Chipangano Chakale chimalamula kukhala ndi makolo mwa makhalidwe abwino ndipo chimadzudzula omwe samawalemekeza. Mwachitsanzo, “Munthu akatemberera bambo ndi mayi ake, aziphedwa ndithu. Iye watemberera bambo ndi mayi ake. Mlandu wa magazi ake ukhale wa iye mwini.” (Levitiko 20: 9) komanso “Mwana wanzeru ndi amene amakondweretsa bambo ake, koma wopusa amanyoza mayi ake.” (Miyambo 15:20) .

Ngakhale kuti kulemekeza bambo ndi mayi kwatchulidwa malo angapo, mwachitsanzo: “Mwana amakhala wanzeru ngati akulandira malangizo kuchokera kwa bambo ake, kma amene sanamve chidzudzulo amakhala wonyoza” (Miyambo 13: 1); tipeza kuti mayi sanatchulidwe. Sitikupeza chitsindikizo pa kuchitira zabwino mayi, pothokoza malinga ndi kuvutika komwe anavutika nthawi yaitali pakutibereka ndi kutiyamwitsa. Komanso tipeza kuti mayi alibe gawo mu chuma chosiyidwa ndi ana ake, pomwe bambo amalandira.

Ndizovuta kuti tinene motsindika kuti Chipangano Chatsopano chimalimbikitsa kulemekeza mayi. Koma mmalo mwake, tikupeza kuti Chipangano Chatsopano chimawona kuti kusamalira mayi kumalepheretsa njira yofikira kwa Mulungu. Malingana ndi Chipangano Chatsopano, munthu sangakhale Mkhristu wabwino, ngakhale kukhala wophunzira wa Khristu, pokhapokha atadana ndi amayi ake. Izitu zinanenedwa kuti Yesu anati:

“Ngati wina wabwera kwa ine, koma osadana ndi bambo ake, mayi ake, mkazi wake, ana ake, abale ake ndi alongo ake, ngakhale moyo wake umene, sangakhale wophunzira wanga” (Luka 14:26). 42

Komanso, Chipangano Chatsopano chikuwonetsera chithunzi cha Yesu kuti anali wosayamika mayi ake enieni. Mwachitsanzo, pamene anapita kukamufunafuna pamene anali kulalikira kwa gulu la anthu, sanasamale zoti mayi ake akumufunafuna:

Tsopano panafika mayi ake ndi abale ake, ndipo anaimirira kunja, ndi kutumiza mthenga kukamuitana. Iye anali ndi khamu la anthu litakhala momuzungulira, ndipo anthuwo anamuuza kuti: “Mayi anu ndi abale anu ali panjapa, akukufunani.” Koma iye anawayankha kuti: “Mayi anga ndi abale anga ndani?” Kenako anayang’ana onse amene anakhala pansi momuzungulira aja, ndi kunena kuti: “Onani! Mayi anga ndi abale anga ndi awa. Aliyense wochita chifuniro cha Mulungu, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mayi anga.” (Maliko 3: 31-35)

Mwinatu wina akhonza kunena kuti Yesu anali kuyesera kuphunzitsa anthu phunziro lofunika kuti maubwenzi achipembedzo ndi ofunika kwambiri kuposa chiyanjano cha banja. Komabe, akanatha kuphunzitsa omvera ake phunziro lomwelo popanda kusonyeza kuti alibe chidwi ndi mayi ake. Mtima wosayamika womwewo unasonyezedwa pamene anakana kuvomereza mawu a womvera ake pamene anali kuyamikira udindo wa mayi ake pomubereka ndi kumusamalira:

Pamene anali kunena mawu amenewa, mayi wina mkhamu la anthulo anafuula nkumuuza kuti: “Ndi wodala mayi amene mimba yake inanyamula inu ndiponso amene munayamwa mabere ake!” Koma iye anati: “Ayi, mmalomwake, odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!” (Luka 11: 27-28)

Ngati mayi wolemekezeka koposa, yemwe ndi Maria, adakanidwa kuchitiridwa zabwino ndi mwana wake weniweni yemwe ndi Yesu, monga momwe Chipangano Chatsopano chikutiwonetsera, kodi nanga amayi a Chikhristu wamba angachitidwe bwanji ndi ana awo?

Mu Chisilamu, ulemu kwa mayi sungalekanitsidwe; Qur’an inaika kufunika kwa kuchitira zabwino makolo onse awiri pambuyo pa kupembedza Mulungu Mmodzi  Wamphamvu zonse:

Quran 17:23: “Ndipo walamula Mbuye wako kuti musapembedze (wina) koma Iye yekha, ndi kuti muchitire zabwino makolo (anu). Ngati mmodzi waiwo afika msinkhu waukalamba uli naye, kapena onse awiri, usawanenere mawu amnyozo ndiponso usawakalipire koma yankhula nawo ndi mau aulemu. Ndipo afungatire ndi phiko lodzichepetsa powachitira chisoni, ndipo nena: “Mbuye wanga achitireni chisoni (makolo anga) monga momwe ankandilerera ku ubwana.”

Qur’an yagogomezera kwambiri udindo wa amayi pakubereka ndi kuyamwitsa:

Qur’an 31:14: “Ndipo tamulangiza munthu kwa makolo ake (kuwachitira zabwino) adamsenza (pathupi) mayi wake ali wofooka pamwamba pakufooka. (Adamuyamwitsa) ndi kumusiyitsa patapita zaka ziwiri. Ndithokoze ine ndi makolo ako, kwa ine nkobwerera.”

Kulemekezeka kwa mayi kwapadera kunatchulidwa ndi Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam momveka bwino: “Munthu wina anafunsa Mtumiki kuti: ‘Ndindani yemwe ndikuyenera kulemekeza kwambiri?’ Mtumiki anati: ‘Amayi ako’. Munthuyo anafunsa: kenako ndai: Mtumiki anati: ‘Amayi ako’. Munthu anafunsanso: kenako ndani: Mtumiki anati: ‘Amayi ako!’ Munthuyo anafunsanso: kenako ndani? Ndipo Mtumiki anati: ‘Bambo ako”(Bukhari ndi Muslim)

Zina mwa ziphunzitso za Chisilamu zomwe Asilamu amadzigwiritsa ntchito mpaka lero lino, ndi kuchitira zabwino ndikulemekeza amayi. Ulemu umene amayi a Chisilamu amalandira kuchokera kwa ana awo aamuna ndi aakazi, ndi ulemu wa chitsanzo chabwino. Ubale wachikondi pakati pa amayi a Chisilamu ndi ana awo, komanso kulemekeza kwakukulu kumene ana amachitira amayi awo, kumawadabwitsa anthu a Kumadzulo.

Ulowammalo wa Mkazi pa Chuma Chosiyidwa