Mbiri ya Abu Bakr Al Siddiq mwachidule

Alongosolereni ana anu achichepere nkhani zimenezi

Abu Bakr anabadwira ku Makkah kuchokera mu fuko chi Quraysh, la Banu Taimi.

Dzina lake lenileni linali Abdul Ka’ba (Kapolo wa Ka’ba) ndipo dzina loti Abu Bakr analipeza chifukwa chakuweta ngamira. Kenako Mtumik salla Allah alaih wasallam anamusintha dzina ndikumutcha Abdullah (Kapolo wa Allah), ndipo anampatsa title ya Assidiq, kutanthauza kuti anali wokamba zoona.

Abu Bakr anali munthu wolemera, ndipo asanalowe Chislamu anali mmodzi mwa anthu olemekezeka ku Makkah. Iye anali wamkulu kuposa Mtumiki ndi zaka zitatu ndipo awiriwa anali kuchezera limodzi kuyambira ku umwana wawo mpaka kumwalira kwa Mtumiki. Pamene Mtumiki anaitanira akubanja kwa ke Chisilamu, Abu Bakar anali mmodzi mwa oyambilira kuchilandira ndipo iye anamuitanira Uthman ndi Bilal pamodzi ndi anthu ena ambiri.

Kumayambiliro kwenikweni kwa Utumiki, Asilamu ambiri anali kuvutitsidwa ndi ma Quraish ndipo Abu Bakr anapereka theka la chuma chake . Pamene Allah anamulangiza Mtumiki salla Allah alaih wasallam kuti asamukire ku Madina, anamusankha Abu Bakr kuti ayende naye pa ulendowu.

Abu Bakr nthawi zonse anali ndi Mtumiki pa nkhondo zolimbana ndi adani a Chislmau. Tsiku lina anapititsa chuma chake chonse kwa Mtumiki kuti chiperekedwe poteteza Madina. Mtumiki salla Allah alaih wasallam atamufunsa kuti wasiya chani kunyumba kwake, anayankha modzichepetsa kuti wasiya Allah ndi Mtumiki wake.

Ngakhale mmene anali kunja kwa Chislamu, Abu Bakr anali kudziwika ndi chikhalidwe cholungama; iye anali kuthandiza osawuka . Anali kukhala moyo wa simple ngakhale anali olemera, anali kupereka chuma chake kwa osawuka, kumasala akapolo, komanso kuthandiza kupititsa Chisilamu patsogolo. Iye anali kupemphera usiku, ndipo banja lake linali losangala nthawi zonse.

Pamen Mtumiki salla Allah alaih wasallam ankamwalira, Abu Bakr radhia Allah anhu kunalibe, ndipo pamene anamva za imfa yake, anapita kunyumba yachisoni ndipo anadandaula, kenako anapsopsona tsaya lake ndikutsanzikana naye.

Pamene anatuluka mnyumba yachisoni muja ndikulengeza za imfa ya Mtumiki, anthu sanakhuluilire ndipo anadandaula kwambiri. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali mtsogoleri komanso kwa iye ndi komwe uthenga wochokera kwa Allah unali kutsikira, iye ndamene anawatulutsa anthu mu kupembedza mafano, amwalira bwanji munthu oteroyo? Awa anali madandaulo a anthu.

Ngakhale Umar, yemwe anali mmodzi mwa anthu olimba mitima komanso amphamvu mwa ma Swahaba a Mtumiki, sanakhulupilire zimenezi ndip anatulutsa lupanga lake ndikulengeza kuti yemwe anganene kuti Muhammad wamwalira amupha. Koma Abu Bakr anamusuntha modekha, ndikupita kutsogholo kwa  anthu ndikulengeza kuti: “E inu anthu, yemwe anali kupembedza Muhammad, ndithu Muhammad wamwalira. Koma yemwe anali kupembedza  Allah, ndithu Allah ndi wamoyo sadzamwalira.” Kenako anamalizira ndi verse ya mu Qur’an:

وََمَا مُحَمَّدٌ إِلاَّ رَسُولٌ قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِهِ الرُّسُلُ أَفَإِن مَّاتَ أَوْ قُتِلَ انقَلَبْتُمْ عَلَى أَعْقَابِكُمْ

“Muhammad sali  chinthu china koma Mtumiki chabe, patsogolo pake adamuka atumiki ambiri. Kodi ngati atamwalira kapena kuphera, mungabwelerenso mbuyo” 3:144

Pambuyo pakumva mawuwa, anthu anadekha ndipo anapeza chilimbikitso.

Nyengo iyi inadutsa, koma tsopano Asilamu anali pa vuto lalikulu la masankhidwe a mtsogoleri wawo. Pambuyo pa kukambirana pakati pa ma Swahaba, anaona kuti palibe yemwe anali oyenera kutenga utsogoleri panthawiyo kuposa Abu Bakr.

Pamene kumwalira kwa Mtumiki salla Allah alaih wasalaam kunamveka, mafuko ena anakana kupereka Zakaat chifukwa choti Mtumiki anamwalira, iwo anali kunena kuti Zakaat inali nthawi ya Mtumiki basi. Ndipo ena mwa iwo anayamba kudzitchula kuti ndi Atumiki. Kuwonjezera pamenepa, ma ufumu a ku Rome ndi Iran anaopsezanso  utsogoleri wa Chisilamu watsopano uja.

Ma swahaba ambiri kuphatikizapo Umar radhia Allah anhu anamupempha Abu Bakr kuti aimitse lamulo la zakaat kwa kanthawi, koma iye anakanisitsa kutero powakumbutsa kuti Lamulo la Allah silingagawidwe; palibe kusiyana kulikonse pakati pa  Zakaat ndi Swalaat, ndipo kusokoneza kulikonse kwa malamulo a Allah kudzagwetsa Chisilamu. Umar pamodzi ndi ena anazindikira za kulakwitsa kwawo.

Posakhalitsa, magulu otsutsa aja anawukira mzinda wa Madina. Abu Bakr anatsogolera gulu lake polimbana nawo, ndipo pamene anagonja, ambiri analowa Chisilamu.

Chiopsezo chochokera ku Rome chinalipo ngakhale nthawi ya Mtumiki salla Allah alaih wasala, ndipo Mtumiki anakhonza gulu la nkhondo motsogozedwa ndi Usama, yemwe anali mwana wa kapolo yemwe anamasulidwa. Koma asilikali aja sanapite chifukwa cha kudwala kwa Mtumiki. Tsopano pambuyo pa kumwalira kwa Mtumiki, anaganiza kuti kodi atumizebe asilikali aja, kapena angokhala adziteteza Madina? Abu Bakr analamula kuti awatumize monga mmene Mtumiki analamulira.

Malamulo omwe anaperekedwa kwa Usama amagwirabe ntchito mpaka lero. Malamulo ake ndi awa:

Musasemphane ndi mtsogoleri wanu

Musaphe nkhalamba

Musaphe mzimai kapena mwana

Musaononge mtengo wa chipatso chirichonse

Musaphe nkhosa, ngamira kapena ng’ombe, kupatula ngati mwafuna kudya

Mukakumana ndi anthu omwe amakhala akupembedza mmatchalitchi mwawo, muwasiye musawapange chirichonse.

Nthawi zambiri, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kusankha Khalid bun Walid pa utsogoleri wa Asilakali chifukwa anali wamphamvu komanso wodziwa utsogoleri wa nkhondo. Gulul lake la nkhondo linapita patsogolo mu utsogoleri wa Abu Bakr, ndipo linali kupambana pa nkhondo zonse.

Muntchito zina zotamandika za Abu Bakr, inali kusonkhanitsa kwa Qur’an Yolemekezeka. Iye anamwalira pa 21 Jumaadal Ukhra 13H (634CE) pamene anali ndi zaka 63 ndipo anaikidwa pambali pa Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Anatsogolera Asilamu pafupifupi myezi 27. Panyengo ya utsogoleri wake, Abu Bakr anayesetsa kulimbikitsa anthu ake komanso kuteteza Asilamu ku ziposezo zomwe zinalipo.