Ambiri mwa ife timakhala tikufunafuna barakah (madalitso) kuchikera mu nambala ya 786 poilemba pamayambiliro pa ma kalata, nkhani, pa grocery komanso malo ambiri.

Ena mwaife timailemba nambalayi pa china chane ndikuchikoleka pa galimoto kuti itetezedwe ku ngozi.
Ena mwaife tikamagula sim card timayesetsa ndithu kuti numberyo ipezeke po 786. Ena number plate ya galimoto…poganiza kuti ndi za Chisilamu ndipo potero tipeza madalitso.
Koma kodi number imeneyi imatanthauza chani kwenikweni? Kodi ili ndi kufunikira kulikonse mChisilamu?
Omwe anayambitsa zogwiritsira number imeneyi, amanena kuti chilembo chirichonse cha mzilembo za Arabic (أ – ب -ت -ث -ج…) chimaimira ma number ndipo mukawaphatikiza ma number amene amapanga Basmalah, mupeza kuti alipo 786 (seven hundred eighty six). Choncho, malinga ndi iwo, 786 imaimira “Bismillah-ir Rahmaan-ir Raheem”.
Koma kodi ndi chonchodi? Number ingaimire mmalo mwa mau aakulu ngati amenewa Bismillahi Rrahmaan Rraheem? Mu Shariah zili pati zimenezi?
Nanga Mtumiki salla Allah alaih wasallam kapena ma Sahaba anagwiritsa ntchito 786 mmalo mwa Bismillahi Rrahmaan Rraheem?
Ambiri amangotsatira koma samafufuza kuti zinayamba bwanji. Amangogwiritsa ntchito poti anawapeza makolo akugwiritsa ntchito. Koma kutero mChisilamu ndi koopsa kwambiri
Tikabwelera mu Shariah yomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam anabweretsa, tipeza kuti number ya 786 ilibe kufunika kulikonse kwapadera kosiyana ndi ma number ena. 786 ndi seven hundred eighty six basi. Palibenso china chake choonjezera pamenepo.
Tsoka ndilo, chi bid’ah cholemba 786 mmalo mwa Bismillahi Rrahmaan Rraheem pamwamba pa pepala kapena malo ena aliwonse pofuna kupeza baraka, chakwanira pakati pa Asilamu, makamaka anzathu aku India, ndipo Asilamu anzathu osazindikira amasocheretsedwa ndi chikhulupiliro chabodzachi poganiza kuti ndi zoonadi.
Imeneyitu ndi “game of numbers” kusewera ndi ma number, kusewera ndi mathematics komwe kunkachitika pakati pa anthu akalekale munthawi ija amaitcha kuti ancient civilization. Shariah itabwera inathetsa zikhulupiliro monga superstition, kukhulupilira zodabwitsa zochokera mmatsenga, zochokera mu kusewera ndi ma number (numerological mumbo-jumbo).
Komatu ngakhale zili choncho, ambiti adakali mu ukapolo wa game imeneyi, ndipo amaganiza kuti 786 ndi Bismillah Rrahmaan Rraheem ndipo muli barakah. Kutaya nthawi mmalo mokhulupilira zenizeni. Nchifukwachaketu tikumakonda kulalikira zokhunza Aqeeda komanso maphunziro, kuti mwina tisukusuleko mdima umene tili nawowu.
Mukamawafunsa ozindikira za zimeneziwo, amayankha izi:
Makani awo oyamba ndi otere:
Imeneyi ndi system ya ma number yotchedwa ABJAD; chilembo chirichonse chimaimira number
Yankho la mau amenewo ndi ili:
Qur’an Yolemekezeka si buku la mathematics kapena buku la kutanthauzira zilembo mma number. Kodi tikachotsa Bismillah Rrahmaan Rraheem pamwamba pa surah iriyonse nkuikapo 786, mukuganiza kuti ma number amenewa angakwaniritse dzina la Allah Subhanahu wa Ta’ala?
Kusagwira kwa ABJAD wawoyo komanso kupanda phindu kwake, kukumveka bwino tikafika pa ma number awa: 66, 92, 352 ndi 296. Ma number amenewanso eni akewo amati akutanthauza Allah (66), Muhammad (92), Qur’an (352), ndi Rasool (296).
Ndiye kuti kuyambira lero popanga dua ndikuitana Allah mmalo monena kuti Yaa Allah, ndidziti Yaa 66!, Allahumma ndidziti 66mma! Mmalo monena kuti Muhammad RasuluLlaah ndidziti 92 296 66 ?? Astaghfirullaah wa a’oodhu billaah!!!!
Kodi Allah anasitsa Qur’an mma number? Nchifukwa chani ife tikusintha mau olemekezekawa komanso maina aakulu kwambiri kuwaika mma number?
Makani awo achiwiri akhonza kunena kuti:
Ife sitimafuna kunyoza kapena kuchita chipongwe Dzina Lolemekezeka la Allah, nchifukwa chake timagwiritsa ntchito ma number kuti ngati pepalalo litagwa pansi, tisakhale kuti tagwetsa dzina la Allah.
Yankho la mau amenewo ndi ili:
Inuyo ndi odziwa kulemekeza Dzina la Allah Ta’la kuposa mmene anali kulemekezera mtumiki salla Allah alaih wasallam? Mtumiki anali kutumiza makalata kwa mafumu ndi atsogoleri a chikafir koma anali kulembamo mawu olemekezeka oti “Bismillah-ir Rahmaan-ir Raheem”. Chimodzimodzi Nabi Sulaiman alaih salaam anatumiza kalata kwa Mfumukazi ya ku Sabai (Queen Sheba) ndipo kalatayo inali ndi mau olemekezekawa Bismilllahi Rrahman Rraheem. Iyetu anali Mtumiki,. ndipo anali kudziwa zomwe zingakhale kulemekeza komanso zomwe zingakhale kunyoza Allah!
Makani awo achitatu akhonza kunena kuti:
Ifetu timangogwiritsa ntchito pofuna baraka komanso chitetezo
Yankho la mau amenewo ndi ili:
Kufunafuna baraka kapena chitetezo kudzera munjira iriyonse yomwe Chisilamu sichinaloleze ndi SHIRK chifukwa yemwe angafune chitetezo kapena baraka kuchokera ku china chake kapena wina wake posakhala Allah, ndiye kuti wachita shirk,. shirk ndi tchimo loyambilira mmachimo akuluakulu.
Munthu akuyenera kupempha chithandizo, chitetezo komanso baraka kuchokera kwa Allah yekha basi, kapena kuzera munjira zomwe zili zololezedwa mu Sharia. Koma kupachika zimanumber ayi, ngakhlae zimanumberzo zitamatanthauza chani
Makani awo achitatu akhonza kunena kuti:
Tsopano??? Ngati ife tikugwiritsa ntchito manumberwa vuto liri pati? Kulakwika kuli pati?
Yankho la mau amenewo ndi ili:
Kulakwika komwe kulipo pa kugwiritsa ntchito koteroko ndi koti zimenezo siinali njira ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam, komanso sizololedwa kuchita ibaada munjira iliyonse kupatula njira yomwe inalongosoledwa ndi shariah.
Mtumiki salla Allah alaih wsallam anati: Yemwe ayambitsse chinthu chomwe sichili mu deen yathuyi, chidzakanidwa
 
Makani awo achitatu akhonza kunena kuti:
Ifetu timangogwiritsa ntchito ngati chidule cha mauwo basi. Koma timakhala tikutanthauza Bismillah
Yankho la mau amenewo ndi ili:
Mwina kutheka mwaiwala: “Bismillah-ir Rahmaan-ir Raheem” ndi aayah yoyambilira ya mu Surah yoyambilira mu Qur’an, Surah Al Fatihah. Ndipo Allah anaisitsa Qur’an muchiyankhulo chomveka bwino cha Arabic, choncho palibe yemwe angasinthe chilembo nkuchiika mma number munjira iriyonse, ndipo ikakhala aayah yatunthu ndiye ndikwambiri!
Qur’an si chibvumbulutso chochokera kwa munthu choti inu mudzichiseweretsa ngati mpira chonchi.
لا مبدل لكلماته Palibe kusintha mau ake.
Pomaliza:
Aliyense yemwe angagwiritse ntchito 786 ndi cholinga chopeza baraka kuchokera kwa Allah, ndithu ameneyo ndi osochera, ndipo kuyesera kudzibakira zimenezi munjira iriyonse ndi umbuli waukulu, bid’ah yonukha komanso kuteroko nkutsatira mchimbulimbuli.
Amene anabweretsa za 768 komanso ma number ena aja, ndi olakwa pamaso apa Allah ndipo akalangidwa chifukwa chosintha mau a mu Qur’an, omwe ndi mau a Allah Ta’ala.
Msilamu akuyenera kudzitalikitsa ku mchitidwe woipa umenewu ndipo akayiona number imeneyi adziyiona ngati mmene amaonera ma number ena onse, chimodzimodzi ma number ena aja.
Tipemphe Allah atiwongole ndipo tikhale ogwiritsa ntchito zomwe zili zolondola. Maphunziro ndi ofunika