Pachifukwa chakuti Chipangano Chakale sichidawaganizire akazi powapatsa ufulu wa gawo la chuma chosiyidwa, iwo anali mwa anthu ovutika kwambiri mwa Ayuda. Amuna onse omwe amatenga gawo la chuma chonse amayenera kuwagawira akazi kuchokera mu chumacho, komabe akaziwo analibe ufulu woonesetsa kuti akupeza kanthu kuchokera kwa amunawo, kotero kuti anali kudalira chifundo cha anthu ena. Zonsezi mapeto ake ndi oti amayi amasiye amakhala onyonzeka kwambiri mugulu la ma Israel kalelo, ndipo umasiye wotero unali ngati chizindikiro cha kuchepetsedwa ndi kunyozeka. (Yesaya 54: 4). 46

Malinga ndi chikhalidwe chochokera m’Baibulo, umasiye wa mkazi umakhala wopitilira kuwonjezera pa kusalidwa kwake pa katundu wosiyidwa ndi mwamuna wake. Ndipo malinga ndi Genesis 38, mkazi wamasiye (yemwe mwamuna wake wamwalira) ndipo saanamusiyire mwana, ayenera kukwatiwa ndi mchimwene wa mwamuna wake yemwe wamwalirayo, ngakhale mchimweneyo atakhala kuti ali ndi mkazi wina kale; ncholinga choti dzina la mchimwene wake uja lisafe. 47 “Yuda ataona zimenezi anamuuza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa m’bale wako ndipo uchite chokolo, kuti um’berekere ana m’bale wakoyo.” (Genesis 38: 8).

Limenelo ndi lamulo ndipo sizikufunika kudikira kuti mkaziyo avomereze. Mkazi wamasiye amatengedwa kuti  ndi gawo la chuma cha mwamuna wake wakufa yemwe ntchito yake yaikulu ndi kupitiriza m’badwo wa mwamuna wake. Lamulo limeneli (kulowa chokolo) likupitilirabe mu Israeli mpaka lero. 48

Mkazi wamasiye wa mu Israel opanda mwana, amaperekedwa kwa mchimwene wa mwamuna wake yemwe wamwalira. Ndipo mchimweneyo ngati ali wochepa msinkhu moti sinakwanire nthawi yokwatira, amadikira kuti akule, ndipo ngati angakane kukwatira mkazi wa malemu achimwene akewo (kulowa chokolo) ndiye kuti mkaziyo amapatsidwa ufulu wokwatiwa ndi mwamuna aliyense yemw e wamfuna. Sizodabwitsatu ku Israeli, kuti akazi amasiye amaopsezedwa ndi azilamu awo achimuna kuti apeze ufulu, powakwatira.

‘Ndipo tikaonesetsa, zikhalidwe zambiri zomwe zikulongosoledwa mu bukumu kuti zinayambira komanso zimachitika pakati pa Ayuda, ndizomwenso anthu ena omwe sali Ayuda amadzigwiritsa ntchito lero lino, zikhalidwe za umbuli komanso zopondereza’

Aarabu achikunja anali ndi chikhalidwe chomwechi, ‘poti nawo anali oyandikira kwambiri ndi Ayuda Qur’an isanatsike asanakhale ndi zofanana‘; Mkazi wamasiye anali gawo la chuma cha mwamuna wake kuti adzatenge abale ake achimuna, ndipo kawirikawiri anali kuperekedwa kwa mwana wamwamuna wamkulu wa bambo omwalirayo, yemwe anabadwira mwa mkazi wina ‘(mwana wobadwira mwamkazi wa kumitala, amaperekedwa kuti akwatire mkazi winayo (mwana kukwatira step-mother wake)’ . Koma Qur’an itatsika, inawopseza ndikuphwasula mchitidwe wonyansawu:

Qur’an 4:22: Ndipo musakwatire akazi amene adakwatiwapo ndi atate anu, kupatula zomwe zidapita, (musabwerezenso kuzichita). Ndithudi, chinthu ichi nchauve ndipo nchodedwa ndiponso ndinjirayoipa.

Akazi amasiye ndi akazi osudzulidwa anali kunyozeka kwambiri muchikhalidwe cha Baibulo, moti mkulu wa Ansembe sankaloledwa kukwatira mkazi wamasiye kapena wachiwerewere:

“Mkulu wa ansembe akafuna kukwatira, azikwatira namwali. Asakwatire mkazi wamasiye kapena amene mwamuna wake anamusiya ukwati komanso mkazi amene wataya unamwali wake kapena hule; koma azikwatira namwali pakati pa anthu amtundu wake. Asaipitse ana ake pakati pa anthu amtundu wake…” Levitiko 21:1-4

Lero lino mu Israeli, mbadwa ya Cohen caste (ansembe aakulu a nthawi ya Kachisi) sangakwatire osudzulidwa, wamasiye, kapena wachigololo. Mmalamulo a Chiyuda, mkazi yemwe wakhala wamasiye katatu, ndipo amuna onsewo akhala akumwalira imfa yachilengedwe, amatengedwa kuti ndi mkazi wakupha, choncho amaletsedwa kukwatiwanso kuwopera amuna angamangofa. 50

Komatu Qur’an simaona zimenezo. Akazi amasiye ndi osudzulidwa ali ndi ufulu wokwatiwa ndi aliyense amene wamusankha. Palibe chiopsezo chilichonse chomwe chimalumikizana ndi kusudzulidwa kapena kumwalira kwa mwamuna wake:

Qur’an 2:231: Ndipo pamene musiya akazi powanenera mawu achilekaniro, niiyandikira kukwana nyengo yachiyembekezero chawo (edda yawo), abwerereni mwaubwino; kapena lekananaoni mwaubwino, ndipo musawabwerere mowavutitsa kuti mupyole malirea Mulungu (poswa malamulo ake). Ndipo amene achite zimenezo ndiye kuti wadzichitira yekha zoipa. Ndipo ndime za mawu a Mulungu musazichitire chibwana.

Qur’an 2:234: Ndipo mwainu amene amwalira nasiya akazi, choncho (akaziwo) ayembekezere (asakwatiwe) miyezi inayi ndi masiku khumi. Ndipo akakwanitsa nyengo ya chiyembekezero chawo cha edda, sitchimo kwa inu pazimene akaziwo adzichitira okha (monga kudzikongoletsa ndi kudziwonetsa kwa ofunsira ukwati); komabe zikhale motsatira mmalamulo a Shariya. Ndipo Mulungu Ngodziwa zonse zimene mukuchita.”

Qur’an 2:240: “Ndipo mwainu amene amwalira nasiya akazi awo,alangize (amlowam’malo awo) za akazi awo kuti awapatse zodyera m’nyengo yachaka chimodzi popanda kutulutsidwa (m’nyumba zomwe ankakhala ndi amuna awo). Koma ngati akazi wo atuluka (okha), palibe kulakwa painu pazimene adzichitira okha zomwe nzogwirizana ndi chilamulo cha Shariya. Ndipo Mulungu Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.”

Mitala