kutulutsa mawu ndikuwabweza).
Umboni wake tione Surat  Hud verse106:
Tsono amene adzakhala kumoto (kobwelera kwake koipa) iwo azakhala kumeneko akufuula potulutsa mawu ndi kuwabweza (ngat kulira kwa bulu).