Kalelake kwambiri, Allah Subhannahu wa Ta’la analenga dzuwa, mwezi ndi nthaka. Pambuyo pake anaona kuti zolenga zake sizikukwanira.Choncho anawatuma Angelo ake kuti atenge dothi pa dziko. Angelo aja anamvera ndipo anapititsa dothi kwa Allah lomwe analengera chinthu nachitchula kuti Adam alaih salaam.Koma chinthuchi chinakhala zaka 40 osayendayenda, chinangoima basi.Pamene Iblis anachiona chinthuchi, anali odabwa ndi mantha.

Tsiku lina patatha zaka 40, Allah anaika mzimu mwa Adam.Pamene mzimu unafika kumutu kwake anayetsemuna.Mzimu utafika mmaso mwake, anaona mitundu yonse yodabwitsa ya chakudya.Kenako mzimu utafika mmimba mwake, anamva njala.Mtumiki Adam anaona zipatso zili paliponse, ndipo mzimu usanafike mmyendo mwake, anadumphira zipatso.Adam alaih salaam anagwa poti sankatha kuyenda ndi myendo yake.

Kenako Allah anawalamula Angelo onse ndi Iblish kuti amugwadire Adam alaih salaam pomulemekeza.Angelo onse anamugwadira Mtumiki Adam kupatula Iblis.

Iblis anati iye anali bwino kuposa Adam chifukwa analengedwa kuchokera ku moto. Allah anakwiya ndi Iblis ndipo anamuthamangitsa Munda waMtendere. Kuyambira pamenepo Iblis anatchedwa kuti shaytwaan (satana) ndipo anaponyedwa ku Moto. Kuyambira pamenepo shytwaan anakwiya ndi anthu pothamangitsidwa ku Mtendere chifukwa cha iwo, ndipo analonjeza kuti adzabwezera powasocheretsa anthuwo.

Kenako Allah anamuphunzitsa Adam maina azinthu zonse; mkango, giraffe, ngamira, nkhunda ndi zina zonse.

Allah anamuuza Adam kuti akhonza kudya chipatso chirichonse mmundamo, kupatula chimodzi. Anamuuza kuti asadye kuchokera mumtengo wa kuzindikira.

Adama anali kusewera ndi zinyama nthawi zonse ku munda wa Mtendere.

Patadutsa zaka zingapo, Adam anasungulumwa poti kunalibe munthu wina aliyense. Allah Subhaanau wa Ta’la ataona izi anaganiza zompatsa Adam mkazi.

Pamene Adam anagona usiku wina, Allah analenga mkazi woyamba.Adam atadzuka anali osangalala kuona mkazi ndipo anamutchula kuti Hawaa, kutanthauza kuti analengedwa kuchokera mu chamoyo. Awiriwa anakhala mosangalala mmunda wa Mtendere kwanthawi yaitali. Koma satana anali okwiya kwambiri ndi anthu aja. Zaka zambiri zinadutsa ndipo satana anadziwa kuti munthu uja kutheka anaiwala mau a Allah aja. Tsiku lina, analingalira mmene angamusokonezere Adam kuti athamangitsidwe Mmunda wa Mtendere muja. Anafika Mmunda muja ndikumunyengelera Adam ndi mkazi wake kuti adye chipatso choletsedwa. Adam ndi mkazi wake mosazindikira anatchola chipatso ndikuyamba kudya, koma asanamalize kudya chipatso chija, anazindikira kuti anachita tchimo lalikulu ndipo anali odandaula komanso manyazi.

Pambuyo pakudya chipatso choletsedwa, anazindikira kuti anali maliseche ndipo anadziphimba ndi masamba; tsopano anali ndi mantha poti anadziwa kuti Allah adzawalanga chifukwa cha kusamvera.

Pamene Allah Subhaanah wa Ta’la anadziwa izi, anakwiya …anakwiya, moti Adam ndi mkazi wake anatulutsidwa Mmunda wa Mtendere.

Adam ndi mkazi wake anayenda kwa nthawi yaitali mpaka anakhala pafupi ndi mtsinje.

Adam anadziwa kuti moyo padziko ukakhala ovuta kwambiri; adzayenera kumanga nyumba yokhalamo, komanso kulimbikira ntchito kuti adyetse banja lake, ndipo analibenso mwayi wosangalala ku mundawa Mtendere.

Patadutsa zaka zochepa Hawwaa anabereka mapatsa, mwamuna ndi mkazi.Wamwamuna anamutcha Qaabil.Kenako anabereka mapatsa ena chimodzimodzi mwamuna ndi mkazi, ndipo wamwamuna anamutcha Haabil.

Haabil ndi Qaabil anakula, ndipo Qaabil anali Mlimi pomwe Haabil anali m’busa wa nkhosa.

Pamene Haabil ndi Qaabil anakula, Adam anafuna kuti akwatire. Koma poti padziko panalibe akazi ena, Adam anaganiza kuti Qaabil akwatire mlongo wa Haabil ndipo Haabil akwatire mlongo wa Qaabil.

Mlongo wa Qaabil anali okongola kusiyana ndi mlongo wa Haabil, choncho Qaabil sanasangalale ndi ndondomeko ija ndipo anafuna kukwatira mlongo wake. Panabuka mkangano,  motiAdam anaganiza zothetsa mkangano uja popereka Nsembe kwa Allah Subhaanah wa Ta’la. Anaganiza kuti yemwe nsembe yake ingalandiridwe akwatira mlongowa Qaabil. Choncho Haabil anasankha nkhosa zabwino kwambiri muziweto zake zija ndikupereka nsembe kwa Allah. Pomwe Qaabil sanasankhe zipatso ndi masamba zabwino kuti apereke nsembe, iye anasankha zoipa zokhazokha.

Allah subhaanah wa Ta’la analandira nsembe ya Haabil ndipo anakana nsembe ya Qaabil. Pamene nsembe zinkaperekedwa Adam analipo, ndipo zotsatira zinapezeka kuti Haabil akwatira mlongo wa Qaabil.Koma Qaabil sanasangalatsidwe nazo ndipo anakwiya moti anaganiza zomupha Haabil.

Tsiku lina Haabil anachedwa kubwelera kunyumba, ndipo Adam anatumiza Qaabil kuti akamufufuze.Qaabil anapita kumunda kukamufufuza Haabil ndipo anakumana naye akubwelera kunyumba. Koma Qaabil anali atakwiya ndi Haabil, anati: “Nchifukwa chani nsembe yako inalandiridwa koma yanga sinalandiridwe!” Haabil anayankha nati: “Ndithudi, Allah amalandira nsembe ya amene akuopa Iye”. Qaabil anakwiya atamva izi ndipo anatenga mwala kuti ammenye Haabil. Ngakhale Haabil anali wamkulu ndi wamphamvu kuposa Qaabil, anamuuza kuti: “Ngati utambasula dzanja lako paine kuti undiphe, ine sinditambasula dzanja langa paiwe kuti ndikuphe. Ndithudi, ine ndikuopa Allah, Mbuye wazolengedwa.” Mau awa anaonjezera mkwiyo wa Qaabil ndipo anamupha ndi mwala uja.

Tsopano pamene Qabil anazindikira kuti Haabil wafa, anadzadzidwa ndi mantha ndipo anasowa chochita.Sanafune kuti bambo ake adziwe zomwe wachita zija. Anayamba kuganiza njira zobitsira tchimo lake lija.

Qaabil anayendayenda ndi thupi la Haabil kuyesera kulibisa, ndipo kenako anaona akhwangwala awiri akumenyana mpaka mmodzi anapha nzake.Wakupha uja anayamba kukumba dzenje padothi ndikukwilira nzake uja, kenako anakwilira.

Izi zinampatsa nzeru Qaabil, kotero kuti anakumba dzenje ndikumukwilira m’bale wake uja. Uku kunali kukwilira (mmanda) koyamba mumbiri ya munthu.

Qaabil anali ndi manyazi pa zomwe anachita, satana anamugonjetsa ndipo anadziwa kuti basi sangabwelerenso kwawo.

Adam anadziwa zomwe zachitika ndipo analilira ana ake; anataya ana ake onse pamene mmodzi anamwalira ndipo winayo anasocheretsedwa ndi satana.

Kenako anawachenjeza ana ake otsala za satana ndipo anawalangiza kuti adzitsatira malamulo a Allah Subhaanah wa Ta’ala nthawi zonse.

Patadutsa nthawi yaitali, Adam anali ndi ana ochuluka ndipo anakalamba, koma ana ake anali kumukonda kwambiri.

Pamene Adam alaih salaam anadziwa kuti imfa yake yawandikira, anamusankha Sheth kuti akhale mlowammalo oyang’anira banja lake.

Pamene nthawi yakumwalira inakwana, Angelo anabwera ndikuima pambali pake. Pamene Adam anazindikira kuti Mngelo wa Imfa wafika, anamwetulira ndikumwalira.