Ngati makolo athu kapena abale athu ali ma kafir, tisawachite kukhala atetezi athu
E inu amene mwakhulupirira! Musawachite makolo anu ndi abale anu kukhala atetezi anu ngati (iwo) akukonda kusakhulupirira Mulungu m’malo mokhulupirira (kukhala Asilamu). Ndipo mwa inu amene ati awasankhe kukhala atetezi, otero ndiwo adzichitira okha zoipa.
Nena: “Ngati makolo anu, ana anu,  abale anu, akazi anu, ndi anansi anu ndi chuma chimene mwachipata, ndi malonda anu amene mukuopa kuti angaonongeke, ndi nyumba zanu zimene mukuzikonda, (ngati zinthuzi zili) zokondeka kwambiri kwa inu kuposa Mulungu ndi Mtumiki wake ndi kuchita Jihad pa njira yake, choncho dikirani kufikira Mulungu adzabwera ndi lamulo lake (Lokukhaulitsani). Ndipo Mulungu satsogolera anthu otuluka m’chilamulo (chake).
Chongomva mauwa, ena anafunsa kuti:
“Apatu ndimvetsetse apa akuti makolo athu ngati Ali makafiri tisawachite kukhala abale athu kutathauza kuti ubale uthe kapena kuti chani?”
Enanso anafinsa nati:
“Kodi Allah samaziwa kuti banja limeneri muzatuluka munthu okhulupilira? Kodi Allah adakafuna kuti tonse tikhale aslam sitidakakhala? Chonde tiuzeni momveka ndimene surahyi ikufotokozera”
Mafunso amenewo ofunika kuchenjera nawo…ali mbali mwa dzenje la kufr
Ndisanalongosole matanthauzo a ma Aayah omwe ndabweretsa aja, ndikufuna ndiyankhe kaye mafunso awiri awa, mafunso oopsa mu Tauhid, komanso ndi ololedwa kufunsa okhawo amene akufuna kudziwa tanthauzo la Aayahyo kuti agwiritse ntchito moyenera. Koma ena saloledwa kufunsa kapena kufunsidwa chifukwa mapeto a nkhani kumakhala kubweretsa zikaiko zamchikhulupiliro mu deen:
Ndiyambe ndi gawo loyamba la funso lachiwiri:
Kodi Allah samaziwa kuti banja limeneri muzatuluka munthu okhulupilira?”
Allah ndiye Mwini kudziwa komanso kudziwa kwake kulibe chiyambi ndinso malire; Amadziwa zomwe sidzinachitike, amadziwa kuti zidzachitika bwanji, zidzamchitikira ndani, komanso zidzachitika nthawi yanji, chifukwa chani, zidzatha bwanji … pamenepo nkuti mwini wake munthu asanabadwe.
Choncho kwa Alla sikopita funso loti: “kodi Mulunguyo samadziwa?”
Allah amadziwa zonse ndipo palibe yemwe ali kuseli kwa Iye amene ali odziwa zina zomwe Iye sadziwa (palibe chomwe sadziwa). Allah amadziwa kuti banja lirilonse mudzatuluka anthu otere otere. Koma choti tidziwe nchoti Allah anatipanga tonsefe kukhala a Chipembedzo chimodzi (Chisilamu), koma tokha timadzisankhira zomwe Iye sanatipatse. Allah amadziwa kuti munthu akadzatuluka umu ali ndi njira ziwiri zomwe adzatsatire (ya shytwan kapena ya Allah) choncho ngati angadzatsatire ya ine, akalowa ku Jannah, ngati angatsatire ya Shytwaan, akalowa ku Moto.
Mofanana ndi funsoli, anthu ena amatha kufunsa kuti nchifukwa chani analenga nkhumba nkutiletsa kudya, nchifukwa chani Isa (Yesu) alaih salam akadzabwera adzapha nkhumba zonse, nchifukwa chani Allah analenga zinthu zosafunikira padziko…?
Mafunso ngati awa ndi osafunikira chifukwa Iye akunena mu Surah Al Kahf 51 kuti
مَا أَشْهَدتُّهُمْ خَلْقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَلَا خَلْقَ أَنفُسِهِمْ وَمَا كُنتُ مُتَّخِذَ الْمُضِلِّينَ عَضُداً
Sindidawachite (iwo) kukhala mboni mu kulenga kwa thambo ndi nthaka, ngakhale kuwalenga kwawo, ndipo sindidawalole osokeretsa kukhala athandizi (anga).
Apa amakamba nkhani ya ma Shytwan komanso anthu omwe akutsatira ma shytwan. Ndipo tikuphunzirapo munkhani yathuyi kuti Iye Allah polenga chilichonse ankadziwa cholinga chake, sikuti chithandize munthu yekha ayi koma chilichonse chili ndi ntchito yake kwa Allah padziko pano.
 وَهَدَيْناهُ النَّجْدَيْنِ
Ndipo tamlongosolera njira ziwiri: (yabwino ndi yoipa, ndipo tampatsa mphamvu yosankhira njira imene akufuna). Surah Al Balad 10
إِنَّا هَدَيْنَاهُ السَّبِيلَ إِمَّا شَاكِراً وَإِمَّا كَفُوراً
Ife tidamlongosolera njira yoongoka: kukhala wokhulupirira kapena wotsutsa (zonse zili kwa iye).
Surah Al Insaan (Al Dahr) 3
Ndimalize gawo lachiwiri la funso lachiwiri lija: “Kodi Allah adakafuna kuti tonse tikhale aslam sitidakakhala?”
Allah anafuna kuti tonsefe tikhale Asilamu ndipo kuti tonse tikalowe ku jannah. Koma anatipatsa ufulu kuposa cholengedwa chilichonse, ufulu wosankha pakati pa zinthu ziwiri: mbali imeneyi anatilemekeza kuposa Angelo, chifukwa iwo sanawapatse kusankha pakati pa chabwino ndi choipa…
Funsoli anayankha kale Mwini Wake, mu Surah Al Maaidah 48:
وَلَوْ شَاء اللّهُ لَجَعَلَكُمْ أُمَّةً وَاحِدَةً وَلَـكِن لِّيَبْلُوَكُمْ فِي مَا آتَاكُم فَاسْتَبِقُوا الخَيْرَاتِ
Mulungu akadafuna, akadakuikani kukhala Mpingo umodzi (wotsata chilamulo chofanana). Koma akufuna kukuyesani pazomwe wakupatsani. Choncho pikisanani pazinthu zabwino.
Apa tikutha kuona kuti cholinga chotibweretsera mipingo ina ndikufuna kutiyesa imaan yathu (koma sikuti mipingo imeneyo ili kanthu kwa Mulungu…ndi mayesero chabe apadziko pano). Ndiye kumapetoko akutiuza zoyenera kutsatira, akuti tipikisane pochita/kutsatira zinthu zabwino, zomwe zikupezeka mu njira yabwino yolungama ya Chisilamu
Akunenanso mu Surah Al Nahl 93:
وَلَوْ شَاء اللّهُ لَجَعَلَكُمْ أُمَّةً وَاحِدَةً وَلكِن يُضِلُّ مَن يَشَاءُ وَيَهْدِي مَن يَشَاءُ وَلَتُسْأَلُنَّ عَمَّا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ
Ndipo Mulungu akadafuna, ndithu, akadakuchitani kukhala gulu limodzi, (nonsenu mukadamumvera monga momwe adawachitira Angelo, koma adakupatsani ufulu kuti muchite chimene mufuna); komatu amamulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo amamuongola wamfuna; ndipo, ndithu mudzafunsidwa pa zomwe munkachita.
Apa palinso phunziro loti akadafuna akadatipanga kukhala ngati Angelo, omwe anangowalamula kuti akhale ochita zabwino, osanyozera malamulo ake komanso onse akhale Asilamu (odzipereka ndi kugonjera malamulo ake), koma ife anatipatsa ufulu, nkutisonyeza njira yabwino ndi yoipa kuti tidzisankhire tokha.
Allah Ta’la akunena mu Surah Al Imraan 19:
 إِنَّ الدِّينَ عِندَ اللّهِ الإِسْلاَمُ
Ndithudi, chipembedzo (choona) kwa Mulungu ndi Chisilamu.
Komanso pa 85 mSurah yomweyi, akunena kuti:
وَمَن يَبْتَغِ غَيْرَ الإِسْلاَمِ دِيناً فَلَن يُقْبَلَ مِنْهُ وَهُوَ فِي الآخِرَةِ مِنَ الْخَاسِرِينَ
Ndipo amene angatsate Chipembedzo chosakhala Chisilamu, sichidzalandiridwa kwa iye. Ndipo iye tsiku Lomaliza adzakhala mmodzi mwa (anthu) otaika.
Atumiki onse omwe anatumizidwa ndi Allah ankaitanira ku Chipembedzo cha Chisilamu. Izi mudzipeza mu Qur’an yomweyi, palibe Mtumiki kapena Mneneri amene anali wachipembedzo cha Chikristu kapena Chipembedzo cha Chiyuda, chifukwa Allah sanapereke zipembedzo zimenezi, koma anapereka Chisilamu basi, ndipo anapereka mabuku anayi (Zabur (Daud), Taurah/Torah (Musa), Injeel/Gospel/Bible (Isa), Qur’an (Muhammad)) koma mabuku onsewa, Atumiki onsewa, anali Achisilamu, kudzatumikira Chisilamu.
komanso anatilenga mchilengedwe chimodzi (fitrah), cha Chipembedzo cha Chisilamu, akunena mu Surah Al Rum 30 kuti:
فَأَقِمْ وَجْهَكَ لِلدِّينِ حَنِيفاً فِطْرَةَ اللَّهِ الَّتِي فَطَرَ النَّاسَ عَلَيْهَا لَا تَبْدِيلَ لِخَلْقِ اللَّهِ ذَلِكَ الدِّينُ الْقَيِّمُ وَلَكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ
Lunjika nkhope yako kuchipembedzo moyenera; (pewa kusokera kwa okana Mulungu. Dzikakamize ku) chilengedwe chimene Mulungu adalengera anthu; (Ichi nchipembedzo cha Chisilamu chomwe nchoyenerana ndi chilengedwe cha munthu). Palibe kusintha m’chilengedwe cha zolengedwa za Mulungu. Ichi ndi chipembedzo choona cCholungama). Koma anthu ambiri sadziwa.
ONSE OMWE SALI MCHIPEMBEDZO CHA CHISILAMU NDI AKUMOTO … palibe kukaikira kapena kutsutsana. Chifukwa Allah anatipangira njira kuti tisankhe, koma iwo anasankha njira yoipa. ya kumoto.
Apa ndimangoyankha kaye mafunso awiri aja, nthawi  ndilowa mma aayah aja kuti tiwamvesetse in sha Allah
Kuchokera mma aayah awa: Surah Al tawbah 23-24
NGATI MAKOLO ATHU KAPENA ABALE ATHU ALI MA KAFIRI, TISAWACHITE KUKHALA ABALE ATHU (MCHIPEMBEDZO)
E inu amene mwakhulupirira! Musawachite makolo anu ndi abale anu kukhala atetezi anu ngati (iwo) akukonda kusakhulupirira Mulungu m’malo mokhulupirira (kukhala Asilamu). Ndipo mwa inu amene ati awasankhe kukhala atetezi, otero ndiwo adzichitira okha zoipa.
24. Nena: “Ngati makolo anu, ana anu,  abale anu, akazi anu, ndi anansi anu ndi chuma chimene mwachipata, ndi malonda anu amene mukuopa kuti angaonongeke, ndi nyumba zanu zimene mukuzikonda, (ngati zinthuzi zili) zokondeka kwambiri kwa inu kuposa Mulungu ndi Mtumiki wake ndi kuchita Jihad pa njira yake, choncho dikirani kufikira Mulungu adzabwera ndi lamulo lake (Lokukhaulitsani). Ndipo Mulungu satsogolera anthu otuluka m’chilamulo (chake).”
Tidziwe kuti iyi ndi Qur’an, mau a Allah Ta’la, samalakwitsa komanso mkati mwake mulibe zokaikitsa, koma ife ndamene sitimaimva.
Nchifukwa chake ngakhale Mtumiki ankati akalandira ma aayah kuchokera kwa Jibril, amakhala naye nkumamuphunzitsa. Tsopano ngati amaphunzira Mtumiki mwini Chibvumbulutso, kusonyeza kuti sakanatha kungolandira mau omangidwa, zikanavuta kuwalongosolera anthu. Kodi nanga ife poti tikungokhala osaiphunzira Qur’an, tingadziwe bwanji zomwe aayah ikutanthauza?
Timvesetse bwinobwino;
Mukaonesetsa mutu wa nkhaniwo panalembedwa ma ubale awiri:
“NGATI MAKOLO ATHU KAPENA ABALE ATHU ALI MAKAFIR …TISAWACHITE KUKHALA ABALE ATHU”
Funso nkumati, kodi zitheka bwanji anthu oti ndi abale athu kale, asakhalenso abale athu?
Yankho, apa ma ubale awiriwo ngosiyana. Ubale woyambawo ndi wa chibadwidwe, ndipo wachiwiriwo ndi wa kuchitira zinthu limodzi, kukhala atetezi athu pa zinthu zina komanso kuthandizana pa zinthu zina za pa umoyo…
Potanthauzira mu Qur’an anena kuti atetezi ndipo mu Arabic anena kuti Awliyaa, choncho ine ndagwiritsa liwu loti abale chifukwa atetezi ndi abale, mchiyankhulo chathu.
Ubale ulipo wamitundu ingapo koma ndikamba mitundu iwiri yokha yomwe ikukhunza nkhaniyi:
Ubale wa umunthu (wachibadwidwe):
Poti tonsefe ndife ana a Adam, choncho ngakhale mkhristu tikuyenera kumuchitira zabwino chifukwa ndi m’bale wathu kuchokera kwa bambo ndi mai Adam+Hawaa. Qur’an yatsindika izi potiitanira liwu limodzi Allah akamafuna kutiyankhula tonsefe padziko:
يا أيها الناس اعبدوا ربكم الذي خلقكم والذين من قبلكم لعلكم تتقون
E inu anthu! pembedzani Mbuye wanu yemwe adakulengani inu ndi omwe adalipo kale, kuti mudzichinjirize (ku chilango cha Mulungu). Surah Al Baqarah (2:21)
Akunenanso malo ena:
يا أيها الناس اتقوا ربكم الذي خلقكم من نفس واحدة وخلق منها زوجها وبث منهما رجالا كثيرا ونساء واتقوا الله الذي تساءلون به والأرحام
E inu anthu! Opani Mbuye wanu yemwe adakulengani kuchokera mwa munthu mmodzi (Adam) ndipo adalenga mmenemo mkazi wake (Hawa), ndipo adafalitsa amuna ndi akazi ambiri kuchokera mwa awiriwo. Ndipo opani Mulungu yemwe kupyolera mwa Iye mumapemphana. Ndipo (sungani) chibale. Ndithudi Mulungu ndimyang’aniri pa inu (akuona chilichonse chimene muchita). Surah Al Nisaai 1
Akutilamula kuti tisunge maubale
Ma Aayah awa akutsimikiza kuti anthufe tili pa ubale ndithu wachibadwidwe, posatengera kusiyana kwa zipembedzo. Mu Hadith ina Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati Mngelo Jibril anali kumulangidza za neighour wake (oyandikana naye malo okhala) kumulangiza za kumuchitira zabwino kotero kuti Mtumiki anaganiza kuti neibhour ameneyu akhonza kukhala ngati m’bale wake. Koma sanali m’bale wake. Komanso  Mtumiki analamula kukhala bwino ndi oyandikana nawo ngakhale atakha kafir. Izi palibe kusutsa kulikonse.
Chibale chachibadwidwechi chimakhala chikubwelerabwelera pakati pathu kudzera mma banja, mmitundu komanso mmafuko. Chibale chaching’ono kwambiri chikuyambira pa mwana ndi makolo ake, achimwene, chemwali…kumapita uko… Chibale chimenechi sitikuyenera kuchiononga chifukwa Allah akunena kumapeto kwa aya yachiwiri mmwambwamo kuti:
…Ndipo (sungani) chibale…
Kudula ubale ndi ntchimo lalikulu ndipo Allah akalowetsa kumoto munthu odula ubale (ngakhale m’baleyo atakhala kuti si Msilamu) apa tikukamba gawo la ubale wachibadwidwe
Kodi nanga ubale omwe ukuletsedwa kuti tisachitewu ndi uti?
Tisathetse ubale wa biological relationship chifukwa choti m’bale wathu watuluka deen…ubale ukhalepo ndipo tiugwiritse ntchito pomuthandiza kubwelera ku Chsilamu m’bale wathuyo, chifukwa Allah akunena kuti
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا قُوا أَنفُسَكُمْ وَأَهْلِيكُمْ نَاراً وَقُودُهَا النَّاسُ وَالْحِجَارَةُ
E Inu amene mwakhulupilira, atetezeni abale anu ku moto womwe nkhuni zake zikakhala anthu ndi myala… Surah Al Tahrim (66:6)
Ubale wa Mchipembedzo:
Ichi ndi chibale chomwe Mkristu amakhala m’bale wake Mkristu, Myuda kukhala m’bale wake Myuda, Msilamu kukhala m’bale wake Msilamu.
Izi zimachitika chifukwa cha kukhala ndi chikhulupiliro chofanana pa Mulungu. Mwachitsanzo, Mkristu m’bale wake ndi Mkristu chifukwa onse amakhulupilira kuti Yesu ndi mwana wa Allah. Myuda m’bale wake ndi Myuda chifukwa onse amakhulupilira kuti Uzair ndi mwana wa Allah. Msilamu m’bale wake ndi Msilamu chifukwa onse amakhulupilira kuti Allah ndi Mmodzi yekha alibe mwana komanso alibe ofanana naye.
Choncho Ayuda ndi Akristu ali ndi zikhulupiliro zambiri zofana kwambiri ndipo amakhala akuthandizana ngati abale muzambiri mu zikhulupiliro za mChipembedzo zawo.
الكفر ملة واحدة
Onse okanira zawo nzimodzi
Pomwe Asilam ali paokha sagawana zikhulupiliro ndi awiriwa.
Choncho Asilamu sali pa ubale wa mChipembedzo ndi Akristu kapena Ayuda chifukwa zikhulupiliro zawo nzosiyana, ndipo sangathandizane kapena kukhala atetezi wina ndi mzake pakati pawo (pa chipembedzo)
Zili mmalemba zimenezi? Inde, mmalemba ake awa:
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُواْ لاَ تَتَّخِذُواْ الْيَهُودَ وَالنَّصَارَى أَوْلِيَاء بَعْضُهُمْ أَوْلِيَاء بَعْضٍ وَمَن يَتَوَلَّهُم مِّنكُمْ فَإِنَّهُ مِنْهُمْ إِنَّ اللّهَ لاَ يَهْدِي الْقَوْمَ الظَّالِمِينَ المائدة
E inu amene mwakhulupirira! Ayuda ndi akhrisitu musawapale ubwenzi (nkumawauza chinsinsi chanu). Iwo pakati pawo ndi abwenzi ndi atetezi kwa wina ndi mnzake. Amene awapale ubwenzi mwa inu, ndiye kuti iye ndi m’modzi wa iwo. Ndithudi, Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa. Al Maaidah 51
Malemba enanso awa: Al Imraan 28
لا يَتَّخِذِ الْمُؤْمِنُونَ الْكَافِرِينَ أَوْلِيَاء مِن دُوْنِ الْمُؤْمِنِينَ وَمَن يَفْعَلْ ذَلِكَ فَلَيْسَ مِنَ اللّهِ فِي شَيْءٍ
Asilamu okhulupilira asapale ubwenzi osakhulupilira kusiya Asilamu anzawo. Amene achite zimenezo, sadzakhala ndi chilichonse pachipembedzo cha Mulungu..
Tikaonjezeranso pamenepa Surah Al Tawbah ija Aayah 23-24, komanso ma aayah ena ambiri, tipeza chimodzimodzi akutanthauza kuti tisawatenge abale athu omwe akonda kupanga kufr (omwe akonda kukhala okanira Allah ndi Mtumiki wake) kukhala atetezi athu (abale athu pa Chipembedzo – othandizana nawo mu deen) … ngakhale atakhala m’bale wathu.
Ndimalize nkhaniyi ndi chitsanzo kuchokera mbuyomu nthawi ya Mtumiki Nuhu (Noah) alayh Ssalaam, yemwe anali ndi mwana dzina lake Saam (Shem) ndipo mwanayu anali kafir.
Pamene chigumula chosetsa okanira onse chinadza, iye anakana kukwera nawo mchombo cha bambo ake ndipo anatchalenja ndikukanira kwakeko kuti “ndikwera pa phiri linditeteza ku madziwo!” zimenezo kuwauza bambo ake omwe anali Mtumikinso.
 Nuh anapempha Allah kuti:
رَبِّ إِنَّ ابْنِي مِنْ أَهْلِي وَإِنَّ وَعْدَكَ الْحَقُّ وَأَنْتَ أَحْكَمُ الْحَاكِمِينَ
E Mbuye wanga! Ndithu, mwana wanga ali mgulu la (abale) akubanja langa (akuonongedwa). Ndipo ndithu, lonjezo lanu ndiloona, ndipo inu ndinu Woweruza mwachoonadi kuposa aweruzi onse.”
Ankafuna kuti Allah ampulumutse chifukwa choti iye ndi mwana wake – m’bale wake. Koma taonani zomwe Allah anamuyankha Mtumiki,…
يَا نُوحُ إِنَّهُ لَيْسَ مِنْ أَهْلِكَ إِنَّهُ عَمَلٌ غَيْرُ صَالِحٍ
E iwe Nuh! Ndithu, iyeyo simwana wa m’banja lako. Iye zochita zake sizili zabwino. Surah Hud, Aayah 45-46
Tikaonesetsa, apa Allah amadziwa kuti Sam ndi mwana wa Nuh, koma kumbali ya zintchito zake sanali mwana wake!
Pofika pamenepo, ndikhulupilira kuti tadziwa ndi ubale wanji umene ma aayahwo akutanthauza.
Zolakwika sizimalephera tikamalongosola nkhani zimenezi, choncho tikaona mistake kapena kupindika kwa malongosoledwe, tisangoyang’ana nkusiira pompo, tilembereni pansipo ngati comment, kapena titumizireni kuzera mu page ya contact us, mmwambamo. Chifukwa munthu sungaphunzire popanda kulakwitsa, mukatikhonza ndiye kuti tionjezeranso ilm pamenepo.
Allah adzitidalitsa komanso kutionjezera kuzindikira munjira zosiyanasiyana
Wassalam alaikum Warahmatullah wabarakaatuh