Kulibwino kumangomva mbiri ya Al Mu’ayidiyy, kusiyana ndikumuwona
تسمع عن المعيدي خير من أن تراه
Umenewu ndi mwambi wa kalekale pakati pa ma Arabs munthawi ya umbuli Mtumiki asanabadwe. Ndipo anayankhula Al Nu’man bun Al Mundhir (yemwe anali mfumu pa nthawiyo), pomunena Shuqqat bun Dhwamrah bun Dhwamrah Al Nahshaliy.
Dhwamrah anali shaa’iru (mlakatuli), anali odzichepetsa, koma wanzeru wamphamvu ndipo odziwa ndale za nkhondo…anali kulimbana ndi asilikali a Mundir. Pamene Mundir anamulephera, anaona kuti angomutenga, choncho amulembera kuti alowe mu ulamuliro wake akhale mmodzi mwa anthu ake, koma anakana. Anamunyengelera ndi ngamira 100 mpaka analola. Atamuitana kunyumba kwake nkumuwona, sanakhulupilire mmene amaonekera; anali wa maonekedwe apansi kwambiri ndipo zovala zake zinali za simple osagwirizana ndi momwe mbiri yake inamvekera, komanso maonekedwe a thupi lake anali osasangalatsa.
Ndipamene Mundhir anati: 
“تسمع بالمعيدي خير من أن تراه” 
“Kulibwino kumangomva za Al Mu’aidiyy (Dhwamrah), kusiyana ndikumuwona”
Mauwa akutanthauza kuti mbiri yake pakati pa anthu inali yamphamvu osafanana ndi maonekedwe ake. Dhwamrah anadandaula pa zomwe zinayankhulidwazo, komabe anayankha mwa hikma kuti: “E Mfumu, dekhani; dziwani kuti munthu sakuyenera kuweruzidwa chifukwa cha maonekedwe ake, munthu sali ngati ng’ombe kapena mbuzi yomwe mumayang’ana kunenepa kwake kuti mudziwe ubwino wake… chofunika kwambiri kuwona pa moyo wa munthu aliyense ndi zomwe zikuchokera mumtima mwake komanso mu lirime lake”.
Mfumu ija inasangalatsidwa ndi mau a hikma omwe anatulutsa Dhwamrah ndipo anaona kuti akhonza kupindula naye akamutenga kukhala mulangizi wake.
Mwambi umenewu umanenedwa kwa munthu yemwe anthu ambiri ankangomva za iye koma sanamuonepo; chifukwa choti amaganiza kuti mbiri yakeyo ikuyendera limodzi ndi maonekdwe ake komanso sangakhale opanda chuma.
Al  Nu’man bun Al Mundhir anali Mfumu yomaliza mu Ufumu wa Al Manaadhira (Lakhmid Kingdom) ya ma Arabs mzaka za mma 582-602CE ndipo anali kutchuka ndi dzina loti Abu Qaabus. Anali wa chikhristu (Nestorian Christian Arab). Izi zikuchokera mu
أنساب الأشراف للبلاذري
Phindu Kuchokera mu Nkhaniyi:
Khalani ngati Mu’aidiyyu ndipo mupewe kukhala ngati Qaarun – yemwe anali ndi chuma, makiyi a nkhokwe zake amachita kunyamulitsana anthu amphamvu zawo … tawerengani Surat A Qasas aayah 76:
إِنَّ قَارُونَ كَانَ مِن قَوْمِ مُوسَى فَبَغَى عَلَيْهِمْ وَآتَيْنَاهُ مِنَ الْكُنُوزِ مَا إِنَّ مَفَاتِحَهُ لَتَنُوءُ بِالْعُصْبَةِ أُولِي الْقُوَّةِ إِذْ قَالَ لَهُ قَوْمُهُ لَا تَفْرَحْ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ الْفَرِحِينَ
“Ndithu Qaarun adali mwa anthu a Musa; koma adadzikweza kwa iwo, ndipo tidampatsa nkhokwe za chuma zomwe makiyi ake ngolemetsa (kuwatsenza) kagulu ka anthu anyonga. Anthu ake adamuuza: “usanyade, ndithu Allah sakonda onyada”.
Nkhaniyi si nthano chabe, koma inachitikadi ndipo imakambidwa pofuna kuphunziramo mmene tingamakhalire monga Asilamu owopa Allah pa zomwe watipatsa. Ngakhale inachitika munthawi ya umbuli, ife tikufuna phunziro pa makhalidwe a umunthu. Tikaonesetsa, tipeza kuti Al Mu’aidiyyu anali munthu wa simple, wopereka mwamtima wonse, ndipo sanadzikundikire chuma chake, koma anali kupereka mowolowa manja, choncho analibe nthawi yodzikongoletsa ndikudzikhutitsa pa dziko. Kusiyana ndi Qarun yemwe Allah anamudalitsa ndi chuma, koma anali kutenga nthawi pa dziko povala zovala zomutchukitsa, zamtengo wapatali zoti munthu wamba sangagule, anali kusungira golide wambiri koma kwa anthu ake anali opondereza, omana, odzikweza komanso ofuna kutchuka. Sanamvere malangizo a anthu ake, mapeto ake Allah anailamula nthaka kuti imumeze pamodzi ndi chinyumba chake chomwe anali kunyadiracho.
Nanga inuyo malinga ndi mmene Allah wakudalitsirani, mukufuna mutakhala ngati ndani? Musazizunze ndi maonekedwe anu kuti mupange attract maso ndi mitima ya anthu pokusimbani ndi ubwino, musawapange maonekedwe anu kukhala ofunikira pakati pa anthu. Mukhonza kumulemekeza munthu chifukwa cha mmene mwamuonera thupi lake ndi zovala zake kapena katundu yemwe ali naye, koma simukudziwa mwina kwa Allah ndi onyozeka chifukwa Iye amayang’ana za muntima ndi ntchito ya munthu, osati maonekedwe a thupi. Mukhonza kumamuona onyozeka mmaso mwanu malinga ndi thupi lake komanso zomwe ali nazo, koma simukudziwa kutheka kwa Allah ndi olemekezeka komanso olemera. Allah akunena mu Surah Al Hujuraat aayah 11 kuti:
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آَمَنُوا لَا يَسْخَرْ قَومٌ مِنْ قَوْمٍ عَسَى أَنْ يَكُونُوا خَيْرًا مِنْهُمْ وَلَا نِسَاءٌ مِنْ نِسَاءٍ عَسَى أَنْ يَكُنَّ خَيْرًا مِنْهُنَّ وَلَا تَلْمِزُوا أَنْفُسَكُمْ وَلَا تَنَابَزُوا بِالْأَلْقَابِ بِئْسَ الِاسْمُ الْفُسُوقُ بَعْدَ الْإِيمَانِ وَمَنْ لَمْ يَتُبْ فَأُولَئِكَ هُمُ الظَّالِمُونَ
“Ee inu amene mwakhulupilira, amuna asanyoze amuna anzawo; mwina (onyozedwawo) nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Nawonso akazi asanyoze akazi anzawo; mwina onyozedwa nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Ndipo musatukwanizane pokumbana mitundu kapena kuitanana maina oipa. Taonani kuipa komuitanira munthu ndi dzina loti fassiq (wotuluka mmalamulo a Allah) kumachita atakhulupilira kale; ndipo amene salapa (kuzimenezi), iwo ndiwo (ochimwa) odzichitira okha chinyengo.”
Nkhani ikuchokera kwa Abdillah bun Mas’ud radhia Allah anhu, yemwe anati Mtumiki salla Allah alayh wasallam anati:
لا يدخل الجنة من كان في قلبه مثقال ذرة من كبر. فقال رجل: إن الرجل يجب أن يكون ثوبه حسناً ونعله حسنة ، فقال عليه الصلاة والسلام: «إن الله جميل يحب الجمال ، الكبر: بطر الحق وغمط الناس». أي: إن تحسين المظهر واللباس ليس من التكبر المذموم، بل إن المذموم هو احتقار الناس والاستخفاف بهم.
“Sadzalowa ku Jannah yemwe mumtima mwake mudzapezeke kudzikweza kolemera ngati kanjere kakang’ono” Munthu wina anati: “komatu munthu amayenera kuvala zovala ndi nsapato zabwino,” Mtumiki anati: “ndithu Allah ndi wokongola, amakonda zokongola. Kudzikweza (komwe ndikunena apa) ndi kukana chilungamo komanso kunyoza anthu”. 
Kutanthauza kuti kuvala zovala zokongola, kudzisamalira pathupi, sikuli mgulu la kudzikweza, potinso ndi zomwe Allah amakonda. Koma zikakhala kuti munthu akupanga zimenezo ponyoza ena kuwaona ngati apansi, kapena zikumpagitsa kudelera malamulo a Chislamu poona kuti ali ndi chirichonse, kumeneko ndiye kudzikweza komwe sakalowa nako munthu ku Jannah.
Musamutchule mzanu ndi dzina lomwe amadana nalo:
Zinafalikira pakati pathu, ndipo ndi mmene moyo ukuyendera masiku ano…timapatsana zimaina  komanso ma _nickname_ omwe osakhala bwino; amalongosola zomwe otchulidwayo samasangalatsidwa nazo, monga maonekedwe a thupi lake, ndipo mainawa amaperekedwa poselewula.
Allah Ta’ala ndiye anatiletsa mchitidwe woterowo mu aaya yomwe taimva ija, komanso analonjeza chilango choopsa kwa anthu otero, mu Surah Al Humazah aayah 1:
 وَيْلٌ لِّكُلِّ هُمَزَةٍ لُّمَزَة
Kuonongeka koopsa kudzampeza aliyense wojeda ndi wonyoza anthu polozera (ndi maso kapena kuyankhula ndi lirime)
Waylu (Al Waylu) ndi chilango kapena dambo la ku Jahannam lomwe adzamiremo aliyense onyoza anthu ena
Kuyambira pamayambiliro mpaka pamapeto pa nkhaniyi, tatolapo maphunziro osiyanasiyana, ndipo zili ndi ife kusankha phunziro lomwe lingatipindulire mu deen yathuyi.
Allah atichitire Chifundo ndikutipanga kukhala olemekezeka pamaso pake ngakhale titanyozeka pamaso pa anthu, kuti adzasangalale nafe potilandira ndi chiweruzo cha mtengo wapatali.