Kusiyana kwa pakati pa Baibulo ndi Qur’an pa nkhani ya akazi, kukuyamba pamene mkazi abadwa. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti nyengo ya kuyera kwa mayi yemwe wabereka mwana wamkazi kumakhala kotalika kawiri kuyerekeza ndi kubadwa kwa mwana wamwamuna (Levitiko 12:2-5). Baibulo la Chikatolika lafotokoza mosapita mmbali kuti:

“Kubadwa kwa mwana wamkazi ndiko kutaya” (Mlaliki 22: 3).

Pomwe ana amuna amalandira matamando apadera:

“Munthu amene amaphunzitsa mwana wake wamwamuna adzakhala ochitiridwa nsanje ndi mdani wake.” (Mlaliki 30: 3)

Atsogoleri a Chiyuda anaika lamulo kwa amuna a Chiyuda kuti adzibereka ana ochuluka kuti afalitse, koma sanabise pa kukondera kwawo kwa ana achimuna: “Ndzabwino kwa omwe ana awo ndi amuna, koma ndizoipa kwa omwe ana awo ndi akazi”, “Pamene mwana wamwamuna wabadwa, onse amasangalala … pomwe kubadwa kwa mwana wamkazi onse amakhala pachisoni”, ndipo “Mtendere umabwera pamene mwana wamwamuna abwera padziko … ndipo palibe chomwe chimabwera pamene mwana wamkazi abwera.” 7

Mwana wamkazi amaonedwa kuti ndi mavuto owawa komanso amachititsa manyazi atate wake:

“Kodi mwana wanu wamkazi ndi wovuta? Wonesetsani kuti asakuyalutseni kwa adani anu, musakhale okambidwa nkhani paliponse, musakhale ochititsidwa manyazi” (Mlaliki 42:11).

“Musamusiye mwana wanu wamkazi kukhala womasuka kuwopera kuti akuyalutsani” (Mlaliki 26: 10-11).

Chimodzimodzi lingaliro lomweli lochita ana aakazi kukhala gwero la manyazi, linawatsogolera Arabu achikunja Chisilamu chisanabwere, kuti azikwilira ana aakazi amoyo. Qur’an inatsutsa mwambo woipawu, Qur’an 16:58-59:

“Ndipo mmodzi wawo akauzidwa nkhani ya (kuti wabereka) mwana wamkazi, nkhope yake imada, ndipo amadzala ndi madandaulo. Amadzibisa kwa anthu chifukwa cha nkhani yoipa imene wauzidwa (nayamba kulingalira) kodi akhale naye pamodzi ndikuyaluka (pamaso pa Anthu), kapena angomkwirira m’dothi (ali moyo)? Mverani! Ndi choipa kwabasi chiweruzo chawo.”

Qur’an 16:59 Amadzibisa kwa anthu chifukwa chankhani yoipa imene wauzidwa (nayamba kulingalira) kodi akhale naye pamodzi ndikuyaluka (pamaso pa anthu), kapena angomkwirira m’dothi (ali moyo)? Mverani! Ndi choipa kwabasi chiweruzo chawo.”

Chikhalidwe choipa chimenechi chikanavuta kulekeka ku Arabiya Qur’an ikadapanda kuletsa mwamphamvu (16:59, 43:17, 81: 8-9).

Qur’an siyilekanitsa pakati pa mwana wamwamuna ndi wamkazi, monga mmene Baibulo limachitira. Qur’an imaona kuti kubadwa kwa mwana wamkazi ndi mphatso ndi madalitso ochokera kwa Mulungu, chimodzimodzi kubadwa kwa mwana wamwamuna. Pokamba za kubadwa, Qur’an imatsogoza kubadwa kwa mwana wamkazi kenako wamwamuna:

Qur’an 42:49: “Ufumu wakumwamba ndi padziko lapansi ngwa Mulungu; amalenga zimene wafuna; amene wamfuna amampatsa ana achikazi ndiponso amene wamfuna amampatsa ana achimuna.”

Maphunziro a Ana Achikazi