HUSAIN .. MADAD YA HUSAIN .. YA HUSAIN !!

Nchifukwa chani ma Shia amatamanda ndi kulemekeza Husain (رضي الله عنه) yekha ndi kusiya ana ena onse a Ali (رضي الله عنه)?

Kodi munayamba mwadzifunsapo funso limeneli?

Nanga nkhani imeneyi inayamba yakudabwitsanipo?

Ndisanayankhe mafunso amenewa, dziwani lero izi: Ali bun Abi Talib, anali cousin wa Mtumiki ﷺ chifukwa Abu Talib anali amalume a Mtumiki ﷺ. Ndipo Ali anakwatira Fatimah, mwana wa Mtumiki ﷺ ndikubereka mapatsa (Hasan ndi Husain) ngati ana oyamba mwa ana 11. Choncho Ali anali ndi ana ambiri osati Husain yekha, koma izi ambiri sadziwa.

Tiyeni tiwadziwe lero ana a Ali (رضي الله عنه) onse mwatsatanetsatane:

1) Hasan (الحسن)
2) Husain (الحسين)
3) Muhsin (المحسن)
4) ‘Abbaas (العباس)
5) Hilaal (هلال)
6) ‘Abdullah (عبدالله)
7) Ja’far (جعفر)
8) ‘Uthmaan (عثمان)
9) ‘Ubaydullah (عبيدالله)
10) Abubakr (أبو بكر)
11) ‘Umar (عمر)
Awa ndi ana omwe Ali (رضي الله عنه) anabereka.

Kodi munayamba mwaonapo ma Shia akulemba mma scarf awo “Ya Abbaas” kapena “Ya Hasain” kapena “Ya Muhsin”?
Ayi ndithu sitinawonepo akulemba izi.

Nanga ndichifukwa chani ma Shia amangoti “Ya Husain”, komanso amachita istighaatha (kupempha chithandizo) kwa Husain koma osati Hasan, kumachita kuti ndizodziwika kuti Hasan ndi Husain anali mapatsa aku banja lolemekezeka la Mtumiki ﷺ?
Chifukwa chani kusankha Husain yekha?

Tisanayankhe mafunso amenewa ndikugawireni uthenga uwu wopatsa chidwi:

Ma Shia ali ndi ma Imam 12 omwe amawakhulupilira ndikuwalemekeza kufika powachita ngati Atumiki a Allah, ndipo amati iwowo alibe machimo. Mukudziwa kuti ma imam onsewo ndi ana ochokera mwa Husain (رضي الله عنه)?

Kodi pamenepa kapena ana onse a Ali tawatchula aja ana awo anali osaphunzira?

NDICHIFUKWA CHANI MASHIA AMATAMANDA HUSAIN YEKHA KUSIYA ANA ONSE A ALI?

Husain (رضي الله عنه) anakwatira mkazi wa chi Persia (wa ku Iran), yemwe anali mwana wa Mfumu Kisra, wochokera mu Sasanian Empire Yezdagerd (Yazdajerd) wachitatu. Ndipo mkazi ameneyu dzina lake linali Shahrbanu, kapena Shahrabanu (Sheherbaanu) malingana ndi malembedwe osiyanasiyana. Dzina limeneli ndi lachi Farsi kapena kuti chi Persian lomwe limatanthauza kuti The Lady of The Land.

Anthu awa anali makafir omwe anali kupembedza mafano monga Mazda. Apa mpomwe ena anatengera dzina la Company yopanga magalimoto loti Mazda. Magalimoto a Mazda. Limenelo ndi dzina la fano lomwe anthu aku Iran Persian anali kupembedza.

Analinso ndi mulungu wina Ahura (Ahura Mazda) yemwe ankakhulupilira kuti ndiye mulungu amene amapereka moyo, amalenga.

Munthawi yomwe Asilamu analowa ku Iran, anamenyana ndi Kingdom ya Kisra Yazdagerd wachitatu mpaka anaigonjetsa ndipo anatenga ena mwa anthu ngati akapolo.
Imeneyitu inali nthawi ya utsogoleri wa ‘Umar bun Al-Khattaab (رضي الله عنه).

Mkati mwa akapolo omwe anagwidwa aja munali mtsikana wotchedwa Shahrbanu mwana wamfumu Kisra. Ndipo ‘Umar (رضي الله عنه) anatenga mtsikanayu namupatsa Husain (رضي الله عنه) kuti amukwatire, ndipo anamukwatiradi.

Ndikhulupilira tsopano tadziwa pamene pakuchokera kulemekezeka kwa Husain kuposa Hasan ndi azichimwene ake onse.
Husain atakwatira mtsikanayu, anabereka ana 12, omwe ndi ma imam olemekezeka kwambiri kwa ma Shia.

Choncho amanama kuti amakonda aku Banja la Mtumiki ﷺ … izi sizoona ayi… Zoonazake ndizoti ma Shia amakonda akubanja la Mfumu Kisra, kafir wopembedza mafano yemwe ndi gogo wa ma imam awo 12 !! osati zoti amakonda agogo ake a Husain (رضي الله عنه) womwe ndi Mtumiki ﷺ!!

Akanakhala kuti amakondadi akubanja la Mtumiki ﷺ bwenzi akukonda ndikulemekeza anthu onse akubanja la Mtumiki ﷺ sakanapatula, kuyambira mkazi wake Aisha.

Inu simudabwa amangoti Ahlu Bayt (Abale a ku Nyumba) samapitiriza kuti Ahlu Bayti Nnabiy (Abale a ku Nyumba ya Mtumiki) chifukwa chani???

Indetu, iwo samanama, ndi Ahlu Bayt Kisra, gogo wa ma Imam awo aja 12 osati Ahlu Bayt a Mtumiki ﷺ gogo wa ana 11 a Ali ndi Faatimah رضي الله عنهم.

Nkhanizi muzipeza ndi ibn Katheer mu:

البداية والنهاية (Albidayah Wannihayah) Vol. 9

Al-Tabari – Dalaailul Imaamah p.194

Al-Kaafi (Usool) vol.1 p.297m’chaka

Mu Al Bidaayah wa Nnihaayah anati:

[[Ibn Khalkan ananena kuti Ummu Salamah anali mmodzi mwa ana achikazi a Yazdagerd mmodzi mwa mafumu achi Faris (Persian). Ndipo Al Zamakhshariyy (الزمخشري) analongosola mu buku lake lotchedwa (ربيع الأبرار) “Rabi’ul Abraar” kuti Yazdagerd anali ndi akapolo achikazi atatu mu nthawi ya utsogoleri wa ‘Umar (رضي الله عنه), ndipo Asilamu atagonjetsa ufumu wa Yazdagerd analanda akapolo amenewa nawapereka kwa ‘Umar. ‘Umar (رضي الله عنه) anawamasula akapolowa ndipo mwa atsikana omwe analipo anatenga mmodzi ndikumpatsa mwana wake Abdullah (رضي الله عنه) kuti akwatire. Mmenemo Abdullah bun Umar anabereka naye mwana wotchedwa Salma.

Ndipo mtsikana wina anampatsa Muhammad mwana wa Abubakr Siddeeq (رضي الله عنه) kuti amukwatire, ndipo anabereka naye mwana wotchedwa Qassim.

Ndipo mtsikana wachitatu anampatsa Husain mwana Alie (رضي الله عنه) kuti amukwatire, ndipo anabereka naye Ali Zainul Abdeen … Ana onsewo anali adzukulu a mfumu Yazdagerd yachi Persian.]

Tsopano atsogoleri (ma Imaam) a chi Shia aja omwe amawatamanda ndikuwayeretsa kwambiri omwe amafika pa level ya kulemekezeka kwawo ngati Atumiki ndi aneneri a Allah ﷻ, amakhulupilira kuti ndi ma’asumoon (opanda ma chimo), onsewo ndi ana a Husain omwe anaberekera kwa mkazi ameneyo (Shahrbanu).

Ma Shia amakonda Husain (رضي الله عنه) kwambiri komanso ma Imaam awo 12 aja chifukwa choti iwo amati muli magazi awo a chifumu cha chi Persian (Iran) mwa ma Imaam amenewa, chifukwa ndi ana ochokera kwa mkazi wachifumu Kisra Yazdagerd yaku Iran.

Pachifukwa ichi amakonda zidzukulu za chifumu Kisra, kafir amene anali kupembedza mafano ngati mmene talongosolera kale.
Akanakhala kuti amakonda Husain chifukwa choti ndi mzukulu wa Mtumiki, bwenzi akulemekeza akunyumba kwa Mtumiki kuyambira Aaisha radhia Allah anha (Mai wa Okhulupilira).

Awuzeni lero anthu zoona kuti ma Shia amakonda aku banja la Kisra Yazdagerd mfumu ya chi Persian osati aku Banja la Mtumiki ﷺ ngati mmene iwo amanamira.

Musangowerenga nokha uthengawu komanso aphunzitseni ma Shiatu Raafidhah – ambiriwotu sadziwa zoona amangotsatira, chilungamo chake sachidziwa.

Aphunzitseninso Asilamu anzanu adziwe choonadi, awadziwe kuti ma Shia ndi ndani.